Print Sermon

Cholinga cha tsamba ili ndi kupereka ma ulaliki a ulere olembedwa komanso a mkanema kwa a busa mdziko lonse la pansi makamaka maiko okwera kumene, komwe kuli ma sukulu a Baibulo ochepa kapena kulibiretu.

Maulaliki awa olembedwa komanso a m’ma video akupezeka pafupifupi m’ma kompyuta 1,500,000 m’maiko 221chaka chilichonse pa www.sermonsfortheworld.com. Anthu zikwi-zikwi amaonera kanema wa pa YouTube, koma kenaka amasiya YouTube ndikubwera ku website yathu. You Tube imawalondolera anthu ku website yathu. Maulaliki olembedwawa akupezeka mzilankhulo 46 mu makomputa 120,000 mwezi uli wonse. Maulalikiwa alibe chiletso, kotero alaliki akhoza kuagwiritsa ntchito mosafuna chilolezo. Chonde sindikizani apa kuti mudziwe m’mene mungaperekere thandizo la mwezi ndi mwezi lomwe lingathandize kwakukulu pofalitsa uthenga wa bwino kudziko lonse la pansi.

Mukafuna kulembera Dr. Hymers nthawi zonse muuzeni dziko limene mukukhala, apo ayi sangakuyankheni. E-mail ya Dr.Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net.
KUTEMBENUKA KWENI-KWENI – WOLEMBEDWA 2015

REAL CONVERSION – 2015 EDITION
(Chichewa – A Language of Malawi)

Wolemba Dr. R. L. Hymers, Jr.

Uthenga wolalikidwa pa Baptist Tabernacle ku Los Angeles
m’mawa wa tsiku la Ambuye, January 4, 2015
A sermon preached at the Baptist Tabernacle of Los Angeles
Lord’s Day Morning, January 4, 2015

“Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa kumwamba” (Mateyu 18:3).


Yesu ananeneratu poyera, “ngati simutembenuka… simudzalowa konse mu ufumu wa kumwamba”. Ananena momveka bwino kuti muyenera kutembenuka. Iye anati ngati simutembenuka, simukalowa mu ufumu wa kumwamba.

M’mawa uno ndifuna ndikuuzeni za munthu amene anatembenuka kweni-kweni. Ndanena kuti kutembenuka “kweni-kweni”. Pogwilitsa ntchito “pemphero la wochimwa”, ndi machitidwe ena a zisankho,anthu a unyinji atembenuka mwa chinyengo.

Tiri ndi anthu ochepa mtchalitchi mwathu, kuphatikizapo mkazi wanga amene anatembenuka kwa nthawi yoyamba yommwe anamva ulaliki wolalikidwa monveka bwino. Awatu anali akuluakulu amene anakozekeretsedwa ndi zimene amadutsamo m’moyo wawo asanamve uthenga wa bwino. Onsewa palibe amene anali khanda. Kutembenuka kwathu kwene-kweni kwambiri, kwakhala kukuchitika pakati pa achinyamata amene amadza kwa Yesu patangotha miyezi (mwinanso zaka) atamva ulaliki wa uthenga wa bwino. Spurgeon anati, ”Pakhonza kukhala chikhulupirilo kwa nthawi yoyamba, koma kawiri-kawiri timafikira chikhulupirilo mzigawo-mzigawo” (C. H. Spurgeon, Around the Wicket Gate, Pilgrim Publications, 1992 losindikizidwanso mchaka cha 1992, p.57). Izi ndi “zigawo” zimene anthu amadutsamo.

