Print Sermon

Cholinga cha tsamba ili ndi kupereka ma ulaliki a ulere olembedwa komanso a mkanema kwa a busa mdziko lonse la pansi makamaka maiko okwera kumene, komwe kuli ma sukulu a Baibulo ochepa kapena kulibiretu.

Maulaliki awa olembedwa komanso a m’ma video akupezeka pafupifupi m’ma kompyuta 1,500,000 m’maiko 221chaka chilichonse pa www.sermonsfortheworld.com. Anthu zikwi-zikwi amaonera kanema wa pa YouTube, koma kenaka amasiya YouTube ndikubwera ku website yathu. You Tube imawalondolera anthu ku website yathu. Maulaliki olembedwawa akupezeka mzilankhulo 46 mu makomputa 120,000 mwezi uli wonse. Maulalikiwa alibe chiletso, kotero alaliki akhoza kuagwiritsa ntchito mosafuna chilolezo. Chonde sindikizani apa kuti mudziwe m’mene mungaperekere thandizo la mwezi ndi mwezi lomwe lingathandize kwakukulu pofalitsa uthenga wa bwino kudziko lonse la pansi.

Mukafuna kulembera Dr. Hymers nthawi zonse muuzeni dziko limene mukukhala, apo ayi sangakuyankheni. E-mail ya Dr.Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net.




M’MENE TINGAKHALIRE WOGONJETSA!

HOW TO BE AN OVERCOMER!
(Chichewa)

ndi Dr. R. L. Hymers, Jr.,
Mbusa Emeritus
Wochokera mu ulaliki wolamitsa
wa Timothy Lin. Ph.D., mbusa wanga kwa zaka 24.

Uthenga wolalikidwa pa chihema cha Baptist ku Los Angeles
Kumadzulo kwa tsiku la Ambuye, Julaye 26,2020

A sermon preached at the Baptist Tabernacle of Los Angeles
Lord’s Day Afternoon, July 26, 2020

Nyimbo yoyimbidwa ulaliki usanayambe:
“Ndine msirikali wa Mtanda?” (ndi Isaac Watts, 1674-1748).

“Galamuka, mphepo ya kumpoto iwe, nudze, mphepo iwe ya kum’mwera; nuwombe pamunda panga, kuti zonunkhiritsa zache ziturukemo.” (Nyimbo ya Solomoni 4:16)


Uwu ndi ulaliki wofunikira umene ndinaumvapo m’moyo wanga. Mutati muwerenge nkhani ya mbiri yanga mudzaona m’mene nkhaniyi inasinthira moyo wanga. Dr. Robert L. Summer anati, “Ndimayamikira komanso kusirira munthu amene amaima pa choonadi- chingakhale akumane ndi zotsutsana zambiri. R. L. Hymers, Jr. ali ngati munthu ameneyu” (Ulemu wonse unali kwa ine: Ziphona za chikhulupiriro zimene njira zao zanawoloka njira zanga, nyumba yosindikizira mabuku a Chivangeli 2015, tsamba 103-105). M’modzi mwa a mishoni athu wa ku Indonesia anati, “Dr. Hymers ndi ngwazi amene wagonjetsa nkhondo za mbiri.” Uwu ndi ulaliki wa Dr. Timothy Lin umene unanditakasa kungwira mokhala mgonjetsi. Ndikukhulupirira kuti uthenga uwu

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +
MA ULALIKI ATHU AKUPEZEKA MU MA FONI
ANU A M’MANJA TSOPANO.
PITANI KU WWW.SERMONSFORTHEWORLD.COM.
DAFANYANI BATANI LOBILIWIRA LOMWE LIRI NDI LIU LOTI “APP”
TSATIRANI MALANGIZO OTSATIRAWO.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

Dr. Timothy Lin anati, “munthu sanalengedwe mwa mwai; analengedwa kuti alamulire zolengedwa za Mulungu…umoyo wa Yosefe ukutionetsera m’mene okhulupirira ayenera kukonzekera ulamuliro ulinkudza [mu ufumu uli nkudza wa Kristu].”

