Print Sermon

Cholinga cha tsamba ili ndi kupereka ma ulaliki a ulere olembedwa komanso a mkanema kwa a busa mdziko lonse la pansi makamaka maiko okwera kumene, komwe kuli ma sukulu a Baibulo ochepa kapena kulibiretu.

Maulaliki awa olembedwa komanso a m’ma video akupezeka pafupifupi m’ma kompyuta 1,500,000 m’maiko 221chaka chilichonse pa www.sermonsfortheworld.com. Anthu zikwi-zikwi amaonera kanema wa pa YouTube, koma kenaka amasiya YouTube ndikubwera ku website yathu. You Tube imawalondolera anthu ku website yathu. Maulaliki olembedwawa akupezeka mzilankhulo 46 mu makomputa 120,000 mwezi uli wonse. Maulalikiwa alibe chiletso, kotero alaliki akhoza kuagwiritsa ntchito mosafuna chilolezo. Chonde sindikizani apa kuti mudziwe m’mene mungaperekere thandizo la mwezi ndi mwezi lomwe lingathandize kwakukulu pofalitsa uthenga wa bwino kudziko lonse la pansi.

Mukafuna kulembera Dr. Hymers nthawi zonse muuzeni dziko limene mukukhala, apo ayi sangakuyankheni. E-mail ya Dr.Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net.




KUFALITSA UTHENGA MWAMPHAMVU

THE EVANGELISM EXPLOSION
(Chichewa)

ndi Dr.R.L. Hymers Jr.

Uthenga wolalikidwa pa Chihema cha paBaptist ku Los Angeles
Usiku wa tsiku la a Mbuye, November 3, 2019
A sermon preached at the Baptist Tabernacle of Los Angeles
Lord’s Day Evening, November 3, 2019

“Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu; chiri mphatso ya Mulungu; chosachokera ku ntchito, kuti asadzitamandire munthu ali yense” (Aefeso 2:8,9)


Ndinabwera kumapemphero ku tchalitchi chathu usiku wa la chinayi chatha. Sindinalalikire kapena kutsogolera ma pemphero. Koma nditakhala ku mbuyo ndinakhudzidwa ndi mnyamata amene anali wotayika. Pa mapeto pa mapemphero ndinamupempha kuti adzakhale pafupi ndi ine pamene ena onse amatuluka.

Ndimawerenga za Kufalitsa uthenga mwamphamvu monga mwa kalongosoledwe ka Dr. D. James Kennedy. Ndipo ndinaganiza zogwiritsa ntchito njira imene Dr. Kennedy amanena za mnyamata ameneyu. Zimaoneka kuti zinali zophweka kwambiri kwa iyeyo. Chosecho wakhala akubwera ku tchalitchi kwathu moyo wake wonse. Wamvapo maulaliki ambiri. Nanga bwanji njira yophweka ya Dr. Kennedy inamupatsa chinachake chomwe wakhala akuchisowa pa mwamba pa maulaliki onse amane wamvapo kale? Koma pakuti chirichonse chimene tachinena sichinamuthandize kuti apulumutsidwe ndinaganiza kuti ndimupatse zomwe Dr. D. James analongosola.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

MA ULALIKI ATHU AKUPEZEKA MU MA FONI
ANU A M’MANJA TSOPANO.
PITANI KU WWW.SERMONSFORTHEWORLD.COM.
DAFANYANI BATANI LOBILIWIRA LOMWE LIRI NDI LIU LOTI “APP”
TSATIRANI MALANGIZO OTSATIRAWO.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

Ndinati kwa iye, “Utati wa mwalira usiku uno, ndikufika pamaso pa Mulungu pa chipata cha Kumwamba – ndi Mulungu nati kwa iwe, ‘Chimene ndingakubvomerezere iwe kulowa kumwamba ndi chiyani?’ Kodi ungayankhe chiyani kwa Mulungu?” Anakhala chete kwa mphindi zingapo. Kenaka anati, “Ndikhoza kumuuza kuti ndinali mnyamata wabwino.”

