Print Sermon

Cholinga cha tsamba ili ndi kupereka ma ulaliki a ulere olembedwa komanso a mkanema kwa a busa mdziko lonse la pansi makamaka maiko okwera kumene, komwe kuli ma sukulu a Baibulo ochepa kapena kulibiretu.

Maulaliki awa olembedwa komanso a m’ma video akupezeka pafupifupi m’ma kompyuta 1,500,000 m’maiko 221chaka chilichonse pa www.sermonsfortheworld.com. Anthu zikwi-zikwi amaonera kanema wa pa YouTube, koma kenaka amasiya YouTube ndikubwera ku website yathu. You Tube imawalondolera anthu ku website yathu. Maulaliki olembedwawa akupezeka mzilankhulo 46 mu makomputa 120,000 mwezi uli wonse. Maulalikiwa alibe chiletso, kotero alaliki akhoza kuagwiritsa ntchito mosafuna chilolezo. Chonde sindikizani apa kuti mudziwe m’mene mungaperekere thandizo la mwezi ndi mwezi lomwe lingathandize kwakukulu pofalitsa uthenga wa bwino kudziko lonse la pansi.

Mukafuna kulembera Dr. Hymers nthawi zonse muuzeni dziko limene mukukhala, apo ayi sangakuyankheni. E-mail ya Dr.Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net.




A KRISTU ONYENGA A ZINDIKIRIKA!

THE FALSE CHRISTIAN DISCOVERED!
(Chichewa)

ndi Dr. R. L. Hymers, Jr.

Uthenga wolalikidwa pa Baptist Tembernacle ku Los Angeles.
M’mawa wa tsiku la Ambuye, July 7, 2019
A sermon preached at the Baptist Tabernacle of Los Angeles
Lord’s Day Morning, July 7, 2019

“Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa kumwamba; koma wakuchita chifuniro cha Atate wa kumwamba. Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwero, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mau m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kutulutsa mizimu yoyipa, ndikuchita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, sindinakudziwani inu nthawi zonse; chokani kwa Ine inu akuchita kusayeluzika” (Mateyu 7:21-23).


Ndatenga mutu wanga wa chiphunzitso pa vesi 21,

“Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa kumwamba; koma wakuchita chifuniro cha Atate wa kumwamba” (Mateyu 7: 21)

Ulaliki uwu sunachoke m’maganizo anga. Wakhazikika pa mau a Kristu mwini, ndi ndemanga ya Pulitani Matthew Mead (1629- 1699). Wothirira ndemanga pa Baibulo John MacAuthur anabvomereza buku, Almost Christian Discovered. Nanenso ndikukibvomereza

“Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa kumwamba; koma wakuchita chifuniro cha Atate wa kumwamba” (Mateyu 7: 21)

Munthu akhonza kukhala ndi chidziwitso chambiri, chidziwitso chambiri cha pa Kristu, kuma chonsecho ndi wotayika. A Farisi anali ndi chidziwitso chambiri, chonsecho unali m’badwo wonyenga. Kalanga ine! Amabiri ku gahena ndi chidziwitso chambiri! Kudziwa kokha kudziwa zambiri chimangokhala chidwi chabe. Kudziwonetsera kuti mumadziwa zinthu kumakhala kudzitengera ulemerero pa chabe. Kudziwa ndikuchita chimene ukudziwa ndi chikristu cheni-cheni!

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

MA ULALIKI ATHU AKUPEZEKA MU MA FONI
ANU A M’MANJA TSOPANO.
PITANI KU WWW.SERMONSFORTHEWORLD.COM.
DAFANYANI BATANI LOBILIWIRA LOMWE LIRI NDI LIU LOTI “APP”
TSATIRANI MALANGIZO OTSATIRAWO.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

Munthu akhonza kukhala ndi mphatso za uzimu koma ali wosocera. Mphatso ya pemphero ndi mphatso ya uzimu. Munthu akhonza kumapemphera bwino koma ndikukhala wosochera. Munthu akhonza kukhala ndi mphatso yo lalika chonsecho ali wosapulumuka. Yudasi anali m’laliki wa mphamvu. Yudasi ati, “ Ambuye, Ambuye, ta [lalikira] mdzina lanu, ndi mdzina lanu tatulutsa ziwanda.” Akhonza kuphempherera , ndi kulalikira, kuposa akristu enieni chonsecho sindinu a Kristu eni-eni. Munthu akhoza kuthandiza ena m’mapemphero ndi mu ulaliki pomwe iyeyo akusowa chithandizo.