Yosefe asanakhale wolamulira Aigupto, Mulungu anamudutsitsa mu zowawa zambiri kumukonzekeretsa kukhala mgonjetsi ndi wosunga Mau Ake mpaka kumapeto a moyo [wake]. Zazikulu zimene Yosefe anachita sizinangopindulira Aigupto okha ai komanso Israeli, komanso ku mpingo wa Mulungu ku zaka zonse ziri nkudza. Pakadapanda Yosefe kulamulira si Aigupto okha amene akanatha chipere komanso Aisraeli, komanso bvumbulutso la maomboledwa la Mulungu la ku Genesis sirikadakwaniritsidwa.

Njira zimene Mulungu anagwiritsa ntchito poumba moyo wa uzimu wa Yosefe zikhonza kuganiziridwa molinga ndi ndi Nyimbo ya Solomo 4:16.

“Galamuka, mphepo ya kumpoto iwe, nudze, mphepo iwe ya kum’mwera; nuwombe pamunda panga, kuti zonunkhiritsa zache ziturukemo.” (Nyimbo ya Solomoni 4:16)

Pozukuta umoyo wa Yosefe mozamitsa, wina nkuona m’mene Mulungu amabvomerezera mphepo za kumpoto ndi za ku m’mwera kuti ziombe pa iye kuti mpaka zonunkhiritsa za khalidwe lake zituruke. Mulungu anakonzekeretsa khalidwe lake kudzera m’manzunzo, kulikhwimitsa thupi lake ndi, zitonzo, kukhumudwitsidwa, kufoketsedwa ndi kusowa chilungamo ndi kusayamikira, kuti maganizo ake akonzekere, kuti kaganizidwe kake kakhale kakuya, ndi kachitedwe kazinthu kuti kakhale ka machawi, ndi kuti chikhulupiriro chake komanso khalidwe lake likhwime ndi chikhuluriro chake pa Ambuye kuti chikulire-kulire. Machitachita a mphepo za ku mpoto ndi kum’mwera m’moyo waYosefe zimachita kuoneka bwino lomwe.

Mphepo za ku m’mwera- Anamva Chikondi cha Makolo.

Chonde tsekulani Genesis 37:1-4.

“Ndipo Yakobo anakhala mdziko limene anakhalamo mlendo atate wache, m’dziko la Kanani. Mibadwo ya Yakobo ndi iyi: Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri anali nkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ache; ndipo anali mnyamata pamodzi ndi ana a Biliha, ndi ana amuna a Zilipa, akazi a atate ache; ndipo Yosefe anafotokozera atate ache mbiri yao yoipa. Koma Israeli anamkonda Yosefe koposa ana ache onse, pakuti anali mwana wa ukalamba wache; ndipo anamsokera iye Malaya a mwinjiro. Ndipo abale ache anaona kuti atate ache anamkonda iye koposa abale ache onse: Ndipo anamuda iye, ndipo sanathe kulankhula ndi iye mwamtendere.” (Genesis 37:1-4)

Dr. Lin anati, “Chikondi cha makolo chimachita kwakukulu pa khalidwe la kutsogolo la mwana…”

“Yosefe amadziwa kusiyanitsa pakati pa chikondi ndi udani… chikondi ndi chilungamo zimayendera pamodzi, koma siziri choncho ndi chikondi ndi choipa, ndi zinthu ziwiri zosiyana. Kuopa kuonetsera choipa si chikondi, koma mantha… Na ngati choilinga cha munthuyo ndi chakusadzikonda, kuonetsera poyera choipa ndi ntchito yotamandika ndipo chiyenera kulimbikitsidwa…Tsatane-tsatane wa maloto awiri a Yosefe anali ophweteka ndipo anatakasa kudzikuza kwa abale ake ndi udani wawonso unatakasidwa; koma Yosefe anali kuwakondabe abale ake komanso anapitiriza kukha mwana womvera bambo ake.”

