Print Sermon

Cholinga cha tsamba ili ndi kupereka ma ulaliki a ulere olembedwa komanso a mkanema kwa a busa mdziko lonse la pansi makamaka maiko okwera kumene, komwe kuli ma sukulu a Baibulo ochepa kapena kulibiretu.

Maulaliki awa olembedwa komanso a m’ma video akupezeka pafupifupi m’ma kompyuta 1,500,000 m’maiko 221chaka chilichonse pa www.sermonsfortheworld.com. Anthu zikwi-zikwi amaonera kanema wa pa YouTube, koma kenaka amasiya YouTube ndikubwera ku website yathu. You Tube imawalondolera anthu ku website yathu. Maulaliki olembedwawa akupezeka mzilankhulo 46 mu makomputa 120,000 mwezi uli wonse. Maulalikiwa alibe chiletso, kotero alaliki akhoza kuagwiritsa ntchito mosafuna chilolezo. Chonde sindikizani apa kuti mudziwe m’mene mungaperekere thandizo la mwezi ndi mwezi lomwe lingathandize kwakukulu pofalitsa uthenga wa bwino kudziko lonse la pansi.

Mukafuna kulembera Dr. Hymers nthawi zonse muuzeni dziko limene mukukhala, apo ayi sangakuyankheni. E-mail ya Dr.Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net.




KUONETSEREDWA KWA CHIDUTWA CHA UNENERI WOSIIDWA MASIKU ANO

A MISSING PIECE OF BIBLE PROPHECY
ILLUMINATED FOR US TODAY
(Chichewa)

ndi Dr. R.L. Hymers, Jr.

Uthenga wolalikidwa ndi Dr. R. L. Hymers, Jr. pa Chihema cha Baptist
ku Los Angeles Madzulo a tsiku la Ambuye Septermber 22, 2019
A sermon preached at the Baptist Tabernacle of Los Angeles
Lord’s Day Evening, September 22, 2019

“Koma iwe Danieli tsekera mau awa, nukomere chizindikilo buku, mpaka nthawi ya chimariziro….” (Danieli 12:4; tsamba 792).

“Ndinachimva ichi koma osazindikira; pamenepo ndinati Mbuye wanga, chizindikiro cha izi ndi chiyani? Ndipo anati, Pita Danieli; pakuti mauwo atsekedwa, nakomeredwa chizindikilo mpaka nthawi ya chitsiriziro.” (Danieli 12:8, 9; tsamba 792).


Mneneri Daniel sanamvetsetsa tsatane-tsatane wa “nthawi zomalizira” tauzidwa mwachimvekere pa vesi 8, “Ndinachimva ichi koma osazindikira.” Kenaka Mulungu anauza Danieli, “mauwo atsekeredwa, nakomeredwa chizindikiro mpaka nthawi ya chimariziro.” (Danieli 12:9).

Danieli anamvetsetsa za mau a uneneri. Koma sanazindikire m’mene zinthu zidzakhalire m’nthawi yomaliza. Pakuti mauwo atsekeredwa, nakomeredwa chizindikiro mpaka nthawi ya chimaliziro.” (Danieli 12: 9). Anapatsidwa mau mwa bvumbulutso. Koma tanthauzo lake sili nalongosoledwe. Kulongosola kwa mau sikunachitike “kufikira nthawi yomaliza”. Pamene tikuyandikira mapeto a m’badwo uno, kuzindikira kwa ma uneneri kudzaonjezereka.

