Print Sermon

Cholinga cha tsamba ili ndi kupereka ma ulaliki a ulere olembedwa komanso a mkanema kwa a busa mdziko lonse la pansi makamaka maiko okwera kumene, komwe kuli ma sukulu a Baibulo ochepa kapena kulibiretu.

Maulaliki awa olembedwa komanso a m’ma video akupezeka pafupifupi m’ma kompyuta 1,500,000 m’maiko 221chaka chilichonse pa www.sermonsfortheworld.com. Anthu zikwi-zikwi amaonera kanema wa pa YouTube, koma kenaka amasiya YouTube ndikubwera ku website yathu. You Tube imawalondolera anthu ku website yathu. Maulaliki olembedwawa akupezeka mzilankhulo 46 mu makomputa 120,000 mwezi uli wonse. Maulalikiwa alibe chiletso, kotero alaliki akhoza kuagwiritsa ntchito mosafuna chilolezo. Chonde sindikizani apa kuti mudziwe m’mene mungaperekere thandizo la mwezi ndi mwezi lomwe lingathandize kwakukulu pofalitsa uthenga wa bwino kudziko lonse la pansi.

Mukafuna kulembera Dr. Hymers nthawi zonse muuzeni dziko limene mukukhala, apo ayi sangakuyankheni. E-mail ya Dr.Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net.




MA DIKONI A M’BAIBULO

BIBLICAL DEACONS
(Chichewa)

ndi Dr. R.L. Hymers, Jr.,
Mbusa Emeritus

Phunziro lophunzitsidwa pa chihema cha Baptist ku Los Angeles
Kumadzulo kwa tsiku la Ambuye, Januwale 10, 2021
A lesson taught at the Baptist Tabernacle of Los Angeles
Lord’s Day Afternoon, January 10, 2021

Nyimbo yoimbidwa chiphunzitso chisanayambe: “Kutenga kanthawi pokhala mchiyero” (Woyimba William D. Longstaff, 1822-1894; ndime 1, 2 ndi 4).


Madzulo ano ndikufuna mudziwe zimene Baibulo likunena zokhudza ma dikoni. Chonde tsekulani Machitidwe a tumwi 6:1-7).

“Koma masiku awo pakuchulukitsa ophunzira, kunauka chidandaulo, Aheleniste kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye awo anaiwalika pachitumikiro cha tsiku ndi tsiku. Ndipo khumi ndi awiriwo anaitana unyinji wa ophunzira, nati, sikuyenera kuti tisiye mau a Mulungu ndi kutumikira podyerapo. Chifukwa chache, abale, yang’anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi. Koma ife tidzalimbika m’kupemphera, ndi kutumikira mau. Ndipo mau amene anakonda a unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanora ndi Timo, ndi Parmena ndi Nikolao ndiye wopinduka wa ku Antiokeya: amenewo anawaika pamaso pa atumwi; ndipo m’mene anapemphera, Anaika manja pa iwo. Ndipo mau a Mulungu anakula; ndipo chiwerengero cha akuphunzira chidachurukatu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikuru la ansembe linamvera chikhulupirirocho. (Machitidwe a Atumwi 6:1-7).

Mukhoza ku khala.

Mbusa wanga wa kale pamene ndinali ku mpingo wa chi China wa Baptist wa ku Los Angeles, Dr. Timothy Lin, adafunsa amene amafuna kusankhidwa kukhala ma dikoni kuti alonjeze kutsatira zowayenereza khumi:

"Zinthu Kumi ‘ZOYENERA’ wofuna kusankhidwa kukhala dikoni mu mpingo”

(1) Akhale ndi chidwi chofuna kutumikira Ambuye ngati dikoni ndi kufuna kukhala wolemekeza wina ndi mzake.

(2) Ayesetse kukwaniritsa zowayenereza za pa 1Timoteo 3:1-10.

(3) Ayenera kumawerenga Baibulo ndi kumapemphera tsiku ndi tsiku ndi kumapereka cha chikhumi mwasangala nthawi zonse.

(4) Ayenera kukhala wokwatira, ndipo mkazi wake ayenera kukhala wofuna kuthangatira mwamuna wake m’mene angathere.

(5) Akhale wakutha kuphunzitsa Sande sukulu.

(6) Ayenera kukhala wokonzekera kutumikira Ambuye pena paliponse, makamaka pokayendera ena.