Ine sindinachione chikondi cha a bambo anga, koma chikondi cha amai ndi chirimbikitso chao chimandipangitsa kuti ndisamawapsere mtima a bamboo. Amai anga sikuti anali a ngwiro, koma “anali achifundo kwambiri, achikondi, koma a machita zinthu mosamalitsa kwambiri, ndakhala ndikuwadziwa motere kuyambira pa ubwana wanga onse. Anandiphunzitsa kukonda ma buku, kuyendetsa galimoto, koposa zonse kuti ndizitha kuima ndikulankhula chimene chiyenera kunenedwa, chingakhale ndikuchinena ndekha” (tsamba 16 la buku la mbiri yanga). Tsono, amai anga anali wotchinjiriza ndi mkhala pakati wanga. Kenaka mai anga anapulumutsidwa ali ndi zaka 80, chinali chinthu chachikuru kwambiri chomwe chinachitika m’moyo wanga.

Mphepo yaku mpoto-kugulitsidwa ku ukapolo
Genesis 37:18-36

Chonde tiyeni tiwerenge Genesis 37:23-28 ndipo tiimirire pamene tikuwerenga.

“Ndipo panali pamene Yosefe anafika kwa abale ake, anamvula Yosefe Malaya ake, Malaya a mwinjiro amene anabvala iye; ndipo anamtenga iye namponya mdzenje, mdzenjemo munalibe kanthu, munalibe madzi m’menemo. Ndipo iwo anakhala pansi kuti adye chakudya; ndipo anatukula manso ao, nayang’ana, ndipo taonani, ulendo wa Aismayele anachokera ku Giledi ndi ngamila zao, zirinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndi libano ali nkumuka kutsikira nazo ku Aigupto. Ndipo Yuda anati kwa abale ache, Nanga tidzapindulanji tikamupha mbale wathu ndi kufotsera mwazi wache? Tiyeni timgulitse iye kwa Aismayele, tisasamulire iye manja; chifukwa ndiye mbale wathu, thupi athu. Ndipo anamvera iye abale ake. Ndipo anapita pamenepo Amidyani amalonda: ndipo anamtulutsa namkweza Yosefe m’dzenjemo namgulitsa kwa Aismayele ndi ndalama za siliva makumi awiri; ndipo ananka naye Yosefe ku Aigupto” (Genesis 37:23-28)

Mukhonza kukhala.

Dr. Lin anati, “Kuona mtima, kumvera, kudekha, kukhulupirika, kukhazikika, kuonetsetsa, ndi nzeru sizipezeka m’moyo wofewa, koma popirira zokhoma ndi zotchinga. Yosefe sakadamalizitsa kukonzekera kukhala [wogonjetsa] akanangokhala pa nyumba. Kugulitsidwa pamtengo wa ma siliva khumi kukadapangitsa kuti anthu ambiri a dwale. Koma Yosefe sanatsutse, kapena kuwatemberera abale ake, chingakhale anali odabwa kuti maloto ake awiri angakwaniritsidwe bwanji kudzera m’mabvuto onsewa.

Mphepo Yaku M’mwera- Kutsimikizidwa ndi Kulimbikitsidwa -
Genesis 39:1-6

Chonde tsekulani pa Genesis 39:1-6.

“Ndipo anatsika naye Yosefe kunka ku Aigupto; ndipo Potifara, nduna ya Farao, Kazembe wa a londa, M’aigupto, anamgula iye m’manja mwa Aismayele amene anatsika naye kunka kumeneko. Ndipo Yehova anali ndi Yosefe; ndipo iye anali wolemera-lemera, nakhala mnyumba ya mbuyache M-aigupto. Ndipo mbuyache anaona kuti Yehova anamlemereza m’dzanja lache zonse anazichita. Ndipo Yosefe anapeza ufulu, ndipo anamtumikira iye; ndipo anamuyesa iye woyang’anira pa nyumba yache, nayika m’manja mwake zonse anali nazo. Ndipo panali chiyambire anamuyesa iye woyang’anira panyumba yache, ndi pazache zonse, Yehova anadalitsa nyumba ya M-aigupto chifukwa cha Yosefe; ndipo mdalitso wa Yehova unali pa zache zonse, m’nyumba ndi m’munda. Ndipo iye anasiya zache zonse m’manja a Yosefe: osadziwa chomwe analinacho, koma chakudya chimene anadya. Ndipo Yosefe anali wokoma thupi ndi wokongola.” (Genesis 39:1-6)

Taonani.

