Print Sermon

Cholinga cha tsamba ili ndi kupereka ma ulaliki a ulere olembedwa komanso a mkanema kwa a busa mdziko lonse la pansi makamaka maiko okwera kumene, komwe kuli ma sukulu a Baibulo ochepa kapena kulibiretu.

Maulaliki awa olembedwa komanso a m’ma video akupezeka pafupifupi m’ma kompyuta 1,500,000 m’maiko 221chaka chilichonse pa www.sermonsfortheworld.com. Anthu zikwi-zikwi amaonera kanema wa pa YouTube, koma kenaka amasiya YouTube ndikubwera ku website yathu. You Tube imawalondolera anthu ku website yathu. Maulaliki olembedwawa akupezeka mzilankhulo 46 mu makomputa 120,000 mwezi uli wonse. Maulalikiwa alibe chiletso, kotero alaliki akhoza kuagwiritsa ntchito mosafuna chilolezo. Chonde sindikizani apa kuti mudziwe m’mene mungaperekere thandizo la mwezi ndi mwezi lomwe lingathandize kwakukulu pofalitsa uthenga wa bwino kudziko lonse la pansi.

Mukafuna kulembera Dr. Hymers nthawi zonse muuzeni dziko limene mukukhala, apo ayi sangakuyankheni. E-mail ya Dr.Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net.




M’MENE PETRO ANAKHALIRA WOPHUNZIRA

HOW PETER BECAME A DISCIPLE
(Chichewa)

Wolemba ndi Dr. Christopher L. Cagan;
wolalikira ndi Dr. R. L. Hymers, Jr.
pa chihema cha Baptist ku Los Angeles
Madzulo a tsiku la Ambuye Septermber 1, 2019
Text by Dr. Christopher L. Cagan;
preached by Dr. R. L. Hymers, Jr.
at the Baptist Tabernacle of Los Angeles
Lord’s Day Evening, September 1, 2019

“Andreya mbale wache wa Simioni Petro anali m’modzi wa awiriwo, anamva Yohane, namtsata Iye. Anayamba iye kupeza mbale wache yekha Simoni, nanena naye, Tapeza ife Mesiya, ndiko kusandulika Kristu. Anadza naye kwa Yesu. M’mene anmyang’ana iye, anati, uli Simoni mwana wa Yohane; udzatchedwa Kefa, ndiko kusandulika Petro, Mwala” (Yohane 1:40-42; p. 99 Buku lopatulika ndilo mau a Mulungu).


Aka kanali koyamba kuti Petro akumane ndi Yesu. Dzina lake laubwana anali Simon. Yesu anampatsa dzina loti “Petro,” kutanthauza kuti “thandwe” Andreya anali m’bale wake. Petro anali msodzi. Andreya ndi Petro amakhala m’mudzi umene sunali kutali ndi Nyanja ya Galileya, kumene amasodzera. Moyo unali wovuta, chifukwa usodzi umafuna kuti munthu akhale ndi mphamvu, chifukwa ndi ntchito yolemetsa. Petro anali wokwatira chifukwa Yesu anachiritsa a pongozi ake. Petro anali pafupi-fupi zaka makumi atatu pamene amakumana ndi Yesu. Iye anali wa mkulu kuposa ophunzira onse.

Asodzi a m’nyanja ya Galileya anali amphamvu kwambiri. Usodzi umafuna anthu a mphamvu. Anayenera kuchotsa mantha, chifukwa amayenera kukummana ndi anam’mondwe ambiri pa Nyanja. A nam’mondwe amenewa amatha kugudubuza ma bwato awo ang’ono-ang’ono ndi kumira.