I. Choyamba, mumabwera ku tchalitchi pa zifukwa zina osati kuti mudzatembenuke.

Pafupi-fupi wina aliyese amabwera ku tchalitchi kangapo konse ndi zifukwa, “zolakwika” ngati m’mene ndinachitira ine. Ndinabwera kutchalitchi ngati wa chisodzera chifukwa a neba anandiitana kuti ndipite nao kutchalitchi. Ndiye ndinayamba kubwera ku tchalitchi mchaka cha 1954 chifukwa choti ndimasowa wocheza naye, ndi anthu amene anali pafupi ndi nyumba yathu amandikonda. Ichi sichifukwa “chabwino” si choncho? Ndinapita “kutsogolo” pamapeto pa ulaliki woyamba umene ndinamva ndipo ndina batizidwa osapatsidwa uphungu wina uliwonse, osafusidwanso chifukwa chimene ndinabwerera kutsogolo. Umu ndi m’mene ndinakhalira wa Baptist. Koma sindinatembenuke. Ndinabwera chifukwa cha anthu amene anali pafupi ndi nyumba yathu amandikonda, osati chifukwa ndimafuna kupulumutsidwa. Choncho, ndinavutika kwa nthawi yayitali mpaka zaka zisanu ndi ziwiri ndisana tembenuke pa September 28, 1961, pamene ndinamva Dr. Charles J. Woodbridge a kulalika pa Biola College (tsopano ikutchedwa Biola University). Ili ndi tsiku ndinakhulupilira Yesu, ndipo anandiyeretsa na ndipulumutsa ku machimo.

Nanga inu bwanji? Munabwera ku tchalitchi kuno chifukwa mumasowa wocheza naye – kapena makolo anu ndi amene a kubweretsani monga mwana? Ngati muli pano m’mawa uno monga mwa chizolowezi, ngati mwana amene mwakulira mtchalitchi, sizikutanthauza kuti mwatembenuka. Kapena munabwera ngati m’mene ndinachitira ine, pakuti mumasowa wocheza naye ndipo wina anachita kukuitanani? Ngati ndi choncho, sikuti mwatembenuka ayi. Mundimvetse apa. Ndasangalala kuti mwabwera- kaya ndi mwachizolowezi ngati mwana wongotengedwera kutchalitchi kapena mumasowa wocheza naye.

Sipolakwika kupezeka pano mwachizolowezi kapena poti mwasowa wocheza naye. Kungoti sichifukwa chokwanira. Muyenera kufuna chinachake choposa pamenepa kuti mutembenuke, osati chifukwa mumangomva bwino mkamabwera ku tchalitchi.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

MA ULALIKI ATHU AKUPEZEKA MU MA FONI ANU A M’MANJA TSOPANO
PITANI KU WWW.SERMONSFORTHEWORD.COM
NAFANYANI BATANI LOBILIWIRA LOMWE LIRI NDI LIU LOTI “APP”
TSATIRANI MALANGIZO OTSATIRAWO.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

II. Chachiwiri, mumayamba kuzindikira kuti kuli Mulungudi.

Mwina mumadziwa kale kuti Mulungu alikodi musanabwere ku tchalitchi kuno. Koma anthu ambiri amangoona mchizire-zire, osamdziwitsitsa chikhulupiliro chao pa Mulungu asanakumane ndi uthenga wabwino. Mwina ndi m’mene zinaliri ndi inu, ngati munachita kuitannidwa kubwera kuno.

Ngati munakulira mtchalitchi, mumadziwa kale malemba. Mukhoza kupeza malo oyenera m’Baibulo. Mukudziwa chikonzero cha chipulumutso. Mukudziwa ma vesi ndi nyimbo. Koma Mulungu simukumudziwitsitsa.

Kotero, kaya ndinu mulendo, kapena mwana wa mtchalitchi, chinachake chimayamba kuchitika. Mumayamba kuzindikira kuti kuli Mulungudi - osati ku mango lankhula za Mulungu. Mulungu amakhala munthu weni-weni kwa inu.

Kuyambira ndiri wa mng’ono sindima mzindikira Mulungu. Sindinadziwe za “Mulungu wamkulu ndi woopsa” (Nehemiya 1:5) wa m’Baibulo mpaka pamene ndinafika zaka khumi ndi zisanu – patatha zaka ziwiri chiyambireni kupemphera ku mpingo wa Baptist ndi anthu amene amanditenga. Tsiku limene a gogo anga amayikidwa m’manda ndinathawira kumitengo ya kumanda ndinagwapansi ndili wefu-wefu kwinaku thukuta lili kamu-kamu. Mwadzidzidzi Mulungu anatsikira pa ine – ndipo ndi nadziwa kuti ndi weni-wenidi, ndiwamphamvu zonse, ndiwochititsa mantha, mu ulemerero wake. Koma ndinali ndi sanatembenukebe.