Yosefe anagulitsidwa kwa mkulu wa asirikari a Farao dzinalake Potifara. M’malo moti azidandaula, Yosefe amagwira bwino ntchito imene anapatsidwa. Potifara, bwana wake, anamukhulupirira kwambiri, ndipo anachita bwino kwambiri. Koma Yosefe anasoweka maphunziro ena. Ndipo Mulungu analolera kuti achititsidwe manyazi.

Mphepo ya kumpoto- Kukumana ndi mayesero ndi kusowa chilungamo.
Genesis 39:7-20

Tsopano imirirani pamene ndi kuwerenga Genesis 39:1-18. Dr. Lin anati, “Pamene mphepo yakumpoto iwomba m’miyoyo mwawo, achinyamata ambiri amaganiza kuti ndi ngozi… koma mabvuto ngati amenewa kumangokhala kuonetseredwa kwa chisomo cha Mulungu. Yeremiya anati, ‘Nkokoma kuti munthu asenze gori ali wamng’ono. (Maliro 3:27). Moyo wofewa opanda mabvuto ukhoza kuononga wachinyamata. Koma gori losenza uli wang’ono ndi popondera kupita gawo lina la pamwamba.

“Ndipo anatsika naye Yosefe kunka ku Aigupto; ndipo Potifara, nduna ya Farao, Kazembe wa a londa, M’aigupto, anamgula iye m’manja mwa Aismayele amene anatsika naye kunka kumeneko. Ndipo Yehova anali ndi Yosefe; ndipo iye anali wolemeralemera, nakhala mnyumba ya mbuyache M-aigupto. Ndipo mbuyache anaona kuti Yehova anamlemerereza m’dzanja lache zonse anazichita. Ndipo Yosefe anapeza ufulu, ndipo anamtumikira iye; ndipo anamuyesa iye woyang’anira pa nyumba yache, nayika m’manja mwake zonse anali nazo. Ndipo panali chiyambire anamuyesa iye woyang’anira panyumba yache, ndi pazache zonse, Yehova anadalitsa nyumba ya M-aigupto chifukwa cha Yosefe; ndipo mdalitso wa Yehova unali pa zache zonse, m’nyumba ndi m’munda. Ndipo iye anasiya zache zonse m’manja a Yosefe: osadziwa chomwe analinacho, koma chakudya chimene anadya. Ndipo Yosefe anali wokoma thupi ndi wokongola. Ndipo panali zitapita izi, kuti mkazi wa mbuyache anamyang’anira maso Yosefe: ndipo mkaziyo anati, Gona ndi ine. Koma iye anakana, nati kwa mkazi wa mbuyache, Taonani, mbuyanga sadziwa chimene chirindi ine m’nyumbamu, ndipo anayika zake zonse m’manja anga; mulibe wina mnyumba wamkuru ndine; ndipo sanandikaniza ine kanthu, koma iwe, chifukwa kuti uli mkazi wache: nanga ndikachita choipa chachikuru ichi bwanji ndikuchimwira Mulungu? Ndipo pali pakunenanena ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, iye sanamvera mkazi kugona naye kapena kukhala naye. Ndipo panali, nthawi yomweyo iye analowa, m’nyumba kuti agwire ntchito yache; ndipo munalibe amuna a m’nyumba m’katimo. Ndipo mkazi anagwira chofunda chache, nati, Gona ndi ine; ndipo anasiya chopfunda chache mdzanja lache nathawa, naturuka kubwalo. Ndipo panali pamene mkazi anaona kuti wasiya chofunda chache mdzanja lache, nathawa kubwalo, anaitana amuna a m’nyumba yake, nanene ndi iwo kuti; Taonani, walowetsa kwa ife Mhebri kuti atiseke ife. Analowa kwa ine kugona ndi ine, ndipo ndinafuula ndi mau akuru: ndipo panali pamenene iye anamva kuti ndinakweza mau anga ndi kufuula, iye anasiya chofunda chache kwa ine nathawira kubwalo. Ndipo anasunga chopfunda chache chikhale ndi iye kufikira atabwera kwao mbuyache. Ndipo ananena kwa iye monga mau awa, nati, Analowa kwa ine kapolo wa Chihebri uja, munabwera naye kwathu, kundipunza ine,:Ndipo panali pamene ndinakweza mau anga ndi kufuula, iye anasiya chobvala chache kwa ine, nathawira kunja”. (Genesis 39:1-18)

Mutha kukhala pansi.