Petro si anali Mfalisi. Poti anali mu Yuda amapita ku kachisi nthawi zina. Si anali wosunga miyambo, ngati m’mene Afalisi amachitira. Koma mosiyana ndi asodzi ena, Petro amadziwa kuti ndi wochimwa. Kenaka anati kwa Yesu, “Muchoke kwa ine Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa” (Luka 5:8)

Kotero, Petro sanayambe ngati munthu wa chipembedzo, kapena ngati Mkristu wabwino. Anali munthu wovuta. Anayenera kukhala wadzimphamvu kuti akhale msodzi. Sanali ngati “munthu watchalitchi” wophunzitsidwa bwino. Amagwiritsa ntchito mau oyipa komanso anali wosachedwa kupsa mtima. Anali wochimwa amene anali ndi zolakwatsa zambiri.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

MA ULALIKI ATHU AKUPEZEKA MU MA FONI
ANU A M’MANJA TSOPANO.
PITANI KU WWW.SERMONSFORTHEWORLD.COM.
DAFANYANI BATANI LOBILIWIRA LOMWE LIRI NDI LIU LOTI “APP”
TSATIRANI MALANGIZO OTSATIRAWO.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

Tsopano ganizirani za munthu amene mukufuna kuti adziwe Kristu. Monga Petro, Si anali ndi chidziwitso chambiri mzamau a Mulungu anali munthu wa chipembedzo chabe. Munthu wosazindikira chifukwa choti azibwerera ku tchalitchi kuno. Amaganiza kuti ziribwino kumangokhala kunyumba kumangoonerera masewea a pa kanema, kapena kumangocheza bawo ndi anzake ochimwa. Aliyense amenene amamudziwa ndi kucheza naye anali ngati iyeyo zochitika zao zofanana. Ali ndi machimo ake. Ali ndi maganizo olakwika ake. Ali ndi mavuto ake. Simungamutengere kwa Kristu pokangana naye. M’malo mwache muuzeni za Yesu pazimene Yesu anakuchitirani. Khalani bwenzi lake. Zidzasoweka kuganizira yekha kuti akulondoleni kutchalitchi. Petro sanaphunzitsidwe, komanso simunthu wosochera mdziko.

Mbale wake Andreya ndi amene anamuuza Petro za Yesu. “ Anayamba iye kupeza mbale wake yekha Simoni (Petro), nanena naye, Tapeza ife Mesiya (Mesiya) ndiko kusandulika Kristu”. (Yohane 1:41; p.99). Petro sanakhale wophunzira nthawi yoyamba kumva za Yesu.

Ichi ndi chofunikira kwambiri. Mkalembedwe kake ka “Kapangiidwe ka zisankho” Dr. A.W. Tozer akunena momveka kuti kuwakakamiza anthu kuti anene “pemphero la kulapa” kawirikawiri sizitulutsa M’kristu weni-weni ndi wophunzira wene-weni. Petro sanapange “chisankho” nthawi yoyamba imene anamva za Yesu. Inde, Petro anali ndi chidwi ndi zimene amamva. Ndipo amafuna kumva zambiri. Izi zinali choncho kufikira pamene Yohane m’batizi anamangidwa, mpamene Petro anapanga chisankho kumtsatira Yesu ndikukha wophunzira wake.

“Ndipo ataperekedwa Yohane, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira uthenga wabwino wa Mulungu, nanena, Nthawi yakwana, ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira; temmbenukani mtima, khulupilirani uthenga wa bwino. Ndipo pakuyenda mbali mwa Nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi Andreya, mbale wake wa Simoni , alinkuponya psasa mnyanja; pakuti anali asodzi.Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu. Ndipo pomwepo anasiya makoka ao, namtsata Iye” (Marko 1:14-18; p. 38)

Munthu wina aliyense amene mudzayese kumubweretsa kwa Kristu adzakhala ndi chisankho chokhala wophnzira wa Kristu kapena ayi. Apa mpamene pali kulimbana. Iyi ndi nkhondo. Sikuti yatha pamene wayamba kubwera nanu ku tchalitchi masabata ochepa kapena miyezi. Ndi nkhondo imene iyenera kupitirira kwa miyezi ingapo mwinanso chaka chimene.

Pakusadziwa ichi ndi chimene chikupangitsa kuti ulaliki wa Kreighton Chan ukhale wosapindula kweni-kweni. Amaganiza ngati ena onse otere kuti “alowa” pomwe angomva?