Ndikutha kukumbukira bwino lomwe nthawi yoyamba pamene ndinamva za “mkwatulo.” Aphunzitsi anga anatiuza kuti mkwatulo udzachitiza zisanafike zaka zisanu ndi ziwiri za chimsautso. Ndinawafunsa aphunzitsi angawo kuti izi zinaphunzitsidwa pati m’Baibulo zoti mkwatulo udzachitika chisanafike chisautso. Sanathe kundiyankha. Ndi m’mene, kwazaka zambiri ndakhala ndikufunsa za “nthawi ina ili yonse” mkwatulo, wa zaka zisanu ndi ziwiri usanachitike. Ndiye ndinazindikira kuti zoti mkwatulo udzachitika chisautso chisanadze anayambitsa ndi J.N. Darby, ndikuti Darby “anachitenga” kuchoka kwa mtsikana wa zaka khumi ndi zisanu wotchedwa Margaret MacDonald, wa chi kalazimatiki amene anachita ku zi “lota.” Kenaka J.N. Darby anayamba kuzilankhula pazifukwa zodziwa yekha. Kenakanso zinayamba kunenedwa ndi C.I. Scofield mu Baibulo lo thirira ndemanga la Scofield. Anthu ambiri achigwira chimenechi tsopano.

Kenaka Marvin J. Rosenthal analemba buku lotchedwa The Pre-Wrath Rapture of the Church (Thomas Nelson, 1990). Chingakhale sindigwirizana ndi zonse zimene Rosenthal analemba, ndikukhulupirira kuti anatsekula khomo la kamvetsedwe kabwino ka nthawi imene “mkwatulo” udzachitikire. Mukhale nalo buku limeneri ndi kuliwerenga musanatsutse maganizo a m’busa Rosenthal. Amaphunzitsa kuti “mkwatulo” udzachitika kufupi ndi kumapeto kwa chimsautso, patangotsala pang’ono kuti Mulungu apungulire mkwiyo Wake pa “mbale za chiweruzo” za pa Chibvumbulutso, mutu wa 16. APa zikumveka zosiyana ndi zimene zidakhazikika pa maloto a kamtsikana zija!

Kodi ichi ndi chofunikira bwanji? Ndikuuzani chifukwa. Ngati mkwatulo utabwera isanafike nthawi ya zaka zisanu ndi ziwiri za mkwatulo, ndiye kuti a Khristu sakuyenera kuchita chirichonse. Kungopita kutchalitchi ndi gulu pa ola limodzi m’mawa wa la Mulungu! Osalalikira kuti anthu apulumutsike. Osadzipatula ku za dziko. Izi zimalimbikitsa chiphunzitso cha Kusasunga chilamulo (dafanyani apa kuti muwerenge za izi).

Mutu wa uthenga uwu ndi “ Kuonetseredwa kwa chidutwa cha uneneri wa m’Baibulo wosiyidwa kwa ife “ Kodi” chidutwa “chosiyidwa” chimenechi ndi chiti? Ndi “wosiya chikhulupiriro.” Ndakhala ndi kusanthula za ma uneneri a Mbaibulo kwa zaka zoposa 50. Zimandikhudza kuti chiphunzitso cha anthu onyoza chikhulipiriro sichikuphunzitsidwa m’masiku athu ano. Pa gome langa pali mabuku atatu a za uneneri – amene akhudza mbali zofunikira zonse za chiphunzitso cha uneneri. Analembedwa ndi anthu abwino a Mulungu, anthu odalirika pa chiphunzitso chimenechi. Koma palibe ndi m’modzi yemwe amane ali ndi mutu wa “osiya chikhulupiriro chapoyamba” Zosiya chikhulupiriro cha poyamba ndi zimene zikuchitikira anthu ambiri m’masiku anthu ano.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

MA ULALIKI ATHU AKUPEZEKA MU MA FONI
ANU A M’MANJA TSOPANO.
PITANI KU WWW.SERMONSFORTHEWORLD.COM.
DAFANYANI BATANI LOBILIWIRA LOMWE LIRI NDI LIU LOTI “APP”
TSATIRANI MALANGIZO OTSATIRAWO.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

Chonde tsekulani II Atesaonika 2:3.

“Munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma chiyambe chifike chipatukocho, nabvumbulutsike munthu wosayeruzika, mwana wa chionongeko” (II Atesalonika 2:3; tsamba 214 Buku lopatulika ndio Mau a Mulungu)

Mu Chichewa china vesi ili likuti,

“Wina asakunyengeni konse, kuti silifika, koma chiyambe chifike chipatukocho, nabvumbuluke munthu wonyozayo, mwana wa chionongeko” (II Atesalonika 2:3, Chichewa chatsopano)

“Wotayachikhulupiriro cha poyamba” zitanthauzanso kuti “wakugwa” m’chichewa cha kale

.