Tsiku lina pamene Yosefe amagwira ntchito mnyumba ya Potifara, mkazi wake anayesa kumugwiririra kuti agone naye. Koma Yosefe anampulumuka, namusiyira chobvala chake m’manja mwake, ndipo anathawa.

Yesero iri anyamata ambiri akhonza kubvutika nalo kuligonjetsa kwake, koma Yosefe analigonjetsa. Analigonjetsa pochokapo msanga. Mayesero ena amagonjetsedwa pokumana nao, koma mayesero okhudzana ndi chigololo ndi chilakolako amagonjetsedwa pothawa (II Timoteo 2:22) amati, “Thawa chilakolako cha unyamata”). Chigonjetso cha Yosefe – kukhulupirika kwake- kwa Mulungu, kwa Potifara amene anamudalira kwa thunthu, ndi kwa iye mwini, kotero chiyero chake chinamusunga pakukhala wa ngwiro. Chifukwa cha Mulungu analolera kukalowa ku ukaidi kusiyana ndikukwaniritsa zilako lako za mkazi woyipayo. Chifukwa cha Potifara sanadzitchinjirize, kuopa kumuchititsa manyazi mkazi wa bwana wake. Kotero anakhala chete. Pamene Potifara anabwerera kunyumba anamvera zonene za mkazi wake, na muyika mkaidi Yosefe.

Mphepo ya ku m’mwera-Kukwezedwa ndi kukhala ndi abwenzi.
Genesis 39:21-40:22

Tsekulani Genesis 39:19-22. Imani pamene ndikuwerenga.

“Ndipo panali pamene mbuyache anamva mau a mkazi wache, amene ananena kwa iye, kuti, choterochi anandichitira ine kapolo wako kuti iye anapsya mtima. Ndipo mbuyache wa Yosefe anamtenga iye namuika mu m’kaidi, umo anamangidwa akaidi a mfumu; ndipo iye anali m’mwemo mkaidimo. Koma Yehova anali ndi Yosefe na mchitira iye zokoma, na mpatsa ufulu pamaso pa woyang'anira mkaidi. Ndipo woyang’anira kaidi anapereka m’manja a Yosefe akaidi onse okhala mkaidimo, ndipo zonse anazichita iwo m’menemo, iye ndiye wozichita.” Genesis 39:19-22.

Mukhoza ku khala.

Chingakhale kuthupi Yosefe zinthu zinkankira-nkira kuyipa, koma moyo wake wa uzimu sumasuntha. Ndipo Mulungu anapitiriza kumudalitsa chingakhale anali mu ukaidi.

Yosefe amatha kupeza abwenzi chingakhale anali mu ukaidi. Wopereka chikho wa mkulu wa Farao ndi wophika mkate wache, amene analinso mu ukaidi, ananzunzika ndi maloto. Panalibe wowatanthauzira malotowo. M’maganizo a Yosefe Mulungu amatha kuchitiramo china chirichonse. Anatanthauzira maloto a wopereka chikho wamkulu ndi wophika mkate. Patatha masiku atatu matanthauziro onse anakwaniritsidwa. Woperekera chikho anabwezeretsedwa, ndi wophika mkate ananyongedwa. Iyi inali mphepo yaku m’mwera yowomba pa Yosefe, chingakhale mu m’kaidi.

Mphepo ya ku Mpoto- Kupirira ku kusakumbukiridwa ndi kuchedwetsedwa.
Genesis 40:23

Taonani pa Genesis 40:23

“Koma woperekera chikho wamkulu sanakumbukira Yosefe, koma anamuiwala.” (Genesis 40:23)