“Pa ichi ambiri a akuphunzira ache anabwerera m’mbuyo, ndipo sanayenda-yendanso ndi Iye. Chifukwa chache Yesu anati kwa khumi ndi a wiriwo, Nanga inunso mufuna kuchoka? Simoni Petro anamyankha Iye, Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu mulinao mau a moyo wosatha. Ndipo tikhulupiria, ndipo tidziwa kuti ndinu Kristu Mwana wa Mulungu wa Moyo.” (Yohane 6:66-67; p 106)

Yesu anati kwa ophunzira khumi ndi awiriwo, “inunso mufuna kuchoka?” “Ndipo Simoni Petro anamyankha Iye, Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu Mulinao mau a moyo wosatha” (Yohane 6:67,68). Zinthu ziwiri zofunikira pa ndime imeneyi.

1. Amene anachoka sanamvekenso! Mu zaka 61 zanga za utumiki ndaona kuti iwo amene amachoka mu mpatuko wa mpingo sakhala ophunzira a mphamvu. Sindinamuone ndi m’modzi yemwe!

2. Petro akanapitanao “ogalukirawo” sakanatembenuka mtima.

“Anaturuka mwa ife, komatu si anali a ife; pakuti akanakhala a ife akanakhalabe ndi ife koma kudatero kuti aonekere kuti si ali onse a ife” (1Yohane 2:19; p 244)

“Kuti ananena nanu, panthawi yotsiriza padzakhala otonza, akuyenda monga mwa zilako-lako zosapembedza za iwo wokha. Iwo ndiwo opatukitsa, anthu amakhalidwe achibadwidwe, osakhala naye Mzimu” (Yuda 18,19; p. 249)

Amene amachoka amangosonyeza kuti sa naone zeni-zeni za kukhala wophunzira. Kukhala wophunzira, wotembenuka weni-weni zimaposa kungo loweza ma vesi angapo a m’baibulo, kapena kungokhulupirira ziphunzitso zingapo. Kukhala wophunzira kumaphatikiza kupanga chisankho chokhalabe; ndipo sipakhalanso zochoka, chifukwa “kunjako” kulibe phindu. Petro anachiona ichi – koma anali wosatembenuka.

Ndikuganiza kuti mwaona tsopano kuti kupulumutsa moyo sichinthu cha masewera! Sikungo lemba dzina kapena kupanga munthu kuti a nene pemphero. Ndikulimbana kwa munthu wa moyo.

Kupulutsika ndi kukhala wophunzira kumaposa kuonetsera kuti Yesu ndani!

“Koma inu mutani kuti Ine ndine yana? Ndipo Simioni Petro anayankha nati; Inu ndin Kristu Mwana wa Mulungu wa moyo. Ndipo Yesu anayankha iye, nati, ndiwe wodala Simoni Bar-Yona pakuti thupi ndi mwazi sizinakuululira ichi, koma atate anga akumwamba.” (Mateyu 16:15-17; p. 21)

Mulungu Tate anaonetsera (anaunikiridwa) kuti Yesu ndani kwa Petro. Mulungu anaonetsera Petro kuti Yesu ndi ndanidi. Koma Petro anali asana pulumutsidwe!!! Anthu ambiri amaganiza kuti anali wopulutsidwa. Koma amalakwitsa.

Yohane atangoonetsa Petro kuti Yesu analidi ndani – pamenepo Petro anayamba kukana uthena wa bwino!!!

“Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukanzunzidwa zambiri ndi a kulu, ndi a nsembe a kulu, ndi alembi; ndikukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa. Ndipo Petro anamtenga Iye, nayamba kumudzudzula, kuti, Dzichitireni chifundo, Ambuye sichidzatero kwa Inu ai. Koma Iye anapotoloka, nati kwa Petro, pita kumbuyo kwanga, satana iwe! Ndiwe chondikhumudwitsa Ine! Chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu. (Mateyu 16:21-23; p 21).

Petro anakaniza uthenga wa bwino. Anafika mpaka pa kumudzudzula pamene ananena kuti Adzapita pamtanda ndi kuuka kwa a kufa. Potero anakana Uthenga! Munthu akhoza kukhala womutsatira Yesu kwa zaka zambiri koma ndi kumalimbanabe ndi malemba kotheratu!

Petro amadzitamandira kuti ndi mkristu wa mphamvu. Usanafike usiku umene Kristu anapachikidwira, Petro anati kwa Iye, Ngakhale ine ndikafa ndi Inu, sindidzakukanani Inu iai.” (Mateyu 26:35; p 34). Pomwe patangotha maola ochepa okha Petro anamukana Yesu katatu!