Kodi zinakuchitikiranipo izi? Ichi ndiye chinthu chofunikira kwambiri. Baibulo limati,

“Koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo” (Ahebri 11:6).

Kukhulupirira Mulungu kufunika chikhulupiriro chochulukirapo – sichikhulupiriro chotembenuka. Kawiri-kawiri mai wanga amanena kuti, “Ndimakhulipirira Mulungu”. Ndipo ichi sichinali chokaikitsa ayi. Anakhulipirira Mulungu kuyambira ali wa mng’ono. Koma anali wosatembenuka kufikira ali ndi zaka 80. Chinali chofunikira kukhulupirira Mulungu, koma kumafunikira kuonjezera pamenepa kuti a khale wotembenukadi.

Ndiye, ndikunena kuti, mwina mwabwera kutchalitchi kuno osamdziwitsitsa Mulungu. Koma,mwina pang’ono pang’ono, kapena mwachangu, mukutha kuona kuti kuli Mulungudi. Ichi ndiye chigawo chachiwiri, koma sikuti mwatembenuka ayi.

III. Chachitatu, mumazindikira kuti mwa mukhumudwitsa Mulungu ndi machimo anu.

Baibulo limati, “iwo amene ali m’thupi (i.e. iwo amene sanatembenuke) sangathe ku kondweretsa Mulungu” (Aroma 8:8). Ndiye mumayamba kuzindikira kuti ngati munthu wosatembenuka, simungachite chinthu chosangalatsa Mulungu. Mumayamba kuzindikira kuti ndinu wochimwa. Tsiku liri lonse “mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo” (Aroma 2:5). Baibulo limati:

“Mulungu ndiye wakukwiya masiku onse” (Masalmo 7:11).

Mutatha kuzindikira kuti Mulungu alipodi, mumayamba kuzindikira kuti mwamukhumudwitsa Mulunguyo ndi machismo anu. Mwamukhumudwitsanso Mulungu pakusamukonda. Machimo amene mwachimwa ndiwotsutsana ndi Mulungu komanso malamulo ake. Mudzayamba kuzindikira kuti izi ndi zoona. Tsopano kusamukonda Mulungu mudzakuona kuti ndi tchimo lalikulu. Kuposera apa,

Gawo iri kawiri-kawiri limadziwika ndi anthu odziwa malamulo ndi kuti “kugalamuka”. Koma sikungakhale kugalamuka popanda tchimo lirirose ndikutsutsika. Mudzamva ngati m’mene anamvera John Newton amene analemba izi:

O Ambuye, wopanda pake ine, wodetsedwa ndi wopanda chiyero!
Ndingadze bwanji chifupi ndi inu ndi mtolo wa uchimo ngati uwu?
Mtima wonyasa ngati uyu ungakhale pokhalapo panu?
Kalanga ine ndimachimo anji ndikuaonawa!
   (“O Ambuye, wopanda pake ine,” wolemba John Newton, 1725- 1807)

Mudzayamba kuganizira mozama za machimo a muntima mwanu. Mudzaganiza, “mtima wanga ndiwochimwitsitsa, ndikuti uli kutari ndi Mulungu.” Maganizo amenewa adzakusowetsani mtendere. Mudzayamba kudzipyera mtima chifukwa cha maganizo anu ochimwa ndikusowa chikondi kwanu pa Mulungu. Kuzizira kwa mtima kwanu pa Mulungu kudzayamba kukunzunzani tsopano. Mudzayamba kuzindikira kuti munthu woyipa mtima ngati wanuwo alibe chiyembekezo. Mudzaona kuti nkoyenera kuti Mulungu akuponyeni ku Gehena – chifukwa ndinu woyenera Gehena. Izi ndi zimene mudzaganize muka galamukadi ndi kuzindikira kuti mwamukhumudwitsa Mulungu ndi kumu psyetsa mtima ndi machimo anu. Chigawo ichi cha kugalamuka ndichofunikira kwambiri, koma si kutembenuka. Munthu amene waona kuchimwa kwake wagalamuka – koma sanatembenuke. Kutembenuka kumaposera kungotsutsika ndichimo.

