Print Sermon

Cholinga cha tsamba ili ndi kupereka ma ulaliki a ulere olembedwa komanso a mkanema kwa a busa mdziko lonse la pansi makamaka maiko okwera kumene, komwe kuli ma sukulu a Baibulo ochepa kapena kulibiretu.

Maulaliki awa olembedwa komanso a m’ma video akupezeka pafupifupi m’ma kompyuta 1,500,000 m’maiko 221chaka chilichonse pa www.sermonsfortheworld.com. Anthu zikwi-zikwi amaonera kanema wa pa YouTube, koma kenaka amasiya YouTube ndikubwera ku website yathu. You Tube imawalondolera anthu ku website yathu. Maulaliki olembedwawa akupezeka mzilankhulo 46 mu makomputa 120,000 mwezi uli wonse. Maulalikiwa alibe chiletso, kotero alaliki akhoza kuagwiritsa ntchito mosafuna chilolezo. Chonde sindikizani apa kuti mudziwe m’mene mungaperekere thandizo la mwezi ndi mwezi lomwe lingathandize kwakukulu pofalitsa uthenga wa bwino kudziko lonse la pansi.

Mukafuna kulembera Dr. Hymers nthawi zonse muuzeni dziko limene mukukhala, apo ayi sangakuyankheni. E-mail ya Dr.Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net.
KUYANKHA MAFUNSO

ANSWERING QUESTIONS
(Chichewa)

ndi Dr. R.L. Hymers, Jr.
Mbusa Emeritus

Chiphunzitso choperekedwa pa Chihema cha Baptist yaku Los Angeles
kumadzulo a tsiku la a Ambuye, October 4, 2020
A lesson given at the Baptist Tabernacle of Los Angeles
Lord’s Day Afternoon, October 4, 2020

Nyimbo phunziro lisanayambe:
“O malilime zikwi” (woyimba Charles Wesley, 1707-1788).


Kodi muyenera kukhumudwa munthu akakufunsani? Nzoona nzakuti ayi. Mtumwi Petro anati,

“Koma mumpatukitse Ambuye Kristu m’mitima yanu; okozeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chiri mwa inu, koma ndi chifatso ndi mantha.” (1 Petro 3:15)

Mafunso ofunsidwa kawiri-kawiri

1. Sindikhulupirira Baibulo.

Mtumwi Paulo ananena zolembedwa Mbaibulo kwa anthu amene samalikhulupirira. Paulo samayesa kuwakakamiza kuti akhulupirire zimene amanena. Potumikira tiyenera kumango lengeza osati kuteteza.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +
MA ULALIKI ATHU AKUPEZEKA MU MA FONI
ANU A M’MANJA TSOPANO.
PITANI KU WWW.SERMONSFORTHEWORLD.COM.
DAFANYANI BATANI LOBILIWIRA LOMWE LIRI NDI LIU LOTI “APP”
TSATIRANI MALANGIZO OTSATIRAWO.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

Uthenga weni-weni wa Baibulo ndi woti kodi angakhale bwanji ndi moyo wosatha. Ngati akunena kuti sakukhulupirira moyo wosatha, mukhoza kunena kuti, “Kodi mumalimvetsa bwanji Baibulo likamanena za mutu umenewu?” Ndipo mukumvetsa bwanji ndi m’mene Baibulo limaphunzitsira za zimenezi?”

Nthawi zambiri, amanena kuti, “Posunga Malamulo Khumi kapena kutsanzira Kristu.” Ndiye mutha kunena kuti, “izi ndi zimene ndimaopa. Mwalikana Baibulo pakusamvetsa chiphunzitso chake, pakuti yankho lanu silolakwika kokha, koma ndi zotsutsana kwathunthu ndi zimene Baibulo limaphunzitsira. Tsopano, sichinthu chanzeru kwambiri kodi kundilora ine kuti ndigawane nanu zimene Baibulo likuphunzitsa pa za phunziro limeneri? Potero mukhonza kukhala ndi chisankho chabwino cha kukana kapena kubvomereza.”

Tsopano ndikuwerengerani zolosera khumi za Yesu.

