Print Sermon

Cholinga cha tsamba ili ndi kupereka ma ulaliki a ulere olembedwa komanso a mkanema kwa a busa mdziko lonse la pansi makamaka maiko okwera kumene, komwe kuli ma sukulu a Baibulo ochepa kapena kulibiretu.

Maulaliki awa olembedwa komanso a m’ma video akupezeka pafupifupi m’ma kompyuta 1,500,000 m’maiko 221chaka chilichonse pa www.sermonsfortheworld.com. Anthu zikwi-zikwi amaonera kanema wa pa YouTube, koma kenaka amasiya YouTube ndikubwera ku website yathu. You Tube imawalondolera anthu ku website yathu. Maulaliki olembedwawa akupezeka mzilankhulo 46 mu makomputa 120,000 mwezi uli wonse. Maulalikiwa alibe chiletso, kotero alaliki akhoza kuagwiritsa ntchito mosafuna chilolezo. Chonde sindikizani apa kuti mudziwe m’mene mungaperekere thandizo la mwezi ndi mwezi lomwe lingathandize kwakukulu pofalitsa uthenga wa bwino kudziko lonse la pansi.

Mukafuna kulembera Dr. Hymers nthawi zonse muuzeni dziko limene mukukhala, apo ayi sangakuyankheni. E-mail ya Dr.Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net.
A. W. TOZER KUKAMBA ZA CHITSITSIMUTSO

A. W. TOZER ON REVIVAL
(Chichewa)

ndi Dr. R. L. Hymers, Jr.

Phunziro lophunzitsidwa pa Chihema cha Baptist cha ku Los Angels
Kumadzulo kwa tsiku la Ambuye, May 9, 2021
A lesson taught at the Baptist Tabernacle of Los Angeles
Lord’s Day Afternoon, May 9, 2021

Nyimbo chiphunzitso chisanayambe:
“Dzadzani Masomphenya Anga”
   (Woyimba Avis Burgeson Christiansen, 1895-1985).


Chonde tsekulananeni Yoswa 7:12.

“Mwa ichi ana a Israyeli sangathe kuima pamaso pa adani awo, awafulatira adani awo, pakuti aperekedwa aonongeke. Sindidzakhalanso nanu mukapanda kuononga choperekedwacho, kuchichotsa pakati pa inu” (Yoswa 7:12).

Mukhoza kukha. Israeil akhala akugonjetsa anthu a mitundu kuyambira kale mpaka tsopano. Munthu wina anaba zinthu kuchoka kwa anthu amene anawagonjetsawo. Ndipo Mulungu anakhumudwa nao mpingo mchipululu. Munthu winanso wotchedwa Akani anakaniza Mulungu awathandize ngati m’mene anachitira kale. Dr. Scofield ananena bwino motere,

“Kuphwetekedwa kwa Kristu kunadza kaamba ka tchimo, kapena kusowa uzimu kwa wokhulupirira m’modzi.” (ndemanga ya pansi pa tsamba 266 la buku lake)

Tikhoza kumataya nthawi ndi kupempha Mulungu kuti atumize chitsitsimutso pamene tikupitiriza kuphwanya malaulo Ake, mwadaladala kupeputsa zimene Mulungu amafuna. Mulungu anati kwa Yoswa,

“Sindidzakhalanso nanu mukapanda kuononga choperekedwacho” (Yoswa 7:12)

Munthu amene anali ndi mbiri ya chi Katolika akatembenuka kumachimo, amafuna kuti ali lape. Koma kulapa kotero kumakhala koipitsitsa. Tsekulani pa Miyambo 28:13 imirirani ndi kuwerenga mokweza.

“Wobisa machimo ache sadzaona mwai; wakuwabvomereza, nawasiya adzachitiridwa chifundo.” (Miyambo 28:13)

Mukhoza kukhala. Kulapa osasiya zimenene walapazo ndi chimodzi-modzi ndi kusalapa nkomwe!

Tsekulani Yohane 14:21,

“Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda ine adzakondedwa ndi Atate anga.” (Yohane 14:21)

Tsopano tsekulani Yohane 14:15,

“Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga."

Ndondomeko za Dr. Tozer kuti chitsitsimutso chikhaleko.

(1) Musakhutire ndi zochita zanu. Ikani maganizo anu pa za kusintha kwa moyo wanu.

(2) Mudziike pa njira yoti ndinu wodalitsika. Pakufuna chitsitsimutso ndi kusiya kudzipempherera ndikufuna kusiya njira ina ndi kutsata ina.

(3) Malizitsani ntchito ya kulapa. Musathamangire kumaliza.

(4) Pangami fundo zokuthandizani kukhala mchimenecho ngati kungatheke.