Mwadzidzidzi mudzazindikira kuti simunamusangalatse Mulungu, kapena kuti chidziwitso chidzayamba kukula kuchoka pa kungosunga chiphunzitso ndikufikira pakuzindikira kuti Mulungu wakhumudwa nanu. Ndipokha-pokha mutagalamuka pakudziwa kuti ndinu wochimwa ndi wopandachiyero muli wokonzeka kupita “chigawo” cha chinayi cha kutembenuka.

Charles Spurgeon anazindikira za tchimo lake ali ndi zaka 15. A bambo ake ndi a gogo ake onse anali alaliki. Anali m’masiku amene “kupanga chisankho” chakutembenuka kweni-kweni sikumaoneka bwino. Kotero, bambo ake ndi agogo ake “samamukakamiza” kuti apange “chisankho pa Khristu” M’malo mwake, anadikira pa Mulungu kuti agwire ntchito yachipulumutso mwa iye, potero amaganiza akuchita bwino.

Ali ndi zaka khumi ndi zisanu Spurgeon anatsutsika kwambiri ndi tchimo . Spurgeon amalongosola kugalamuka kwake kutchimo lake motere:

Mwadzidzidzi, ndinakumana ndi Mose, atanyamula mdzanja lake lamulo la Mulungu, ndi pakundiyang’ana ine, zimaoneka ngati kuti akundisanthula ndi maso ake a moto. Ana (ndiuza kuti ndi werenge) ‘mau khumi a Mulungu’ – malamulo khumi a Mulungu – ndipo pamene ndinawerenga zimaoneka ngati onsewo amanditsutsa pamaso pa Mulungu woyera.

Pamene izi zimachitika,anaona kuti ndiwochimwa pamaso pa Mulungu, ndikuti palibe “chipembedzo” kapena “ntchito zambwino” zikanatha kumupulumutsa.Mnyamata Spurgeon anadutsa mnyengo ya chiphwinjo chachikulu. Anayesa njira zambiri kuti apeze mtendere ndi Mulungu pakugwiritsa ntchito mphamvu zake, koma kuyesa konseku kunalephera. Ndizimene zimatitengera chigawo cha chinayi cha kutembenuka.

IV. Chachinayi, mumayesa kupeza chipulumutso, kapena kuphunzira za m’mene mugapulumutsidwire.

Munthu wogalamuka amadzimva wochimwa, kuma satembenukira kwa Yesu. Mneneri Yesaya adawalongosola anthu otere pamene ananena, “Monga munthu wobisira anthu nkhope zao, ndipo ife sitinamlemekeza” (Yesaya 53:3). Tiri ngati Adam, amene anadziwa kuti ndiwochimwa, koma anabisala kwa Mpulumutsi, nayesa kuphimba tchimo lake ndi masamba a mkuyu (Genesis 3:7,8).

Monga Adamu wochimwa, wogalamuka anayesa kudzipulumutsa yekha ku tchimo. Akuyesa “kuphunzira” m’mene angadzipulumutsire. Koma akupezeka kuti “kuphunzira” sikukumuchitira ubwino, pakuti ndi ophunzira nthawi zonse, “koma sakhoza konse kufikira kuchidziwitso cha choonadi”(II Timoteo 3:7). Kapena akhonza kumafuna “kudzimva” m’malo mwa Yesu. Anthu amene amafuna monga m’mene “akumvera” amangotero kwa miyezi, pakuti palibe amene amapulumutsika chifukwa cha “kudzimva”. Spurgeon anagalamuka kumachimo ake. Koma anali asanakhulupilire kuti akhonza kupulumutsika pakungo dalira pa Yesu. Anati,

Ndisanadze kwa Khristu, ndinati kwa ine ndekha, “nzoonadi siziyenera kutero, ngati ndakhulupirira mwa Yesu, monga m’mene ndiliri, ndidzapulumutsidwa? Ndiyenera kudzimva chinachache” (ibid).