Aroma 6:23 amati, “Mphatso ya Mulungu ndiyo moyo wosatha.” Kumwamba ndi kwa ulere. Si kogwirira ntchito. Ndiye ndinati, “Kwazaka za mbiri inenso ndi maganiza ngati iweyo. Ndinayenera kukhala wabwino, kuti ‘ndidzipezere’ kumwamba.

Ndinalephera kukhulpirira zimene amanena. Ndipo ndinamufunsanso: “Mulungu akanati kwa iwe, Ndichifukwa chiyani ndingakulowetsere kumwamba?’ Kodi ukanamuyankha chiyani Mulungu?” Panthawi iyi nkuti misozi italengeza m’masomwake. Koma anapereka yakho lomwe lija, “ Ndakanatha kumuuza Mulungu kutit ndakha ndiri mnyamata wa bwino kuyambira pa ubwana wanga onse”. Uyutu ndi mnyamata wachisodzera amene takhala naye mtchalitchi moyo wake wonse- amakhala nao m’mapemphero onse a LaMulungu am’mawa ndi madzulo, komanso mapemphero a pakati pa sabata. Koma akuyankha mwachimvekere kuti amakhulupirira kuti chipulumutso chimadza pakuchita ntchito zabwino. Ndipo sakhulupirira Aefeso 2:8, 9!!!

Sindinamudzudzule. Ndinangonena kuti, “Mu mphindi zochepa ndikuuza uthenga wabwino kwambiri umene siunaumve ndi kalelomwe.” Ndinamuuza kuti ayang’ane Baibulo langa ndi kuwerenga yekha Aefeso 2:8,9.

“Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro; ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu; chosachokera kuntchito, kuti asadzikundikire munthu aliyense” (Aefeso 2:8;9).

Kenaka ndinati, “Tiyeni tiyang’anitsitse mau amenewa m’Baibulo.” Akuyamba ndikuti “pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo.” Chisomo ndi mphatso, “ndi mphatso ya Mulungu.” Kumwamba ndi mphatso – mphatso ya moyo wosatha. Kenaka ndinawerenga chigawo cha chiwiri cha Aroma 6:23, “mphatso ya Mulungu ndi moyo wosatha.” Kumwamba ndi mphatso ya ulere. Su ngachite kuyigwirira ntchito. Kenaka ndinanena kuti, “ Kwa zaka zambiri ndimaganiza ngati m’mene ukuganizira iwemu. Kuti ndinayenera kukhala munthu wa bwino, kuti ndipindule kumwamba. Kenaka ndinazindikira kuti Kumwamba ndi mphatso ya ulere – yaulere kotheratu! Ichi chinandidabwitsa! Baibulo limati, ‘Ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro – chosachokera mwa ntchito, asadzikundikire munthu’ (Aefeso 2:8,9).

Kenaka ndinamuuza kuti “pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerelo wa Mulungu” (Aroma 3:23). Tachimwa m’malakhulidwe, m’maganizo ndi muntchito. Palibe yense wa ife amene ndi wabwino kuti akafike kumwamba. Sitingakhale angwiro.

Koma Mulungu ndi wa chifundo. Safuna kutilanga. Komanso Mulungu ndi wa chilungamo kotero ayenera kulanga tchimo. Mulungu muchifundo chake anapeza njira. Mulungu anathana nalo bvuto limeneri potumiza Mwana Wake, Yesu, kutipulumutsa. Kodi Yesu ndani? Yesu ndi Mulungu-munthu. Monga mwa Baibulo, Yesu Khristu ndi Mulungu, munthu wa chiwiri mu uTatu. Ndipo Baibulo limanena kuti, “ndipo mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife” (Yohane 1:1,14). Yesu , Mulungu- munthu, anafera pa Mtanda ndi kuuka kwa akufa kulipira chilango cha machimo athu kutitengera moyo wosatha kuMwamba. Yesu anadzitengera machimo athu pa Iye, pamtanda. Khristu “ amene anasenza machimo athu mwini yekha” (1 Petro 2:24 ). Anaikidwa m’manda kwa masiku atatu. Koma anauka kwa akufa ndi kukwera Kumwamba, kukatikonzera malo. Tsopano Yesu akupereka moyo wosatha wa Kumwamba – kwa ife kwa ulere. Kodi timalandira bwanji? Timalandira chaulere chimenechi mwachikhulupiriro! “Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhullupiriro” (Aefeso 2:8)