Dr. W.A. Criswell anapeza maphunziro ake a Ph. D. mu kalongosoledwe ka chi Greek kuchoka ku Southern Baptist Theological Seminary ku Louisvaille, Kentucky. Dr. Criswell amasamalitsa kwambiri ku mau a chi Greek a m’chipangano chatsopano. Dr. Criswell anati, “ lisanafike tsiku la Ambuye, kudzakha kubwerera mbuyo kwa okhulupirira achinyengo. Pogwiritsa ntchito liu loti [iye] ndiye kuti Paulo ali ndi munthu wokana Khristu m’mutu mwake.” Podziwa ichi tikuphunzira zinthu ziwiri kuchoka pa II Atesalonika 2:3,


1.  Lisanafike tsiku la Ambuye, wokana Khristu ameneyu adzatenga malo

2.  Lisanafike tsiku la Ambuye, wokana Khristu adza “vumbulitsidwa”


Zinthu ziwiri zonsezi zidzachitika lisanafike tsiku la Ambuye, chomwe ndi chisautso ndi nthawi ya mkwiyo wa Mulungu, kumapeto a mbadwo uno. Mkwatulo chisanafike chinzuzowu aKristu adzakhala atapita kale. Ndi chifukwa chake za okana chikhulupiriro sizikulalikidwa m’matchalitchi ambiri masiku ano, ndipo ndichifukwa chake mulibe mitu yophunzitsa zimenezi mu mabuku a uneneri ambiri masiku ano!

Koma ngati Marvin Rosenthal akunena zoona, ndiye kuti tayamba nthawi ya “ otayachikhulupiriro” panopa! Kodi izi ziakhudza bwanji a Kristu masiku ano? “M’maiko ongokwera kumene” muli anthu ambiri amene akunzunzika kuposa nthawi ina iri yonse mbuyomu. Koma “ kumaiko a azungu” kuno tikunzunzika kwambiri ndi Satana ndi ziwanda zake. Mneneri Daniel anauzidwiratu za zinthu izi, koma anati, “ Sindinazindikire” Ndipo Mulungu anati kwa Daniel, “Pakuti mauwo atsekeredwa, nakhomeredwa chizindikilo mpaka nthawi ya chitsiriziro” (Daniel 12: 8,9).

John S. Dickerson analemba buku labwinoko lotchedwa, “The Great Evangelical Recession (Baker Book, 2013). Dickerson akulemba zimene Gabe Lyons ananena,

Nthawi ino ndiyosiyana ndi nthawi ina iliyonse mu mbiri. Kusiyana kwake kufunika kuti kulonosoledwe bwino. Ngati sitingathe kupeza njira ina ya m’mene tingapititsire zinthu patsogolo, ndiye kuti [tidzataya] mbadyo wonse mu mpungwepungwe, adzayamba kutembenukira [ku] zipembedzo zina za chilendo…..zidzachitika mkanthawi kochepa, koma yochita zazikulu. (The Next Christians, Doubleday, 2010, p. 11; zowonjezera ndi zanga.)

Chikutiro cha buku la Dickerson chimati

Mpingo wa ku Amereka wayamba… kunyentchera. Achinyamata ayamba kuthawa m’mipingo. Chopereka kumpingo chayamba kuphwera…. Chikhalidwe cha United States chayamba kuopseza ndiku tayika mwamsanga. Kodi tingateteze bwanji kuti izi ziyipiretu?”

Chingakhale ndikugwirizana ndi gawo loyamba la buku la Dickerson, ndikutsutsana ndi zambiri mgawo la chiwiri la bukuli, makamaka pa za kukonzekera.

Pa kukonzekera tiyenera kudziwa kuti nthawi yake ndi ino, panopa, pamene tiripa chiyambi cha “onyoza.” Ngati tikuganiza kuti mkwatulo uchitika tikanzunzika kwambiri, ndiye kuti sitingakonzekere pa zomwe zili nkudza.