(7) Ayenera kumapezeka pa kukumana kulikonse, monga kukumana kwa mapemphero konse, sande sukulu kukumana kwa a zitsogoleri, ndikumathandizira zitukuko zonse za pa mpingo.

(8) Ayenera kumakhala nao pa ziphunzitso zonse zochitika mu mpingo ndi zochitika zina.

(9) Ayenera kumapereka chitsanzo chabwino kwa a Kristu oyamba kumene. Osamakangana nao kapena kumawapsera mtima ndikusamawaphunzitsa bwino.

(10) Ayenera kumagwira ntchito ndi abusa.
     (Dr. Timothy Lin, Chinsinsi cha kukula kwa mpingo)


Apa Dr. Lin amanena zoona. Ngati ma dikoni amatsatira zimene Dr. Lin amanena, sakana bweretsa mpatuko. Koma siziri choncho masiku ano.

Madikoni amipingo yodziyimira yokha ngati wathuwu, ndi amene akuyambitsa mipatuko. Madikoni akuyambitsa 92 peresenti ya mipatuko ya mipingo. 93 peresenti ya mipatuko ya m’mipingo ya Southren Baptist. Kafuku-fuku uyu watengendwa mbuku la Mpatuko wa m’mipingo, lolembedwa ndi Dr. Roy L. Branson. Dr. W.A. Criswell ananenapo za buku la Dr. Branson, Mipatuko ya m’mipingo.

Ngati munaphonyana ndi buku lina lirilonse mchaka ichi, musaphonyane ndi bukhu la Mpatuko wa m’mipingo. Ndi buku lofunika kukhala ndi mbusa aliyense kuti aliwerenge.

– Dr. W. A. Criswell,
  Mbusa wa kale wa
  First Baptist Church,
  Dallas, Texas.


Dr. Lee Roberson, wamkulu wa sukulu ya ukachenjede ya Temple anati, za buku la Dr. Lee Roberson.

Abusa ndi atsogoleri adzapindula powerenga buku limeneri.

Branson anati, “Madikoni ambiri ndi oopsa chifukwa amafuna kugwira ntchito imene sanaiphunzire” (Branson, tsamba 51

)

Kodi tingapewe bwanji kugawanika kwa mipingo mtsogolomu? Dr. Branson anati tiyenera kubwerera ku ndondomeko. Dr. Branson akuti

a. Ntchito yawo ndi kulalika, kupemphera, kuphunzitsa ndi kufikira otayika.

b. Amachita motsogozedwa ndi abusa awo.

“Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mau a Mulungu; ndipo poyang’anira chitsiriziro cha mayendedwe ao mutsanze chikhulupiriro chao” (Ahebri 13:7)

“Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi Chimwemwe, osati mwa chisoni: pakuti ichi sichikupindilitsani inu.” (Ahebri 13:7)

c. Kusaka osowa ndi kuwaphunzitsa ndichimene chinali pa mtima pao.

d. Phweketsani chiri chonse!

Siyani zonse koma kulalikira, kupemphera ndi kupindula miyoyo ndiko.


1. Siyani mikumano ya mwezi ndi mwezi.

2. Siyani mikumano ya ma dikoni.

3. Ndi zina zotere. (tsamba 228, 229, 230 Branson).

4. Siyani mikumano ya a kulu a mpingo.


Dr. Branson anati, “Mkumano wokhawo ‘wa ntchito’ m’Baibulo unali pamene abusa/aneneri anasonkhanitsa anthu nati, ‘Izi ndizimene titachite,’ ndipo anthu anayankha , ‘Ziribwino, ife tichita zomwezo.’”

Dr. Branson anati, “Madikoni ambiri ndi oopsa chifukwa amafuna kugwira ntchito imene sanaiphunzire” (Branson, tsamba 51)

Ma dikoni si woyendetsa mpingo; palibe m’Baibulo lonse pamene anapatsidwa mphamvu zopanga ziganizo. Ulamuliro wa pa mpingo unapatsidwa m’manja mwa mbusa. Mulungu akuti,

“Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi Chimwemwe, osati mwa chisoni: pakuti ichi sichikupindilitsani inu.” (Ahebri 13:7)

M’modzi wa ma dikoni anafunsa, “Nanga mukuganiza kuti ma dikoni ayenera kutani?”

Mbusa anatsekula Machitidwe a tumwi 6:1-6. Kenaka mbusa anati, “ Iyi ndi ntchito yokhayo imene inapatsidwa kwa ma dikoni m’Baibulo.” Ndipo dikoniyo anati, “Baibulo likupereka ulamuliro wina wambiri kuposera umenewo!”