(5) Khalani ndi maganizo wokhazikika. Zimitsani Kanema wanu. Muyenera kusintha zochitika zanu apo ayi simuona kusintha kwa moyo wanu wa uzimu.

(6) Chepetsani zimene mumazikonda. Mtima wanu udzatsitsimuka pamene mwautsekera ku za dziko lapansi ndi tchimo ndi kutsekulira kwa Kristu.

(7) Kanani “kuchita dzimbiri.” Muzipezeka-pezeka pafupi ndi a busa anu ndi kumachita chirichonse angakutumeni kuchita. Phunzirani kummvera.

(8) Yambani kuchitira umboni. Bweretsani munthu wina ku mapemphero a la Mulungu ano.

(9) Werengani Baibulo pang’ono pa ng’ono. Wophunzira wina Dr. Samuel Johnson anakayendera Fumu yaku Mangalande, awiriwa anakhala chete kwa kanthawi osalankhulana. Kenaka, Fumu inati kwa Dr. Johnson, “Ukuwoneka kuti umawerenga kwambiri.” “Inde, Bwana,” anatero Dr. Johnson, “komanso ndimaganizira kwambiri.z’

(10) Khalani ndi chikhulupiriro pa Mulungu. Sadzakukhumudwitsani.


Mulungu akudziwa kuti mpingo wanu ukusoweka chitsitsimutso. Ndipo chikhoza kubwera kudzera mwa anthu otsitsimutsidwa, ngati inuyo.

Ndikufuna chiphunzitso ichi mupite nacho kunyumba. Chitani monga m’mene Dr. Tozer ananenera za chitsitsimutso. Tsitsimukani ndipo Mulungu adzakugwiritsani ncthito pa kuthandiza ena kuti nao awone chitsimutso cheni-cheni. Imani kuti tiyimbe nyimbo yathu.

Dzazani masomphenya anga, Mpulumutsi, Ndipemphera, Ndiwone Yesu Yekha lero;
   Ngakhale ndiyende mchingwa Mumanditsogolera, ulemerero Wanu wosatha undikuta
Dzazani masomphenya anga, Mpulumutsi wopambana, Kudzera mwa ulemerero wanu mzimu wanga udzawala.
   Dzazani masomphenya anga, kuti onse aone chithunzi Chanu chikuwala mwa ine.

Dzazani masomphenya anga, chikhumbo changa chonse Chisunge ulemerero Wanu; moyo wanga watakasika.
   Ndi chikondi Chanu changwiro, Chikusefukira panjira yanga ndi kuwala kochoka ku mwamba.
Dzazani masomphenya anga, Mpulumutsi wamphamvu, mpakana ndi ulemerero wanu mzimu wanga udzawala.
   Dzazani masomphenya anga, kuti onse owone chithunzi Chanu chikuwala mwa ine.


Dzazani masomphenya anga, musalole Mthunzi wa tchimo uphimbe kuwala kwa mkati mwanga.
   Ndione nkhope Yanu yodalitsika yokha, Pakudyetsa moyo wanga ndi chisomo Chanu.
Dzazani masomphenya anga, Mpulumutsi wodabwitsa, Mpakana ulemerero wanu uwalire pa mzimu wanga.
   Dzazani masomphenya anga, kuti onse owone chithunzi Chanu chikuwala mwa ine.

(“Dzadzani Maso mphenya Anga,” Woyimba Avis Burgeson Christiansen, 1895-1985).


MUKAFUNA KULEMBERA DR.HYMERS MUYENERA KUTCHULA DZIKO LIMENE MUKULEMERA APO AYI SADZATHA KUYANKHA KALATA YANU. Ngati maulaliki awa akudalitsani tumizani e-mail kwa Dr. Hymers ndikumuuza, koma nthawi zonse tchulani dziko limene mukulembera. E-mail ya Dr. Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net dafanyani apa. Mukhoza kumulembera Dr. Hymers mchilankhulo chirichonse, koma muyesetse Mchigerezi ngati mungathe. Ngati mukufuna kulembera Dr. Hymers pa positi, keyara yake ndi P.O. Box 15308, Los Angels, CA 9001. Mukhoza kuimba foni pa (818) 352-0452.

(MAPETO A ULALIKI)
Mukhoza kuwerenga ma ulaliki a Dr. Hymers sabata iriyose pa intaneti iyi
www.sermonsfortheworld.com,
dafanyani “Maulaliki mchichewa.”

Maulaliki awa si oletsedwa. Mukhoza kuagwiritsa ntchito kopanda kufuna chilorezo kwa
Dr. Hymers. Komabe, maulaliki a mkanema ya tchalitchi lathu ngofunika kuagwiritsa
ntchito potenga chilorezo