Ichi chikutengerani ku gawo lachisanu.

V. Lachisanu, kenaka mumadza kwa Yesu, ndikumudalira iye yekha.

Mnyamata Spurgeon kenaka anamva mlaliki akuti, “Yang’ana kwa Yesu Khristu… Suyenera kudziyang’ana wekha… Yang’ana kwa Khristu.” Atavutika ndi kulimbana kwa mkati mwake – Spurgeon kenaka anayang’ana pa Yesu ndi kumudalira Iye. Spurgeon anati, “Ndinapulumutsidwa ndi mwazi wa (Yesu)! Ndikanavina njira yonse mpaka kunyumba.”

Atavutika ndi kukayika, anasiya kuyang’ana pa m’mene amadzimvera ndi china chilichonse cha pa iye. Anangodalira pa Yesu – ndipo Yesu anampulumutsa pompo-pompo. Mwakamphindi kochepa anayeretsedwa kumachimo ndi Mwazi wa Yesu Khristu! Ndi zophweka, koma ndichinthu chofunikira chomwe chiyenera kuchitika pa munthu. Uku, mzanga, ndiye kutembenuka kweni – kweni! Baibulo limati, “ukhulupirire Ambuye Yesu Khristu, ndipo udzapulumuka” (Machitidwe.16:31). Joseph Hart anati,

Nthawi yomwe wochimwa wakhulupirira,
Nadalira pa Mulungu wake wopachikidwa,
Ndi chikhululukiro amalandira,
Chipulumutso cha thunthu mwa mwazi Wake.
   (“The Moment a Sinner Believes” ndi Joseph Hart, 1712-1768).

Pomaliza

Yesu anati,

“Ngati simutembenuka,nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba” (Mat. 18:3).

Osati monga m’mene anachitira mwini sewero la Pilgrim’s Progress, osakhazikika pa “chisankho pa Khristu” chapamwamba-mwamba. Ayi! Ayi! Muwonetsetse kuti kutembenuka kwanu ndi kweni-kweni, chifukwa ngati simudatembenuke kweni-kweni, “simudzalowa mu ufumu wa kumwamba” (Mateyu 18:3).

Tikati kutembenuka kweni-kweni

1.  Muyenera kufika pa malo okhulupirira kweni-kweni kuti kuli Mulungu – Mulungu weni-weni amene amaponya ochimwa ku Gehena, ndi kutengera wopulumutsidwa ku Mwamba akamwalira.

2.  Muyenera kudziwa kuchokera mkati mwanu, kuti ndinu wochimwa amene mwakhumudwitsa Mulungu kwambiri. Mukhoza kukhala wotere kwa nthawi yaitali (kapena nthawi yayifupi kwa ena). Dr. Cagan, Mbusa mzathu, anati, “Ndinalimba-limba m’masiku ambiri osationa tulo kwa miyezi yambiri Mulungu atakhala weni-weni kwa ine. Ndikhonza kulongosola nthawi imeneyi m’moyo mwanga ngati zaka ziwiri zonzunzika m’maganizo” (C. L. Cagan, Ph.D., From Darwin to Design, Whitaker House, 2006, p. 41).

3.  Muyenera kudziwa kuti simungachite china chilichonse kuti muyanjanitsidwe ndi Mulungu wokhumudwa ndi wokwiya. Palibe chimene munganene, kapena kuphunzira, kapena kuchita, kapena kudzimva zingathe kukuthandizani. Izi zidziwikiretu m’maganizo ndi mu mtima mwanu.