Kenaka dikoni wina anati, Ndikudziwa Baibulo likupereka ulamuliro wochuluka kuposera umenewu.”

Mbusa anati, “Aka ndikomariza kumva phunziro limenero. Chifukwa? Chifukwa sizikupezeka m’Baibulo.”


Pakuti ma dikoni sadzozedwa ndiponso sauza mbusa zochita kapena zoti asachite, ine monga woyambitsa ndi mbusa Emeritus wa mpingo uno, ndikusankha pakali pano amuna atatu kukhala ma dikoni kwa chaka chimodzi. Ndikusankha Bambo Mencia, Bambo Ngann ndi bambo John Wesley Hymers kukhala madikoni kwa chaka chimodzi, ndi Dr, Cagan kwa zaka ziwiri.

Tidzakhala ndi mkumano umodzi m’mwezi wa Januwale, pamene ndi dzasankhe kapena kusankhaso ma dikoni kwa chaka china chimodzi ndikadzaona kuti ndiwoyenera kutero.

Ndiwerenganso ndime ija. Chonde tsekula naneni m’Baibulo mwanu Machitidwe a tumwi 6:1-7

“Koma masiku awo pakuchulukitsa ophunzira, kunauka chidandaulo, Aheleniste kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye awo anaiwalika pachitumikiro cha tsiku ndi tsiku. Ndipo khumi ndi awiriwo anaitana unyinji wa ophunzira, nati, sikuyenera kuti tisiye mau a Mulungu ndi kutumikira podyerapo. Chifukwa chache, abale, yang’anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi. Koma ife tidzalimbika m’kupemphera, ndi kutumikira mau. Ndipo mau amene anakonda a unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanora ndi Timo, ndi Parmena ndi Nikolao ndiye wopinduka wa ku Antiokeya: amenewo anawaika pamaso pa atumwi; ndipo m’mene anapemphera, Anaika manja pa iwo. Ndipo mau a Mulungu anakula; ndipo chiwerengero cha akuphunzira chidachurukatu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikuru la ansembe linamvera chikhulupirirocho. (Machitidwe a Atumwi 6:1-7)

.

Chonde Imani ndi kuyimba nyimbo yathu,

Khalani mchiyero, Lankhulani ndi Ambuye;
   Khalani mwa Iye nthawizonse, ndikudya Mau Ake.
Khalani abwenzi a ana a Mulungu, Thandiza ofoka,
   Osaiwala kufuna mdalitso wake.

Khala mchiyero, Dziko likuthamanga;
   Khala ndi Yesu nthawi zonse.
Poyang’ana kwa Yesu mudzakha ngati Iye;
   Abwenzi anu adzakuonani mukufana ndi Iye.

Khalani mchiyero, Khalani bata muntima mwani.
   Maganizo ndi zolinga zikhale zotsogozedwa ndi Iye.
Potsogozedwa ndi Mzimu Wake Ku kasupe wa chikondi,
   Posachedwa tigwira ntchito yake m’mwamba.
(“Kutenga nthawi pokhala Mchiyero” ndi William D, Longstaff, 1822-1894; ndime 1,2, ndi 4).


MUKAFUNA KULEMBERA DR.HYMERS MUYENERA KUTCHULA DZIKO LIMENE MUKULEMERA APO AYI SADZATHA KUYANKHA KALATA YANU. Ngati maulaliki awa akudalitsani tumizani e-mail kwa Dr. Hymers ndikumuuza, koma nthawi zonse tchulani dziko limene mukulembera. E-mail ya Dr. Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net dafanyani apa. Mukhoza kumulembera Dr. Hymers mchilankhulo chirichonse, koma muyesetse Mchigerezi ngati mungathe. Ngati mukufuna kulembera Dr. Hymers pa positi, keyara yake ndi P.O. Box 15308, Los Angels, CA 9001. Mukhoza kuimba foni pa (818) 352-0452.

(MAPETO A ULALIKI)
Mukhoza kuwerenga ma ulaliki a Dr. Hymers sabata iriyose pa intaneti iyi
www.sermonsfortheworld.com,
dafanyani “Maulaliki mchichewa.”

Maulaliki awa si oletsedwa. Mukhoza kuagwiritsa ntchito kopanda kufuna chilorezo kwa
Dr. Hymers. Komabe, maulaliki a mkanema ya tchalitchi lathu ngofunika kuagwiritsa
ntchito potenga chilorezo