(1) Kunyozedwa,

“Ndipo anandipatsa ndulu ikhale chakudwa change; nandipatsa vinyo wasasa pomva ludzu ine” (Masalmo 69:21)

(2) Kunzunzika chifukwa cha ena

“Zoonadi Iye ananyamula zowawa zathu, ndi kusenza zisoni zathu…analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu; na tundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu… Yehova Anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse” (Yesaya 53:4-6)

.

(3) Kuchita zozizwa

“Pamenepo maso a akhungu adzatsekuka, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa”. (Yesaya 35:5 – 713 zaka Khristu asanabadwe)

(4) Kuperekedwa ndi a nzake.

“Ngakhale bwenzi langa leni-leni, amene ndamkhulupirira, ndiye amene anadyako mkate wanga, adandikwesera chidendene chake.” (Masalmo 41:9).

(5) Kugulitsidwa ndi ndalama za siliva makumi atatu

“Ndipatseni mphotho yanga…ndipo anayerekeza mphotho yanga ndalama za siliva makumi atatu” (Zekariya 11:12 – 713 zaka Khristu asanabadwe).

(6) Kulavulidwa ndi ku kwapulidwa

“Ndinapereka msana wanga kwa iwo omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene anakutsula tsitsi langa.” (Yesaya 50:6 – 712 zaka Khristu asanabadwe)

(7) Kukhomedwa pa mtanda.

“Andiboola manja anga ndi mapazi anga” (Masalmo 22:16)

(8) Kusiidwa ndi Mulungu.

“Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?” (Masalmo 22)

(9) Kuuka kwa akufa kwake.

Simudzalola wokondedwa wanu avunde. (Masalmo 16:10)

(10) Kutembenuka kwa a mitundu kwa Iye.

“Taona mtumiki wanga…Iye adzatulutsira a mitundu chiweruziro” (Yesaya 42: 1 – 712 zaka Khristu asanabadwe)

Awa ndi ma uneneri khumi chabe akulosera za Yesu. Muli ma uneneri oposera mazana awiri m’Baibulo omwe akwaniritsidwa kale.

Zaka zingapo zapitazo, magazini ya National Enquirer inalemba mndandanda wa ma ulosi oloseledwa ndi “aneneri” a masiku ano 61, Mauneneri 61 amenewa amayenera kuchita miyezi isanu ndi umodzi wa chaka chimenecho. Kodi mauneneri amanewa anakwaniritsidwadi? Khulupirirani kapena ayi, mauneri onse 61 anaphonya! Anati Papa Paulo adzapuma ndi mpingo wonse wa a Katorika adzalamulidwa ndi akulu a mpingo; anati George Foreman adzapitirira kukha ngwazi ya nkhonya molingana ndi Mohammed Ali mu Afrika; komanso kuti Ted Kennedy adzachita kampeni ya upulezidenti! Kusiyana kwa mauneneri amasiku anon ndi aja a m’Baibulo ndi koti “mauneneri” amasiku ano anali si anali oona ndi aneneri a m’Mbaibulo anali olondola.

2. Kodi kasinthidwe ka zinthu kamatsutsana ndi chilengedwe?

Dr. A.W. Tozer anati, “Ife amene timakhulupirira Baibulo timadziwa kuti dziko ndi chilengedwe. Si la muyaya poti liri ndi poyambira. Sikuti zinangochitika mwa ngozi kuti chudutwa cha chinthu china chinakalumikizani ndi chofanana nacho kenaka nkusanduka cha moyo pa malo pena pake. Munthu wokhulupirira izi ndi yekhayo amene amasankha kukhulupirira chinthu popanda umboni.

Mnyamata wina anafunsidwa, “Kodi ungapereke umboni wanji womwe unakopedwa nao woti zinthu ziripozi zinachita kusandulika kuchoka ku zinthu zina zomwe zinalipo ndi zoona?

Mzaka za m’ma 1950 James Watson ndi Francis Crick anatulukira tiziduthwa tating’onoting’ono topezeka mmatupi a anthu totchedwa – DNA. Kutulukira kumeneku kunawapangitsa kuti alandire mphotho ya ulemu wa padela. Thupi lamunthu liri ndi tizidutswa tating’onoting’ono timeneti tambiri-mbiri. Ndi tolukana-lukana modabwitsa.