Mbusa Richard Wurmbrand anali mlaliki wa chivangeli amene anakha mndende ya chikomunisiti, ananzunzika chifukwa cha Kristu ku Romania. Kunzunzika kumene anakumana nako mndende, ndikoposa kunzunzika kumene a Kristu ena a ku Amereka anakumananako. Makoswe amaluma zala zake usiku onse. Amamenyedwa. Amamuotcha ndi mawaya amoto zomwe zimamusiya ndi matuza mthupi lake lonse. Ananzunzika mpaka pafupi kufa. Manzunzo awa anachitika kwa zaka 14. Izi zinapangitsa kuti Mbusa Wurmbrand akonze chiphunzitso cha “Kanzunzikidwe” ichi ndi chiphunziso cha kunzunzika. Atabwerera ku Amereka (mozizwitsa) anaphunzitsa za kukonzekera manzunzo m’ma tchalitchi ambiri – kuphatikiza tchalitchi lathu. Anati, “tiyenera kukonzekera tsopano, tisanamangidwe. Mndende umataya chilichonse… palibe chimene umakhala nacho chokometsera moyo. Palibe amene amalimba ngati sanayambe wakana kale zosangalatsa moyo uno nthawi isanafike” (zofotokozeredwa ndi John Piper mbuku lake lotchedwa Let the Nation Be Glad, Baker Books, 2020, tsamba. 10).

Dr. Paul Nyquist anati, “Konzekani. Monga m’mene kusintha kwa chikhalidwe kwabwerera mdziko lathu, tirimbikitsidwe ndi zimene Baibulo likunena… zokhudzana ndi chinzunzo” (J. Paul Nyguist, Prepare: Living your Faith in an Increasingly Hostile Culture, Moody Publishers, 2015, tsamba 14.)

M’MASIKU A NOWA NDI MASIKU OTAYA CHIKHULUPIRIRO

Yesu anati,

“Ndipo monga masiku a [Nowa] kotero kudzakhala kufika kwake kwa mwana wa munthu. Pakuti monga m’masiku aja, chisanafike chigumula, anthu anali nkudya ndi kumwa,anali kukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene [Nowa] analowa m’chingalawa, ndipo iwo sanadziwa kanthu, kufikira pamene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo wonse, kotero kudzakhala kufika kwache kwa Mwana wa munthu.” (Mateyu 24:37-39; tsamba 31).

Ma evangeliko ambiri amaganiza kuti mu nthawi ya Nowa kunali msautso wa ukulu. Koma kunali zambiri. Anthu M’masiku a Nowa a “madya ndi kumwa, kukwatira ndi ku kwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa mchingalawa” (Matayu 24:38).

Izi ndi zeni-zeni zimene zikuchitika ku Amereka ndi maiko ena onse olemera! Ku maiko “ongokwera” kumene kuli kunzunzika kwambiri. Kumaiko monga China kuli chitsitsimutso cheni-cheni. Koma osati ku Amereka ndi maiko ena olemera! Maiko amenewa anthu amangolabadira za chuma. Amadya ndi kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa. Izi zikuonneka kuti ndi m’mene ziyenera kukhalira nthawi zonse. Komatu pali zambiri kuseri kwake. Muzinthu izi ndi m’mene miyoyo yawo yakhazikikamo – “kudya ndi kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa.” Ankaganiza kuti moyo ndiye umenewo! Mitima yawo si inakhazikike pa Mulungu! Kudzikunsikira chuma ndi pamene anakhazikika m’moyo mwao!

MPINGO WA KU LAODIKAYA NDI CHITHUNZI-THUNZI CHA MPINGO WA KU AMEREKA NDI MAIKO ENA ULEMERA.