Mphamvu ya kulalikira ndi kupemphera simadalira ulamuliro wa a mlaliki, kuma mu ulamuliro wa Mulungu a mene amadalitsa. Wina akhonza kupumutsidwa chifukwa cha ulaliki wake, koma wolalikirayo nkupita ku Gehena! Pendleton adalalikira kwa Sanders pa tsiku la Fumukazi Mary kuti ayime ndi uthenga wabwino umenene anango ulalikira, koma pamapeto pake anali mtumwi yemwe anapita ku chiwonongeko! Ndadziwapo anyamata amene anali alaliki a mphamvu, koma kenaka napezeka kuti anali onyenga! Munthu akhonza kulalika ngati m’modzi wa ma Atumwi ndi kupemphera ngati mgelo, koma chonsecho ali ndi mtima wa chiwanda! Munthu akhonza kukhala ndi mphatso ya uzimu yoposa koma chonsecho iye ali wosochera. Bishopu wina anati, “ Anthu osauka ndi osaphunzira amalowa kumwamba, pomwe ife, ndimaphunziro athuwa tikukagwa ku Gehena! Munthu atha kukhala ndi mphatso yayikulu, koma ndikukhala wosokera. Kadontho kamodzi ka chisomo chenicheni, ndi choposa mphatso zochuluka. Yudasi anamtsatira Khristu! Amalalikira uthenga wa bwino wa Khristu, amachotsa ziwanda, mdzina la Khristu, amamwa ndi kudyera pagome limodzi ndi Khristu; chonsecho Yudasi anali wa chinyengo, amene anapita, “ mnjira yake ya yekha” ku Gehena! Amene adziyyerekeza kuti ndi wolungama, chonsecho sachita monga mwa chiyero “ ali ndi maonekedwe chabe a chiyero, koma anakana mphamvu yake.”

Munthu akhonza kudziyenereza kukhala m’Khristu, pomwe mtima wake sunasinthike. Ndi wonyenga amene amaoneka ngati m’Khristu wa bwino, koma wodzala ndi kudzikuza ndi woukira. Ambiri amaoneka ngati a chiyero, koma pomwe chiyero chawo amachita kubvala ngati chophimba kumaso, kubisa kudzikuza ndi kuukira kwa mitima yawo. Izi zikulongosola munthu amene anapita ku sukulu ya Baibulo nadzozedwa. Koma mtima wake sunasinthike. Anasiya mpingo wanthu nkutsatira ka mtsikana kena kokongola koma kosokera. “Dema wandisiya ine, atakonda dziko lino la pansi” (2Timoteo 4:10). Umu ndi m’mene Dr. Kreighton L. Chan, amene anasonyeza kuti ndi wachinyengo pamene kudzikuza ndi kuukira kwake kunaonekera poyera, pamene chophimba kumaso chake chinang’ambika ndi chinyengo chake chinaonekera.

“Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwero, Ambuye, Ambuye, kodi (si ndi) nalalikira mdzina lanu? Ndipo Ine ndidzati kwa iwo: chokani kwa Ine inu akuchita kusayeluzika”

Makoswe ndi mbewa zimakhala mnyumba. Koma nyumba ikamaoneka kuti ikungwa, zimathawa, nkukayang’ana malo ena otetezeka. Masiku amene zinthu ziribwino mtchalitchi amabweretsa onyenga ambiri. Koma pamene mpingo wa gwedezeka, amathawa kuonetsera kuti sanali a Khristu eni-eni kaya amachita zotani mbuyomu. Nawa ena mwa iwo.

Munthu wina ati, “Kumene anditsogolera ndidzamtsata. Kaya ndikumana ndi mabvuto kapena zowawa Yesu… wandipatsa moyo. Lilemekezeke dzina lopambana la Yesu.” Komatu munthu amaneyu ndi amene anali woyambirira kuthawa pamene mpatuko unayamba.

Mtsikana wa chi China anati, “ndikufuna anthu ena adziwe zodabwitsa zimene Mulungu anandichitira. Mulungu agwiritse ntchito moyo wanga kuti ndikhale mboni Yake. Koma anathawa mu mpingo mpatuko usanayambe nkomwe!”

Mnyamata wina wa chi China anati, “sindingathe kulongosola ubwino wa kupumutsidwa ndi Yesu… ndikufuna ena adziwe za zikulu zimene Khristu wandichitira.” Koma patangopita kanthawi kochepa anasiya mpingo ndikutsata Chan, ndikuwonetsa kuti mau ake aja anali achabe. Analibe wonyenga wotayika, wakupita ku Gehena!

Mnyamata wina waku Vietnam anati, “ Ndi chikondi chonse chimene Yesu waonetsa pa ine, sindikukwanitsa kumukonda Iye. Ndipereka moyo wanga kwa Yesu, chipulumutso change.” Patangotha chaka chimodzi anampereka mpulumutsi, ndi kusiya mpingo pamodzi ndi Chan.

Mwana wa Sukulu ya Koleji wina anati, Ndiyamika Mulungu pondiyeretsa ndi mwazi wopambana wa Yesu Khristu. Ambuye alemekezeke!” Zomveka bwino eti? Koma atangonena izi, anabwerera ku machimo a kudziko nkusiya mpingo wathu.

Mtsikana wa chi Japani/ America anati, Umboni wanga ndi wophweka. Ndinadalira Yesu, ndipo anandipulumutsa” – koma anamulipira Iye pakutuluka mu mpingo ndikutsata Chan!

Bambo wina wa ku mexico anati, “ Ndinaoneretsedwa chifundo ndi Mpulumutsi wa chikondi, ndipo ichi sindidzachiyiwala” – koma mwa kanthawi kochepa anaiwala zomwe ananena, natsatira Chan. Ndiri ndi chithunzi cha iye ataima ndi Chan.