Kupezeka kwa Yosefe mndende kwa zaka zina ziwiri inalidi mphepo yaku mpoto kwa iye. “Koma wopereka chikho wamkulu sanakumbukira Yosefe, koma anamuiwala” (Genesis 40:23). Izi zikuonetsa khalidwe losayamika la wopereka chikho. Mchitidwe ngati uwu ukhoza kupangitsa kuti munthu adane ndi dziko lapansi chifukwa cha kusayamikira kwake, koma Yosefe sanatero. Anaphunzira za kudikira pa Mulungu. Mulungu anatalitsira dala kukhala kwake mkaidi kuti Yosefe achuluke mchidziwitso cha kudikira pa Mulungu, komanso kuti azame mkudalira Mulungu. Kuchedwa kwa Mulungu ndi chizindikiro kuti amaonjezera chisomo kwa wogonjetsa. Kenaka Davide anati: “Yembekeza Yehova: Limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako: Inde yembekeza Yehova.” (Masalmo 27:14)

Mphepo yaku M’mwera- Kulamulira ngati Mfumu.
Genesis 47:12-31

Imani pamene ndi kuwerenga Genesis 47:12-17

“Ndipo Yosefe anachereza atate ake ndi abale ache, ndi mbumba yonse ya atate wache ndi chakudya monga mwa mabanja ao. Ndipo munalibe chakudwa m’dziko lonse; pakuti njala inalimba kwambiri; chifukwa chache dziko la Aigupto ndi dziko la Kenani linalefuka chifukwa njalayo. Ndipo Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse anazipeza mdziko la Aigupto ndi mdziko la Kanani, za tirigu amene anagula; ndipo Yosefe anapereka ndalama kunyumba ya Farao. Ndipo zitatha ndalama zonse mdziko la Aigupto ndi mdziko la Kanani, Aigupto onse anadza kwa Yosefe, nati, Mutipatse ife chakudya, tiferanji pamaso panu? Zatsirizika ndalama. Ndipo Yosefe anati, Mundipatse ng’ombe zanu: ndipo ndidzakupatsani inu mtengo wa ng’ombe zanu ngati ndalama zatsirizika. Ndipo anadza nazo ng’ombe zao kwa Yosefe, ndipo Yosefe anapatsa iwo chakudya chosinthana ndi akavalo, ndi nkhosa, ndi ng’ombe, ndi aburu; ndipo anawadyetsa iwo ndi chakudya chosinthana ndi zoweta zao zonse chaka chimenecho.” (Genesis 47:12-17)

Mutha kukhala.

Dr. Lin anati, “Palibe chilango chimene chimasangalatsa ukamachilandira; nthawi zonse chimakhala chowawa ndi chisasangalatsa. Koma chimabala chipatso cha chilungamo kwa iwo ozoloweretsedwa nacho. Tsekulani Ahebri 12:11.

“Chilango chirichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.” (Ahebri 12:11)

Taonani.

Pamapeto pa zaka ziwiri zimenezo, Mulungu anamulotetsa maloto Farao amene anapangitsa wopereka chikho wamkuru akumbukire Yosefe m’mene anatanthauzira maloto ake. Woperekera chikho anamuuza Farao kuti afunse Yosefe kuti atanthauzire maloto a Farao! Maloto anatanthauza kuti zaka zisanu ndi ziwiri za zochuluka ndi zaka zina zisanu ndi ziwiri za njara. Farao anasankha Yosefe kuti apange dongosolo lonse, ndi kukonzekera mzaka zisanu ndi ziwiri za njala. Farao anaona kuti Yosefe anaigwira ntchito nija modabwitsa. Kotero Yosefe anapangidwa kukhala mtsogoleri wa dziko la Aigupto (41:38-43). Yosefe analamulira Aigupto mwa nzeru ndi chidziwitso- ndipo analamulira abale ake mwa mwambo ndi chikondi. Mapeto ake Yosefe anapatsidwa ulemu kuposa abale ake onse (49:26).

Dr. Lin anati, Pamene Mulungu amamuphunzitsa Yosefe kuti atsogolere ufumu wa dziko lapansi, ndi chimodzimodzinso Mulungu akuphunzitsa ogonjetsa ake kuti akhale ndi ulamuliro mu Ufumu uli nkudza. Chipulumutso sichisoweka kuti uchite china chake, kutanthauza kuti palibe ntchito zomwe ziyenera kutsatilidwa. Koma kulamulira ndi Kristu mu Ufumu ulinkudza uyenera kuchita china chake.” Baibulo limati,

“Ngati tipirira tidzachitanso ufumu ndi Iye” (II Timoteo 2:12)

Mbusa Richard Wurmbrand anakhala mndende ya chi komonisiti akunzunzika zaka khumi ndi zinayi. Mbusa Warmbrand anati, “sindinaone Mkristu amene amakhalabe mchikhulupiriro atakumana ndi zowawa natulukamo opanda chirimbikitso.” Mau oyamba a buku lotchedwa “If Prison Walls Could Speak” (Zipupa za Ndende zikanatizimalankhula).