Yesu anati,

“Ndipo kwa mgelo wa Mpingo wa ku Laodikaya lemba; Izi anena Ameni’yo, mboni yokhulupirika ndi yoona, woyamba wa chilengo cha Mulungu: Ndidziwa ntchito zako, kuti suli wozizira kapena wotentha: mwezi utakhala wo zizira kapena wotentha. Kotero popeza uli wofunda, wosati wotentha kapena wozizira, ndidzakulavula mkamwa mwanga. Chiukwa unena kuti ine ndine wolemera ndipo chuma ndiri nacho, osasowa kanthu; ndipo sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa; ndikulangiza ugule kwa Ine golidi woyengeka m’moto, kuti ukakhale wachuma, ndi zobvala zoyera, kuti ukadziveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m’maso mwako, kuti ukaone. Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.” (Chibvumbulutso 3:14-19; tsamba 252)

Ichi ndi chithunzi-thunzi cha mpingo wa otayachikhulupiriro. Ndi mpingo wofunda, “ siwozizira kapena wotenda. (Chibvumbulutso 3:16). Ndi mpingo wodzaza ndi anthu osatembenuka (Chibvumbulutso 3:19).

Taonapo mipatuko iwiri mzaka 40. M’mipatuko yonseyi amachita ndi anthu amene amafuna kukhala “wofunda” ndi a menene anatisiya. Onsewo anali wofunda pa kulalika. Onsewo anakana chi Kristu chenicheni. Chimene anachiona mwa ife chimene chinawapangitsa kuti atuluke ndi chakuti ife “timasamalitsa kwambiri” kutsata zimene Baibulo likunena. Ndipo amaganiza kuti akachoka “akasagalala”. Koma nthawi zonsezi amalephera kukhala ndi mpingo “wa moto” Anadzazindikira mochedwa kuti ngakhale anthu awo sakanatha kukhala pa malo ofunda. Pamapeto pake analephera. Yesu anati, “ndidzakulabvula [kusanza] mkamwa mwanga” (Chivumbulutso 3:16). Samafuna kuchokako pa za mdziko lapansi, kotero anamezedwa ndi zochitika za pa dziko la pansi, thupi, ndi satana. Sanafuna kuchilimika, zotsatira zake, anafunda, mu uzimu anayamba kuzirala!

Dzifunseni. Anthu amene anachoka ndi Chan akadakhala a ku China, kodi akanapitiriiza kupemphera mobisala, kapena akanapita ku tchalitchi lothandizidwa ndi boma? yankho mulinalo nokha! Ndipo yankho munalidziwa kale! Akanathawira ku mpingo wa chikomonisiti. Chifukwa? Chifukwa safuna chi Kristu cheni-cheni. Pakamwa pao pamangofuna uthenga wofewa. Uwu ndi uthenga wa otaya chikhulupiriro Chan! Mukudziwa ichi! Mumadziwa kale ichi!! Sindikukuuzani chiphunzitso cha chilendo!!!

Ndikufuna kumaliza uthengawu ndi kulongosola za otaya chikhuupiriro mu matchalitchi a chivangeli m’masiku ano,

“Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndarama, odzitamandira , odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudiyerekeza, osakhoza kudziretsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma, olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yache adaikana; kwa iwonso udzipatule.” (II Timoteo 3: 1-5; tsamba 220)

“Ophunzira nthawi zonse, koma sakhoza konse kufikira ku chizindikiritso cha choonadi. (II Timoteo 3: 7; tsamba 220).

“Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Kristu Yesu, adzamva manzunzo. (II Timoteo 3: 12; Tsamba 220).

“Lalikira mau; chita nao pa nthawi yache, popanda nthawi yache, tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndikuleza mtima konse ndi chiphunzitso. Pakuti idzafika nthawi imene sadzalola chiphunzitso cholamitsa; komatu poyambwa m’khutu adzadziunjikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha; ndipo adzalubza dala pachoonadi, nadzapatukira kutsata nthano za chabe. Koma iwe khala maso m’zonse, imva zowawa, chita ntchito ya ulaliki wa Uthenga Wabwino, kwaniritsa utumiki wako. (II Timoteo 4:2-5; tsamba 220)