Chikhulupiriro mwa Yesu chimatsekula khomo la Kumwamba. Chikhulupiriro si kuchita zinthu mwa nzeru kokha. Chingakhale Satana ndi ziwanda amakhulupirira mu uMulungu wa Yesu. Koma sanapulumutsidwe. Chikhulupiriro si kungokhala ndi zinthu m’moyo uno – monga moyo wa thanzi, chitetezo ndi tsogolo labwino – zinthu za m’moyo uno zonse zidzapita.

Chikhulupiriro, malinga ndi Baibulo, ndi kudalira Yesu yekha. Khristu anadza kuti atitengere kumwamba, kuti tikakhale ndi moyo wosatha! Baibulo limati, “Khulupirirani Yesu Khristu Ambuye, ndipo mudzapulumutsidwa” (Machitidwe 16:31).

Anthu amadalira chimodzi mwa zinthu ziwiri- amadzidalira iwo wokha kapena Yesu Khristu. Ine kale ndimadalira kuyesetsa kwanga kukhala moyo wabwino. Kenaka ndinazindikira kuti ndiyenera kusiya kudzidalira, ndikuyamba kudalira Yesu. Ndinachitadi izi- ndipo Yesu anandipatsa mphatso ya moyo wosatha. Inali mphatso, “osati chifukwa cha ntchito zanga.”

Ndikupatse chitsanzo pa mpando uwu. Kodi ukukhulupirira kuti ukhonza kukhala pa mpando uwu osagwa? (inde).

Pano mpandowu sukundithandiza chifukwa sindinakhalepo. Ndingatsimikize bwanji kuti ndikudaliradi mpando? Chabwino, ndiyenera kukhalapo!

Umu ndi m’mene muyenera kuchitira ndi Yesu. Muyenera kudalira Iye kuti akulowetseni kumwamba. Ukunena kuti Udzamuuza Mulungu kuti unali mnyamata wabwino.” Ndani munthu yekha amene anali muyankho lako? (iwe).

Ndani amene umadalira kuti akakulowetsa kumwamba pamene umanena zimenezi? (Nzoonadi ndiwe)

Kuti ulandire moyo wosatha uyenera kusiya kudzidalira ndi kuyamba kudalira Yesu. ( Khala pa mpando)

Kodi izi ndi za nzeru? Tsopano funso limene Mulungu akufunsa ndi lakuti “ Kodi ukufuna kulandira mphatso ya moyo wosatha tsopano?” (Inde , ndikufuna).

Ndipemphera tsopano, “Ndikupemphera kuti mumupatse mzangayu mphatso ya moyo wosatha tsopano.”

Tsopano, Yesu ali pano, ndipo akhonza kumva. Ndikufuna umuuze Yesu ngati ufunadi moyo wosatha. Unditsatire mau nditanenewa, koma umuuze Yesu.,

“Yesu, ndikufuna kudalira inu tsopano. Ndine wochimwa. Ndakhala ndikudzidalira ndi ubwino wanga. Tsopano ndikufuna kudalira inu, Ambuye Yesu. Ndikudalirani tsopano. Ndikukhulipirira kuti munafa kulipira machimo anga. Tsopano ndikudalira Inu, Yesu. Ndikuchokako ku kudzikonda kwanga ndi machimo anga. Ndikudalirani. Ndikubvomera mphatso ya ulere ya moyo wosatha. Mdzina lanu Yesu. Ameni.”

Tsopano ndikupempherera. “Yesu, mwamva pemphero limene mzangayu wapemphera. Ndikupemphera kuti amve mumtima mwake, mau anu akunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa’ Iye wodalira ine sadzatayika, koma adzakhala nawo moyo wosatha.” M’dzina la Yesu ndapemphera, Amen.”

Tsopano ndikufuna uwerenge Yohane 6:47 mokweza.

“Ndinena kwa iwe, wakukhulupirira ine ali ndi moyo woaatha.”