Crick, munthu wosakhulupirira kuti kuli Mulungu komanso wokhulupirila kuti zinthu zinapezeka mkusintha kwa nyengo, anaganiza zofufuza kuthekera koti mwina tizidutswa topezeka m’matupiti tinakula tokha mkupita kwa nthawi kwa zaka za 4.6 biliyoni zomwe ndi zaka za dziko lapansi. Kodi mwayi wa mbiri ya kachidutswa kamodzi ngotani? Mukudziwa zimene anapeza? Zilo. Chingakhale patatha zaka 4.6 biliyoni sizikanatha kuchitika kuti kachidutwa kamodzi kasinthe!

Kodi izi zinamupanitsa Francis Crick ku aganize kuti ndi Mulungu anachita zimenezi? Ayi ndithu sanatero.

Kodi chikuoneka cha chilendo kuti a za sayansi amenewa anafeka povomereza kuti zomwe ankanenazo ndi zabodza? Palibe amene ananena, “kuyambira nthawi ya Darwin, takhala tikuphunzitsa zabodza. Tinkakuphunzitsani kuti moyo unapangidwa kudzera mkulumikizana kwa tizidutwa ta milofu. Tsono patatha zaka za mbiri, si uyu tikadali chimodzimodzi. Tinkaganiza kuti umu ndi momwe zinaliri. Nzeru zathu za tsutsika. Tikupepesa kuti tinakusokeretsani.”

Kodi mukudziwa zimene Francis Crick anachita? Anabweranso ndi kaganizidwe kena koti mtundu wina wa zamoyo unaikidwa mchombo cha mlenga-lenga pamodzi ndi mphamvu za umuna, ziri mmenemo zinalumikizana ndi zamoyo za kumeneko ,ati umu ndi m’mene if anthu tinapezekera mdziko lino. Zikumveka ngati kanema.

Moyo sungatuluke mzopanda moyo. Ndichifukwa chake Baibulo limanena kuti, “Pachiyambi Mulungu kumwamba ndi dziko la pansi” (Genesis 1:1).

Zizindikiro zitatu zomwe zandithandiza kuti Mulungu aliko:

(1) Lamulo la chiyambi ndi zotsatira.

     M’mene ndimaonera zinthu mlenga-lenga zinaikidwa mwa loso zomwe zimandisonyeza kuti zinayambira ku chinachake chosaoneka ndi maso yemwe ndimakhulupirira kuti ndi Mulungu.

(2) Umboni wa kapangidwe ka zinthu.

     Mutapita ku dziko la Masi ndikukapezako wotchi yopangidwa mwa luso kumeneko, mukhoza kuzindikira kti wotchiyo yapangidwa ndi wopanga wotchi. Kotero dziko lolengedwa bwinoli limalozera wolenga dziko, wopanga wochedwa Mulungu.

(3) Umboni wa umunthu.

     Tikaona chojambula cha Mona Lisa; timaona umboni wa umunthu. Cithunzichi sichisonyeza kuti wina akuyerekezera. Umboni wa chitatu uwo ndi wofunikira chifukwa sitingaweruzidwe ndi zongochitika kapena mphamvu chabe. Koma munthu ndi amene angathe kutiweruza chifukwa cha machismo athu.

3. Mulungu wanga Sali chomwecho.

Moyo wa John Wesley amene anayambitsa mpingo wa Methodist, analongosola momveka kufunikira ko dalira Mulungu yekha kuti ndiye amapulumutsa. Anapita ku sukulu ya ukachenjede ya Oxford kwa zaka zisanu ndikukhala mbusa wa Mpingo wa ku Mangalande, kumene anatumikira kwa zaka khumi. Kumapeto kwa nthawi imeneyo, pafupi-fupi mzaka za 1735, anachoka ku Mangalande nkukakhala wa Mishoni ku Georgia.