“Pakuti Dema wandisiya ine, atakonda dziko lino lapansi” (II Timoteo 4:10; tsamba220)

“Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang’anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zopunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo. Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Kristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika osocheretsa mitima ya osalakwa.” (Aroma 16:17,18; tsamba 172)

Okondedwa abale ndi alongo, mneneri wamkulu Daniel sanamvetsetse za zinthu zimene ndalalikira madzulo anozi. Koma tiyamika Ambuye wadzutsa wa mishoni dzina lake Marvin Rosenthal kuti alankhule ndi kutipatsa “ kamvetsedwe katsopano ka mkwatulo. Chisautso chachikulu ndi Kubweranso kachiwiri” ka Yesu ( kunja kwa buku la The Pre-Wrath Rapture of the Church, Thomas Nelson, 1990)

Inde, tiri koyambirira kwa nthawi ya onyenga. Inde tiyenera kulowa mchisautso, monga anthu a ku China. Monga Richard Wurmbrand anachitira, monga anthu amene ali mu “maiko okwera kumene”. Koma amene amakonda Kristu adzasangalala kumapeto kwake, pakuti Yesu anati,

“Popeza unasunga mau a chiramulo changa, Inenso ndidzakusunga kukulanditsa mu nthawi ya kuyesedwa, ikudza pa dziko la lonse la pansi, kudzayesa iwo akukhala padziko. Ndidza msanga; gwira chimene uli nacho, kuti wina angalande korona wako. Iye wakulakika, ndidamuyesa iye mzati wa mKachisi wa Mulungu wanga, ndipo kutuluka sadzatulukamonso; ndipo ndidzalemba dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, la Yerusalemu watsopano, wotsika m’Mwamba, kuchokera kwa Mulungu wanga; ndi dzina langa la tsopano. Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.” (Chibvumbulutso 3:10-13; tsamba 252)

Chonde imani kuti muyimbe ndime 1,2, ndi 4 ya “Kodi Ndine Msilikali wa Mtanda?”

Ndine Msilikali wa mtanda, Wotsatira wa mwana wa nkhosa,
Kodi Ndidzaopa kutchedwa ndi dzina Lake, kapena kukhala chete pakutcula dzina Lake?

Kodi ndidzatengedwa mlengalenga kuthawa mabvuto,
Pomwe ena akumenya nkhondo pansi pano? Nasamba m’mitsinje ya magazi?

Ndiyenera kumenya nkhondo, kuti ndiramulire; Onjezani kulimba mtima kwanga Ambuye;
Ndidzasenza chitonzo, ndikupira zowawa, polimbitsidwa ndi Mau Anu.
   (“Kodi Ndine Msilikali wa Mtanda?” Nyimbo ya Dr. Isaac Watts, 1674-1748).


MUKAFUNA KULEMBERA DR.HYMERS MUYENERA KUTCHULA DZIKO LIMENE MUKULEMERA APO AYI SADZATHA KUYANKHA KALATA YANU. Ngati maulaliki awa akudalitsani tumizani e-mail kwa Dr. Hymers ndikumuuza, koma nthawi zonse tchulani dziko limene mukulembera. E-mail ya Dr. Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net dafanyani apa. Mukhoza kumulembera Dr. Hymers mchilankhulo chirichonse, koma muyesetse Mchigerezi ngati mungathe. Ngati mukufuna kulembera Dr. Hymers pa positi, keyara yake ndi P.O. Box 15308, Los Angels, CA 9001. Mukhoza kuimba foni pa (818) 352-0452.

(MAPETO A ULALIKI)
Mukhoza kuwerenga ma ulaliki a Dr. Hymers sabata iriyose pa intaneti iyi
www.sermonsfortheworld.com,
dafanyani “Maulaliki mchichewa.”

Maulaliki awa si oletsedwa. Mukhoza kuagwiritsa ntchito kopanda kufuna chilorezo kwa
Dr. Hymers. Komabe, maulaliki a mkanema ya tchalitchi lathu ngofunika kuagwiritsa
ntchito potenga chilorezo