Print Sermon

Cholinga cha tsamba ili ndi kupereka ma ulaliki a ulere olembedwa komanso a mkanema kwa a busa mdziko lonse la pansi makamaka maiko okwera kumene, komwe kuli ma sukulu a Baibulo ochepa kapena kulibiretu.

Maulaliki awa olembedwa komanso a m’ma video akupezeka pafupifupi m’ma kompyuta 1,500,000 m’maiko 221chaka chilichonse pa www.sermonsfortheworld.com. Anthu zikwi-zikwi amaonera kanema wa pa YouTube, koma kenaka amasiya YouTube ndikubwera ku website yathu. You Tube imawalondolera anthu ku website yathu. Maulaliki olembedwawa akupezeka mzilankhulo 46 mu makomputa 120,000 mwezi uli wonse. Maulalikiwa alibe chiletso, kotero alaliki akhoza kuagwiritsa ntchito mosafuna chilolezo. Chonde sindikizani apa kuti mudziwe m’mene mungaperekere thandizo la mwezi ndi mwezi lomwe lingathandize kwakukulu pofalitsa uthenga wa bwino kudziko lonse la pansi.

Mukafuna kulembera Dr. Hymers nthawi zonse muuzeni dziko limene mukukhala, apo ayi sangakuyankheni. E-mail ya Dr.Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net.
“NJIRA YA CHISOMO” WOLEMBA GEORGE WHITEFIELD, WOKONZEDWA MCHIZUNGU CHATSOPANO

“THE METHOD OF GRACE” BY GEORGE WHITEFIELD,
CONDENSED AND ADAPTED TO MODERN ENGLISH
(Chichewa)

Ndi Dr. R. L. Hymers, Jr.

Uthenga wolalikidwa pa Baptist Tabernacle ku Los Angeles
m’mawa wa tsiku la Ambuye, January 4, 2009
A sermon preached at the Baptist Tabernacle of Los Angeles
Lord’s Day Morning, January 4, 2009

“Ndiponso apoletsa bala la anthu anga pang’onopang’ono, ndi kuti, Mtendere, mtendere; palibe mtendere.” (Yeremiya 6:14)


Mau oyamba: George Whitefield anabadwira ku Gloucester, England mchaka cha 1714. Anali mwana wa mwini malo ogulitsirapo mowa. Ndimalo ngati amenewa kunali kovuta kuti akule mchiKristu, koma kusukulu anali ndi kuthekera kodabwitsa. Anachita maphunziro ake a pa sukulu ya Oxford University kumene anadziwana ndi John ndi Charles Wesley nakhala gawo limodza la mlaga wao wa mapemphero

Akanali mwana wa sukukulu pa Oxford anatembenuka. Kenaka anadzozedwa ndi Mpingo wa England. Maulaliki ake a zofunikira zeni-zeni pa moyo watsopano anapangitsa kuti mipingo izitseka makomo awo kwa iye, pakuti a busa a chithupi-thupi amaopa kuti ma ulaliki ake onena za zofunika zeni-zeni pa moyo wa tsopano anakwiyitsa akuluakulu awo a mpingo. Pachifukwa ichi anakakamizidwa kuchoka mu mpingo, kuti azikalalikira kunja, komwe anakatchuka kwambiri.

Whitefield anapita ku America mchaka cha 1738 ndikuyambitsa malo osungirako ana a masiye. Kenaka anayenda m’maiko onse amene anali pansi pa ulamuliro wa America ndi Britain kulalika ndi kusonkhetsa ndalama zothandizira ana amasiye. Analalika ku Spain, Holland, Germany, France, England, Wales, ndi Scotland, ndi kuyenda maulendo khumi ndi atatu kuwoloka Nyanja ya Atlantic kukalalika ku America.

Anali pa chinzake kwambiri ndi Benjamin Franklin, Jonathan Edwards ndi John Wesley, ndipo iye ndi amene analimbikitsa Wesley kumakalalikira kunja, ngati m’mene amachitira iyeyo. Benjamin Franklin nthawi ina anayerekeza kuti Whitefield analankhula ndi anthu zikwi makumi atatu. Misonkhano yake kawiri-kawiri imakhala ndi anthu oposa 25,000. Nthawi ina analalika pafupi ndi Glasgow, Scotland kwa anthu oposa 100,000 msonkhano umodzi okha – tsiku limodzi nthawi imeneyo kunalibe zimkuza mau! Anthu zikwi khumi anavomereza kuti apulumuka pa msonkhano umenewo.