Komanso, Mbusa Wurmbrand anati, “Abale ndi alongo anga, muyenera kukhulupirira kuti miyoyo yathu iri ngati dothi m’manja a Mulungu. Salakwitsa pochita zinthu. Nthawi zina akakuumitsirani mtima…. Mungo khulupirira. Zindikira uthenga umene aku kuumbani nao. Ameni. (tsamba 16).

Mukakhala wogonjetsa ngati Yosefe, muli ndi lonjezano iri kuchoka kwa Mulungu. Tsekulani Chibvumbulutso 2:26.

“Ndipo iye amene alakika, ndi iye amene asunga ntchito zanga kufikira chitsiriziro, kwa iye ndidzapatsa ulamuliro wa pa a mitundu” (Chibvumbulutso 2:26”

Zikomo, a busa Timothy Lin, pakundiphunzitsa zimene tamva kuchoka mu chiphunzitso chanu. Zinasintha moyo wanga, abusa. Ndikupereka moyo wanga ku chiphunzitso chmenechi!

Chonde Imani ndi kuimba nyimbo yathu ya lero, “Ndine msirikali wa Mtanda?”

Ndine msirikali wa mtanda, Wotsatira Mwana wa Nkhosa;
Kodi ndidzaoa ku Mutsata, kapena kusiya kutchula dzina lake?

Kodi nditengedwe mlengalenga pa maluwa odekha,
Pomwe ena analimbana kuti alandire mphotho, nayandama mnyanja wa mwazi?

Kodi ndiribe adani oti ndi aope? Sindiyenera kusambira m’mafunde?
Kodi iri si dziko la nkhanza ndi bwenzi la chisomo, Kundi thandizira kwa Mulungu?

Nzoona ndiyenera kulimbana, ngati ndikuna kudzalamulira; onjezerani kulimba mtima kwanga, Ambuye!
Ndidzamva zowawa, ndikupirira, Mothandizidwa ndi Mau Anu.
(“Ndine Msirikari wa Mtanda?” ndi Dr. Isaac Watts, 1674-1748).

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

Ngati simunapumutsidwe, ndikufuna mu mudalire Yesu Kristu. Anadza kuchoka kumwamba kudzafera pa Mtanda kulipira mulandu wa tchimo lanu. Nthawi yomwe mutakhulupirire Yesu, mwazi Wake udzakuyeretsani kumachimo onse. Ndi pemphero langa kuti mumudalira Yesu.


MUKAFUNA KULEMBERA DR.HYMERS MUYENERA KUTCHULA DZIKO LIMENE MUKULEMERA APO AYI SADZATHA KUYANKHA KALATA YANU. Ngati maulaliki awa akudalitsani tumizani e-mail kwa Dr. Hymers ndikumuuza, koma nthawi zonse tchulani dziko limene mukulembera. E-mail ya Dr. Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net dafanyani apa. Mukhoza kumulembera Dr. Hymers mchilankhulo chirichonse, koma muyesetse Mchigerezi ngati mungathe. Ngati mukufuna kulembera Dr. Hymers pa positi, keyara yake ndi P.O. Box 15308, Los Angels, CA 9001. Mukhoza kuimba foni pa (818) 352-0452.

(MAPETO A ULALIKI)
Mukhoza kuwerenga ma ulaliki a Dr. Hymers sabata iriyose pa intaneti iyi
www.sermonsfortheworld.com,
dafanyani “Maulaliki mchichewa.”

Maulaliki awa si oletsedwa. Mukhoza kuagwiritsa ntchito kopanda kufuna chilorezo kwa
Dr. Hymers. Komabe, maulaliki a mkanema ya tchalitchi lathu ngofunika kuagwiritsa
ntchito potenga chilorezo