Petro anali asanagonjetsebe! Anamuthawa Yesu pamene amagwidwa m’munda mwa Getsemane. Anamukana Yesu katatu mokweza. Petro anali wophunzira limodzi ndi anzake – koma kulimbana kwake kunali kukanalipobe. Anali asanagonjetsebe. Anali asanafikepo!

Kufikira pamene Yesu anauka kwa a kufa ndi pamene Petro mapeto ake anatembenuka. Zinalembedwa pa Yohane 20:22,

“Ndipo pamene anati ichi anawapumira nanena nao, Landirani Mzimu Woyera” (Yohane 20:19-22 p. 123)

Pothirira ndemanga, John Ellicott anatiuza kuti Mtumwi Yohane “anakumbukira m’mene zochitika mthawi yawoyo zidzasinthire miyoyo mkulengedwa kwa moyo wa Uzimu watsopano, umene anaitanidwira kuchoka ku infa kupita ku moyo” (Ellicott’s Commentary on the Whole Bible). Komanso, Dr. J. Vernon McGee anati kuti ichi ndi pamene Petro anasinthikanso, anabadwanso katsopano, usiku umene Yesu anauka kwa akufa! (Onani Thru the Bible pa Yohane 20:22)

Apa ndi pamene Petro anadalira Yesu kwa thunthu. Anakhala Mtumwi wolimba mtima amene analarikira pa tsiku la Pentekosite pamene anthu zikwi zitatu anapulumutsidwa. Kenaka anafa chifukwa cha Kristu m’malo momukana Iye. Koma izi zisanachitike Petro anadutsa muzolephera zambiri

Mwaona tsopano kuti kupulumutsa munthu ndi ntchito yaikulu? Singangochitika pa telefoni kapena kudzera mpemphero chabe. Ndi kulimba kwa moyo wa bambo kapena mai. Zidzatengera pemphero lanu, zidzatengera nzeru zanu. Zidzatengera mphamvu yanu. Zidzatengera nthawi yanu. Mukapulumutsa moyo umodzi m’moyo wanu, ndinu odala. Mwachita zambiri. Mwachita bwino. Ndipemphera kuti muthe kuchita zimenezi.

Kodi uwu ukuoneka kuti ndi mseu wautali kuutsatira? Kodi zikuoneka kuti ndi zovuta ndi zazitali? Yesu anati, “Pakuti chipata chiri chopapatiza ndi ichepetsa njirayo, yakumuka nayo ku moyo, ndipo akuchipeza chimenecho ali owerengeka. (Mateyu 7:14; p. 9)

Koma tsopano tiyeni timukumbutse Petro mau ake omwe. Awa ndi mau otsiriza amene Petro analemba asanapachikidwe

,

“Koma kulani m’chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Kristu. Kwa Iye kukhale ulemerero , tsopano ndi nthawi zonse” (2 Petro 3:18; p. 243).


MUKAFUNA KULEMBERA DR.HYMERS MUYENERA KUTCHULA DZIKO LIMENE MUKULEMERA APO AYI SADZATHA KUYANKHA KALATA YANU. Ngati maulaliki awa akudalitsani tumizani e-mail kwa Dr. Hymers ndikumuuza, koma nthawi zonse tchulani dziko limene mukulembera. E-mail ya Dr. Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net dafanyani apa. Mukhoza kumulembera Dr. Hymers mchilankhulo chirichonse, koma muyesetse Mchigerezi ngati mungathe. Ngati mukufuna kulembera Dr. Hymers pa positi, keyara yake ndi P.O. Box 15308, Los Angels, CA 9001. Mukhoza kuimba foni pa (818) 352-0452.

(MAPETO A ULALIKI)
Mukhoza kuwerenga ma ulaliki a Dr. Hymers sabata iriyose pa intaneti iyi
www.sermonsfortheworld.com,
dafanyani “Maulaliki mchichewa.”

Maulaliki awa si oletsedwa. Mukhoza kuagwiritsa ntchito kopanda kufuna chilorezo kwa
Dr. Hymers. Komabe, maulaliki a mkanema ya tchalitchi lathu ngofunika kuagwiritsa
ntchito potenga chilorezo