4.  Muyenera kubwera kwa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, ndi kuyeretsedwa kumachimo anu mu Mwazi Wache. Dr. Cagan anati, “Ndikutha kukumbukira, bwinolomwe mphindi, zomwe ndina dalira (Yesu)… Zinali ngati mwadzidzi ndinaona (Yesu)…. Ndinalidi limodzi ndi Yesu Khristu ndi Iye analidi ndi ine. Kwa nthawi yayitali ndakhala ndi kuMukana, chingakhale amandiyandikira, mwachikondi kumafuna kundipulumutsa. Koma usiku umenewo ndinadziwa kuti nthawi yakwana kuti ndi mdalire Iye. Ndinadziwa kuti ndiyenera kudza kwa Iye kapena kumukana. Pa mphindi imeneyi, mwa timphindi tochepa chabe, ndinadza kwa Yesu. Sindinalinso wodzidalira wosakhulupirira. Ndinadalira Yesu Khristu. Ndinakhulupirira mwa Iye. Zinalitu mophweka motero… ndinali wothawa-thawa moyo wanga wonse, koma usiku umenewo ndina tembenuka ndi kulunjika nthawi yomweyo kwa Yesu Khristu” (C. L. Cagan, ibid., p. 19). Uku ndiko kutembenuka kweni-kweni. Izi ndizimene ziyenera kuchitika kwa inu kuti mutembenukire kwa Khristu Yesu! Idzani kwa Yesu ndi kumdalira Iye! Adzakupulumutsani ndi kukuyeretsani kumachimo anu ndi mwazi umene anakhetsa pa mtanda! Amen.


MUKAFUNA KULEMBERA DR.HYMERS MUYENERA KUTCHULA DZIKO LIMENE MUKULEMERA APO AYI SADZATHA KUYANKHA KALATA YANU. Ngati maulaliki awa akudalitsani tumizani e-mail kwa Dr. Hymers ndikumuuza, koma nthawi zonse tchulani dziko limene mukulembera. E-mail ya Dr. Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net dafanyani apa. Mukhoza kumulembera Dr. Hymers mchilankhulo chirichonse, koma muyesetse Mchigerezi ngati mungathe. Ngati mukufuna kulembera Dr. Hymers pa positi, keyara yake ndi P.O. Box 15308, Los Angels, CA 9001. Mukhoza kuimba foni pa (818) 352-0452.

(MAPETO A ULALIKI)
Mukhoza kuwerenga ma ulaliki a Dr. Hymers sabata iriyose pa intaneti iyi
www.sermonsfortheworld.com,
dafanyani “Maulaliki mchichewa.”

Maulaliki awa si oletsedwa. Mukhoza kuagwiritsa ntchito kopanda kufuna chilorezo kwa
Dr. Hymers. Komabe, maulaliki a mkanema ya tchalitchi lathu ngofunika kuagwiritsa
ntchito potenga chilorezo

Pemphero loyamba ndi Mr. Abel Prudhomme.
         Nyimbo ya payekha: “Chisomo Chodabwitsa” (ndi John Newton , 1725-1807).


KALEMBEDWE KA

KUTEMBENUKA KWENI-KWENI – ZOLEMBEDWA 2015

REAL CONVERSION – 2015 EDITION

Wolemba Dr. R.L.Hymers. Jr.

“Indetu Ndinena kwa inu, ngati simutembenuka, nimukhala ngati tianato, simukalowa mu ufumu wa kumwamba” (Mateyu 18:3).

I.    Choyamba, mumabwera ku tchalitchi muzifukwa zina mosiyana ndikudzatembenuka.

II.   Chachiwiri, mumayamba kudziwa kuti kuli Mulungudi, Nehemia 1:5; Ahebri 11:6.

III.  Chachitatu, mumazindikira kuti mwakhumudwitsa ndi kukwiyitsa Mulungu ndi machismo anu, Aroma 8:8; 2:5;Masalmo7:11.

IV.  Chachinayi, mumayesa kudzitengera chipulumutso, kapena kuphunzira za m’mene mungapulumutsidwire, Yesaya 53:3; Genesis 3:7,8; II Timoteo 3:7.

V.   Chachisanu, pomaliza mumadza kwa Yesu, ndi kumdalira Iye yekha, Machitidwe 16:31.