Osayang’ana za m’mene umadzimvera. Ndi chikhulupiriro chaching’ono chabe, dalirani Yesu Khristu.

Ukudalira yani tsopano woti angakupumutse? (Yesu Khristu).

Chikhulupiriro chopulumutsa chimatanthauza kudalira Yesu pa moyo wosatha. Kodi izi ndi zimene wangochita tsopano? (Inde)

Yesu akuti aliyense wochita ichi ali ndi moyo wosatha. Kodi ichi ndi chimene wangochita? (inde)

Tsopano ngati utamwalira usiku uno ndipo Mulungu ndi kukufunsa kuti nchifukwa chiyani angakulowetsere kuMwamba, kodi unganene chiyani? (Ndikudalira Yesu kundipatsa moyo wosatha)

.

Mbale, ngati umatsimikizadi wangopemphera posachedwa zija, Yesu wakukhulurikira kale ku machimo ako, ndipo uli ndi moyo wosatha tsopano!

Ndikufuna kuti uwerenge uthenga wabwino wa Yohane, chaputala chimodzi pa tsiku, uwona kuti pa ma sabata atatu okha uwerenga uthenga wabwino wa Yohane yense.

Ndifuna kuti umuuze munthu m’modzi pa zomwe zakuchitikira usku uno. Munthu ameneyu angakhale ndani? (Mbale wanga)

Kodi ukamuuza kuti wasankha kudalira Yesu madzulo ano? (eya)

Tsopano, ndikanakonda kuti laMulungu likubwerali ndidzakutenge kuti tidzapitire limodzi kutchalitchi. Kodi tikhonza kutero?(inde) Ngati ufuna kulankhula nane undiyimbire.Nambala yanga ndi iyi.

Tsopano, kwa kanthawi kochepa, tiyemi timuthokoze Yesu pa kupulumutsa moyo wako ndikukupatsa moyo wosatha? (Tipemphere).

Tsopano, Ndkufuna uwerenge Aefeso 2:8, 9.

“Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu; chiri mphatso ya Mulungu; chosachokera ku ntchito, kuti asadzitamandire munthu ali yense” (Aefeso 2:8,9).

Kumbukirani kuti mazana-mazana a wanthu mdziko lonse lapansi atembenuka mtima chifukwa cha ulaliki wapafupi umenewu. Chingakhale samvetsetsa zimene zinachitika, malizani kukumana ndi kumwetulira ndipo muonetsetse kuti alonjeza kuwerenga uthenga wabwino wa Yohane chaputala chimodzi pa tsiku. Mudzakhalanso ndi mwayi wolankhulana naonso.

Tengani uthengawu popita kunyumba, muzikawerengani mpaka mutaloweza. Kaulalikireni kwa abale anu mosakhalitsa. Mudzadabwa kuti adzasangalala nao kenaka ndikuyamba kukutsani ku tchalitchi!


MUKAFUNA KULEMBERA DR.HYMERS MUYENERA KUTCHULA DZIKO LIMENE MUKULEMERA APO AYI SADZATHA KUYANKHA KALATA YANU. Ngati maulaliki awa akudalitsani tumizani e-mail kwa Dr. Hymers ndikumuuza, koma nthawi zonse tchulani dziko limene mukulembera. E-mail ya Dr. Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net dafanyani apa. Mukhoza kumulembera Dr. Hymers mchilankhulo chirichonse, koma muyesetse Mchigerezi ngati mungathe. Ngati mukufuna kulembera Dr. Hymers pa positi, keyara yake ndi P.O. Box 15308, Los Angels, CA 9001. Mukhoza kuimba foni pa (818) 352-0452.

(MAPETO A ULALIKI)
Mukhoza kuwerenga ma ulaliki a Dr. Hymers sabata iriyose pa intaneti iyi
www.sermonsfortheworld.com,
dafanyani “Maulaliki mchichewa.”

Maulaliki awa si oletsedwa. Mukhoza kuagwiritsa ntchito kopanda kufuna chilorezo kwa
Dr. Hymers. Komabe, maulaliki a mkanema ya tchalitchi lathu ngofunika kuagwiritsa
ntchito potenga chilorezo