M’moyo wake wonse, anali wolephera mu utumiki wake, chingakhale amatha kutchula anthu amene wa afikira ndi uthenga, kunali kudzipereka kwa thunthu. Amadzuka mbanda kucha ndi kupemphera ma ola awiri. Kenaka ndikuwerenga Baibulo ola limodzi asanatulike kupita kukalalika ku ndende, ndi ku chipatala. Amaphunzitsa, kupempherera, ndi kuthandiza anthu ampaka usiku. Anachita izi kwa zaka zambiri. Makamaka dzina loti Methodist Church lidayambira pamenepo, moyo wa ndondomeko umene Wesley ndi a nzake amakhala.

Pamene amabwerera kuchoka ku Amereka, panali mphepo yaikulu pa Nyanja bwato limene amagwiritsa ntchito linali laling’ono kotero kuti linatsala pang’ono kumira. Mafunde akulu anakhavirira amkabwatoko ndipo amalinyero anayamba kuchita mantha. Wesley naye zinamchititsa mantha kotere amaganiza kuti akufa. Analibe chitsimikizo choti kodi akafa chimuchitikire ndi chiyani. Chingakhale anayesetsa kukhala munthu wa bwino, infa inamukulira ndipo linali funso losayankhidwa.

Mbali ina ya bwatoli kunali kagulu ka anthu amene anali kuimba nyimbo za chitsitsimutso. Anawafunsa, “Inu mukuyimba bwanji pamene mukuona kuti usiku omwe uno mumwalira?” Iwo anayankha, “Ngati bwato iri litamire kulowa pansi pa Nyanja, ife tikwera m’mwamba kukakhala ndi Ambuye kwa nthawi zonse.”

Wesley zinamuzunguza mutu, naganiza kuti, “Kodi iwo akudziwa bwanji izi?” “Ndichiyani chimene iwo anachita kuposa ine?” natinso, “Ine ndinabwera kuno kuti ndidzatembenuze anthu achikunja. Ah, koma nanga atembenuze ine ndani?”

Mchifundo cha Mulungu, bwato linakakocheza bwino ku doko la ku Mangalande. Wesley anapita ku Mzinda wa London mpaka kukafika ku makwalala a Aldersgate kumene kunali kachihema kakang’ono. Atafika kumeneko anamva munthu akuwerenga ulaliki umene unalembedwa zaka zambuyomo ndi Martin Luther, mutu wake unali woti “Mau oyamba a buku la Aroma.” Ulaliki umenewu umalongosola za chikhulupiriro cheni-cheni ndi chiti. Ndi kudalira Kristu yekha kuti ndi amene anapulumutsa – osati pa ntchito zathu zabwino.

Mwadzidzi Wesley anazindikira kuti amalakwitsa nthawi yonseyi. Usiku umenewo analemba izi mkabuku kake: “Isanakwane nayini koloko, akanalongosola za kusintha kumene kwachitika chifukwa chokhulupirira mwa Kristu, ndinamva chinthu cha chilendo mumtima mwanga. Ndinadzimva kuti ndakhupirira Kristu, Kristu yekha, pa chipulumutso; ndipo ndinatsimikizika kuti anachotsa machimo anga onse, nandipulumutsa ku chilamulo ndi infa.”

Ziri moterotu. Chikhulupiriro chopulumutsa. Kulapa machimo ake, anamudalira Yesu Kristu yekha kuti ndiye wopulumutsa. Tsono tinganene kuti Wesley anali asanakhulupirire Yesu Kristu usanafuke usiku umenewu? Zoona zake nzakuti anali atakhulupirira. Anaphunzira za Kristu Mchingerezi, Mchi Latini, mchi Giriki ndi mchi Hebere. Anakhulupirira Kristu mzilankhulo zonsezi. Koma amadalira Yohane Wesley mchipulumutso chake.

Zitachitika izi, anasanduka mlaliki wa mphamvu m’masiku amenewo. Zosezi zinayambika pamene anadalira Yesu Kristu yekha pa chikhulupiriro chake namulandira iye ngati Mbuye wake. (Dr. D. James Kennedy, Evangelism Explosion, kulembedwa kwa chinayi, nyumba yosindikiza mabuku ya Tyndale, 1996, tsamba 183-184).