Mtsikana win wochokera ku China anati, “ Yesu amandikonda! Tsopano ndikufuna kuyimbira Mpulumutsi wanga, Yesu Khristu!” Zumveka bwino eti? Koma mwamsanga anapereka mpingo wathu, ndi kuthawa ndi Chan!

Wina anandiuza, “Dr. Hymers, musabweretsenso ma China. Ndi anthu a nkhope ziwiri onyenga!” Nzoonadi, pokha-pokha atatembenukadi, adzakhala otaika ngati anthu ndawatchulawa. Yesu anati, “Uyenera kubadwanso” (Yohane 3:7)

“Chisomo chophweka” ndi “chi beliyazamu” ndi mau achilendo, koma “Antinomizimu” si lachilendo. Martin Luther (1483-1546) anatipatsa kalongosolelendwe ka mau amenewa. Amanena za iwo amene amangofuna cholowa cha mchipulumutso koma osafuna kutsatira malamulo ake (Sili Deo Publications, chikutiro cha Mathew Mead’s The Almost Christian Discovered, buku lolembedwanso ndi John MacArthur)

M’modzi mwa anthu wosokera a Chan anati, “ Dr. Hymers amaganiza kuti munthu sangapulumuke pokhapokha wapita ku mpingo wake.” Anthu owukira ngati amenewa amanena bodza lilonse kuti akwaniritse zolinga zao zoipa. Ndipo sindikudabwa kuti ananama motero, chifukwa akudziwiratu kuti ine sindinanene zotero – komanso sindikhulupirira chomwecho.

Koma ndimakhulupilira kuti Mpingo ndi “thupi la Khristu” (Aefeso 4:12). Amene amachoka mu mpingo wake amafoketsa thupiki Lake. Amene amalimbana ndi mpingo Wake , amalimbana ndi thupi lake. Amene amagawa mpingo Wake, akugawa thupi Lake. Amene si mamembala a mpingo Wake, si mamembala a thupi Ake. Ma evangeliko ambiri sasamalitsa posanthula malembo. Nchifukwa chake amachokako ku thupi la Khristu!

Anthu ambiri amaganizira kuti awa ndi maganizo “ofunikira”. Kaya mumaganiza motani ndiribe nazo kanthu, umu ndi m’mene Baibulo likunenera. Mpingo ndi “Thupi la Khristu!”

.Ndikukupemphani m’mawa uno kuti mudze kwa Yesu. Anauka kwa a kufa. Akukhala kudzanja lamanja la Mulungu, ku Mwamba. Idzani kwa Yesu. Chokaniko ku mchitidwe wa dziko la pansi ndi tchimo. Mudalireni Yesu, ndipo Adzakuyeretsani ku machimo onse ndi mwazi Wake wopambana! Mudalireni Yesu ndipo mudzakhala gawo limodzi la thupi lake, lomwe ndi mpingo. Amen.

Ngati mukufuna kulankhulana nafe za kumudalira Yesu mwathunthu chonde idzani muymirire patsogolopa tsopano. Pamene tikuyimba nyimboya mbuku 5; “Monga m’mene ndiriri,” mubwere.

Munga m’mene ndiriri, popanda chonditetezera,
   Koma mwazi Winu unakhetsedwa chifukwa cha ine,
Ndipo mukundiitana kuti ndidze kwanu,
   O Mwana wa Nkhosa wa Mulungu, Ndidza!

Monga m’mene ndiriri, ndipo sindidikira,
   Kutchinjira moyo wanga kunjira ya mdima,
Kwa inu amene mwazi wake ungayeretse dontho liri lonse,
   O mwana wa nkhosa wa Mulungu, Ndidza!
(“Monga m’mene ndiriri” ndi Charlotte Elliot, 1789-1871, yokonzedwanso ndi a busa).


MUKAFUNA KULEMBERA DR.HYMERS MUYENERA KUTCHULA DZIKO LIMENE MUKULEMERA APO AYI SADZATHA KUYANKHA KALATA YANU. Ngati maulaliki awa akudalitsani tumizani e-mail kwa Dr. Hymers ndikumuuza, koma nthawi zonse tchulani dziko limene mukulembera. E-mail ya Dr. Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net dafanyani apa. Mukhoza kumulembera Dr. Hymers mchilankhulo chirichonse, koma muyesetse Mchigerezi ngati mungathe. Ngati mukufuna kulembera Dr. Hymers pa positi, keyara yake ndi P.O. Box 15308, Los Angels, CA 9001. Mukhoza kuimba foni pa (818) 352-0452.

(MAPETO A ULALIKI)
Mukhoza kuwerenga ma ulaliki a Dr. Hymers sabata iriyose pa intaneti iyi
www.sermonsfortheworld.com,
dafanyani “Maulaliki mchichewa.”

Maulaliki awa si oletsedwa. Mukhoza kuagwiritsa ntchito kopanda kufuna chilorezo kwa
Dr. Hymers. Komabe, maulaliki a mkanema ya tchalitchi lathu ngofunika kuagwiritsa
ntchito potenga chilorezo