Episitemoloje ndi nthambi ya kaganizidwe kamene kamalimbana ndi kuyankha funso loti – timadziwa bwanji? Pali njira ziwiri za kaganizidwe zomwe zimayankha funso loti- timadziwa bwanji? Pali njira ziwiri zimene anthu amayankhira funso la mmene amaganizira za Mulungu.

1. Kaganizidwe. Pakungogwiritsa ntchito kaganizidwe zatengea kuzikhulupiriro za chilendo.

2. Bvumbulutso. Tsopano, Mpingo wa chikristu wakhala ukumva kuti Mulungu anadzibvumbula yekha kudzera m’Mbaibulo, komanso kudzera mwa mwana wake, Yesu Kristu. Tsopano nkhani siyoti kodi wina aliyense wa ife akuganiza bwanji. Koma funso likhale loti, “Kodi Mulungu anati chiani m’Baibulo ndi kudzera mwa mwana wake, Yesu Kristu?”

4. Kodi achikunja ndi wotayika?

     Nena, “Zimene tikuchita pano ndizofunika msanga kusiyana ndikumangokhazikika pa zo choka m’mutu.
     Mukhoza kunena kuti, “Bob, limeneri ndi funso la bwino, koma tikhonza kuwasiya a chikunja a ku Afirika m’manja mwa Mulungu, chomwe ndi chabwino kwambiri. Lero ndikufuna kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wa muyaya. Mwina kumapetoku tiona zonse zimene Mulungu ananena za onse amene sanamve za uthenga wabwino… Bvuto limene likuzungulira pa funsoli ndi loti, ‘Kodi Mulungu adzaponya achikunja ku Gehena chifukwa choti sanakhulupirire Kristu yemwe sanamumvepo?’
     Baibulo limaphunzitsa kuti Kristu sanabwere kudzatsutsa omwe antsutsidwa kale. Anthu amatsutsidwa pa chifukwa chimodzi chokha - machimo awo.”

5. Sindikhulupirira za moyo wina munthu akamwalira.

     Pulato. Woganiza mwa kuya wa kale dzina lake Pulato anawonetsera kuti mbewu iturutse mtengo wa zipatso zabwino iyenera kudutsa mu ndondomeko ya kufa kaye. Puluto anamalizira ndikuti thupi liyenera kufa kaye lisanasandulikire ku dziko la tsopano ndi moyo wina.
     Pulato anakhala zaka zambiri asanadzewe Kristu ndi Mtumwi Paulo. Koma anaphunzitsabe za chitsimikizo cha kuti kuli moyo munthu akafa zomwe Paulo ndi Kristu ananena pa I Akorinto 15:35-36 ndi Yohane 12:24 Woganiza mwakuya wina dzina lake Immnuel Kant anazindikira kuti anthu onse amakhudzidwa ndi chabwino kapena choipa, ananena kuti, “Tiyenera kuchita za bwino bwanji ngati chilungamo palibe?” Mnjira yina, anaganizira kuti kachitidwe kazinthu kuti kakhale ka nzeru, payenera pakhale chilungamo, chifukwa uchita bwanji zabwino ngati palibe chilungamo? Ndiye anaganiza kuti pakuti chilungamo chikusowa m’moyo uno, kuyenera kuti kuli moyo wina kumene kuli chilungamo. Mwanjira ina tikhonza kunena kuti, woganiza mwakuya ameneyu Kant chilungamo chidzaoneka m’moyo wina, uno ukatha. Izi zikumveka mofanana ndi zimene Baibulo likunena pa Ahebri 9:27)
     Ndiye malinga ndi Immanuel Kant, zeni-zeni nzakuti kuli moyo wina tikafa, ndiye woweruza wake ndi kukhala Mulungu wa m’Baibulo.

(1) Lamulo loyamba la kasinthidwe ka zinthu kupita ku chikhalidwe china, monga m’mene anakhazikitsira Einstein. Limanena kuti mphamvu ndi zidutwa za thupi sizinalengedwe kapena kuonongeka. Ngati munthu atasiya kupezeka, adzakhala cholengedwa chokhacho padziko lonse amene amadzionetsera. Baibulo pa I Akorinto 15:49-51 pakulongosola m’mene thupi la Kristu lidzapiririre. Einstein sanali wosakhuluprira.

(2) Mau omaliza a munthu amene akufa.

     Munthu wosakhulupirira kuti Mulungu alipo wotchedwa Gibbon, pamene amamwalira pa kama wake, analira motere, “Ndikuona mdima wokha wokha” Winanso wotchedwa Adams pamene amamwalira anthu anamumva akufuula mokweza, “Ziwanda ziri m’nyumba ino ndipo zikundikokera pansi.”
     Pomwe mbali inayi, m’Kristu amene analembapo nyimbo za chitsitsimutso, dzina lake Toplady analira motere, “Ndikuona kuwala, kuwala, kuwala!” Winanso wotchedwa Everett, kwa mphindi 25 asanamwalire, anati, “ulemerero, ulemerero, ulemerero,” Anthu mazana-mazana apatsidwa mwai woti awone zimene ziri nkudza, ndi moyo umene akhala alinkudutsamo.

6. Kusonkhanitsa anthu otsitsimutsidwa.

Ndikofunika kudziwa kuti akatswiri a za sayansi posachedwapa anagwedeza dziko kuti zotsatira za kafukufuku wao wapangitsa kuti akhulupirire kuti kuseri kwa manda kuli moyo wina. Ndawamvapo akatwiri a za sayansi ena akunena kuti alawapo Kumwamba ndi Gehena. Zimene akuti anakumana nazozi zimatisiya ndi mafunso ambiri. Komatu amapereka maumboni opatsa chidwi.

Elizabeti Kubler-Ross sanali m’Kristu koma analongosola motere, “Zatsimikizika kuti kuli moyo kutsogolo kwa infa.” Dr. Kubler-Ross anati zimene amakumana nazo anthu amene ali pafupi kufazi ndi zotsimikizika ndi sayansi. “Timangochita mantha kuzilankhula,” anatero.

Dr. Raymond Moody anati, “Kumamveka kulira kwa chinganga pamene munthu akufa.” Onse amanena kuti amakhala ngati atuluka mthupi ndi kuyandama mlenga-lenga kwinaku akuona madotolo mchipinda chimene akuyesa kupulumutsira moyo wao. Awa ndi maumboni osati a anthu achepa okha, koma oposera zikwi zisanu, ochokera mdziko lonse la pansi. Onsewa amanena kuti amaona munthu wowoneka ngati wa chipembedzo. Izi ndi zoona makamaka kwa anthu osakhulupirira kuti Mulungu alipo.

Dr. Kubler-Ross ananena izi kwa gulu la madotolo a zachipatala amene ankamumvetsera akulankhula, “Ndinkakonda Kunene kuti, ‘kuli moyo wina munthu akamwalira.’ Koma tsopano ndikudziwa.”

Akatswiri a za chipatala chikwi chimodzi ndi ophunzira anamupatsa chikho cha chipambano atango maliza kulankhula.

7. Nanga kusandulika kwa mzimu kukhala thupi?

Ndichikhulupiriro pakati pa ma Hindu ndi ma Buda, koma osati a Kristu! Ndiyankhe motere, “Baibulo limati, ‘Kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo atafa chiweruziro.” (Ahebri 9:27)

Maganizo onsewa akutsutsana ndi ntchito imene Yesu Kristu anachita yoyanjanitsa mchiyero chake. Pa infa yake ya pa Mtanda Yesu Kristu; anachotsa machimo athu tonse. Kotero tikadalira Yesu, timatsukidwa ndi Mwazi wake wa pa Mtanda.

8. Gehena ndi weni-weni.

Nthawi zina timaona kuti ndi zothandiza kunena kuti, “Mukudziwa kuti kamakhala kaganizidwe komakana kuti kulibe zinthu zimene umaziopa kwambiri. Kotero chifukwa chakuti timaopa Gehena timaopa kuti ngati kuli malo otere ndiye kuti mudzapita kumeneko.” Kawiri-kawiri yankho limakhala loti, “Ndikuganiza kuti mukunena zoona.”

Koma muyenera kukawauza otsatira anu kuti, “Sindikufuna kuti mukhulupirire Gahena. Mukhoza kutsimikizika kuti simudzapita ku Gehena. Ichi ndicho cholinga cha Uthenga wabwino. Ndimakhulupirira kuti kuli Gehena, koma ndikudziwa kuti sindidzapita kumeneko chifukwa cha lonjezano la Mulungu. Izi ndi zomveka bwino kusiyana ndi kunenena kuti, “Ndikudziwa sidzapita ku Gahena chifukwa sindikhulupirira kuti kuli malo ngati amenewo.’”

9. Tiri ndi Gahena wathu pansi pano.

Ndinu odziwa mdera-mdera. Ndaaona anthu ogulitsa mankhwala ozunguza bongo akudutsa m’gahena pansi pompano. Ndaonapo zidakhwa zomangidwa mu ukapolo.

Mbusa Mark Buckley amalankhula za kugwiritsa ntchito makhwala ozunguza bongo ndi kukathera kuchipatala cha amisala. Mbusa Buckley anazemba Gehena pansi pano podalira Yesu. Yesu anamupulumutsa Mbusa Buckley ku mchitidwe wogwiritsa makhwala ozunguza bongo - Gehena wa pansipano ameneyo. Mukhonza kugula buku limene likunena za moyo wake ndi kutembenuka kwake m’dzina la Yesu. Muone ku Amazon.com ndi kugula buku la Mark. Limatchedwa, “From Darkness to Light: My Journey” ndi Mbusa Mark Buckley. Mutangowerenga ma peji oyambirira, mudzakhala ngati mwawerenga buku lonse. Ine ndaliwerenga kawiri konnse.

Sindife osunga Sabata, koma timagwirizana ndi Mbusa Buckley, amene anati,

“Tikadalira Mulungu ndi kupumula, atha kutipatsa chidziwitso chimene chidzapangitse kuti tikhale obala zipatso zambiri. Sindikulimbikitsa kuti tikhale osunga chilamulo. Koma ndikulimbikitsa kuti tizipatulako nthawi yopuma kuti mukhale a thanzi” (Kuchokera mbuku la Darkness to Light: My Journey, wolemba Mark Buckley).

Imana tiyimbe nyimbo yathu!

O kwa malilime zikwi oyimba
   Matamando a wondipulumutsa
Maulemerero a Mulungu ndi Mfumu
   Chigonjetso cha chisomo.

Mbuye wanga wopambana ndi Mulungu wanga
   Ndithandizeni kufalitsa
Kufalitsa dziko lonse lapansi
   Kulemezeka dzina.

Yesu! Dzina loingitsa mantha athu.
   Lochotsa chisoni chathu
’Nyimbo iyi mkhutu la ochimwa
   Moyo uwu, ndi thanzi, ndi mtendere.

Amaphwanya mphamvu chimo
   Amasula a nsinga
Mwazi wake umayeretsa wochimwitsitsa.
   Mwazi wake unakhera ine.
(“O For a Thousand Tongues” woyimba Charles Wesley, 1707-1788).


MUKAFUNA KULEMBERA DR.HYMERS MUYENERA KUTCHULA DZIKO LIMENE MUKULEMERA APO AYI SADZATHA KUYANKHA KALATA YANU. Ngati maulaliki awa akudalitsani tumizani e-mail kwa Dr. Hymers ndikumuuza, koma nthawi zonse tchulani dziko limene mukulembera. E-mail ya Dr. Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net dafanyani apa. Mukhoza kumulembera Dr. Hymers mchilankhulo chirichonse, koma muyesetse Mchigerezi ngati mungathe. Ngati mukufuna kulembera Dr. Hymers pa positi, keyara yake ndi P.O. Box 15308, Los Angels, CA 9001. Mukhoza kuimba foni pa (818) 352-0452.

(MAPETO A ULALIKI)
Mukhoza kuwerenga ma ulaliki a Dr. Hymers sabata iriyose pa intaneti iyi
www.sermonsfortheworld.com,
dafanyani “Maulaliki mchichewa.”

Maulaliki awa si oletsedwa. Mukhoza kuagwiritsa ntchito kopanda kufuna chilorezo kwa
Dr. Hymers. Komabe, maulaliki a mkanema ya tchalitchi lathu ngofunika kuagwiritsa
ntchito potenga chilorezo