Amadziwika ndi anthu ambiri kuti ndi mlaliki wa mphamvu wa chizungu wa nthawi zonse. Chingakhale Billy Graham analankhula kwa anthu ambiri pogwiritsa ntchito zida zamakono, koma zimene Whitefield anachita zinabweretsa kusintha kwa kukulu mchikhalidwe.

Whitefield anali mtsogoleri wa kugalamuka kwa kukulu, chitsitsimutso chimene chinasula chikhalidwe cha America mkatikati mwa zaka za m’ma 18th century. Maiko onse anayaka ndi moto wa chitsitsimutso pamene amalalika. Pachimake pa chitsitsimutso chimenechi panali mchaka cha 1740 nthawi imene Whitefield anayendera New England kwa masabata asanu ndi limodzi. M’masiku makumi anayi ndi asanu okha analalikira maulaliki oposa 75, ku anthu miyanda- miyanda, anasiya mderalo muli mpungwe-pungwe wa uzimu, imene inali nthawi yosaiwalika mchikristu cha ku America.

Pamene amamwalira anali wosilirika ndi wopatsa chidwi ndi maiko onse amene amalankhula chizungu. Iye ndi amene anathandizira kuyambitsa Princeton University, Dartmouth College, ndi University of Pennsylvania. Anamwalira kanthawi kochepa atangolalikira pa Newburyport, Massachusetts, mchaka cha 1770, zaka zisanu ndi chimodzi kusanafike mpungwe-pungwe wa ndale wa mu America. George Washington anali tate wa dziko lathu, koma George Whitefield anali gogo wake

Ulaliki wotsatilawu wa Whitefield waikidwa mkalankhulidwe katsopano uwu ndi ulaliki wake weni-weni, koma ndauyika m’malankhulidwe atsopano kuti umveke bwino mnyengo yathu ino.

“Ndiponso apoletsa bala la anthu anga pang’onopang’ono, ndi kuti, Mtendere, mtendere; koma palibe mtendere.” (Yeremiya 6:14)

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

MA ULALIKI ATHU AKUPEZEKA MU MA FONI ANU A M’MANJA TSOPANO
PITANI KU WWW.SERMONSFORTHEWORD.COM
NAFANYANI BATANI LOBILIWIRA LOMWE LIRI NDI LIU LOTI “APP”
TSATIRANI MALANGIZO OTSATIRAWO.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

Ulaliki: Mdalitso wa ukulu umene Mulungu akhonza kupereka kudziko ndi kupereka a laliki a bwino ndi okhulupirika. Koma temberero lalikulu limene Mulungu akhonza kutumiza ku dziko ndi kuvomereza mipingo kuti izitsogozendwa ndi a laliki osochera amene amangokhudzidwa ndi kupanga ndalama. Chonsecho mu’badwo wina suliwonse mwakhala muli alaliki onyenga amene amalalika maulaliki ongosangalatsa. Kuli atumiki ambiri okhala ngati amenewa amene amapotoza Baibulo ndi kunyenga anthu.

Umu ndi m’menene zinaliri m’masiku a Yeremiya Ndipo Yeremiya analankhula motsutsana nawo mokhulupirika mkumvera Mulungu. Anatsekula pakamwa pake natsutsana ndi alaliki akuthupi amenewa. Mutawerenga buku lake, muona kuti palibe amene analankhula mwa mphamvu kutsutsana ndi a laliki achinyengo ngati Yeremiya. Analankhula kwambiri motsutsana nao mu chaputala chimene tatengamo mutu wa nkhani yathu.

“Ndiponso apoletsa bala la anthu anga pang’onopang’ono, ndi kuti, Mtendere, mtendere; koma palibe mtendere” (Yeremiya 6:14)

Yeremiya anati iwo amangolalikira za ndalama. Mu vesi la khumi ndi chitatu, Yeremia anati,

“Pakuti kuyambira wamng’ono kufikira wamkuru onse akhala akusirira; ndiponso kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita monyenga” (Yeremiya 6:13).

Iwo anali a kusirira ndi olalika mwa chinyengo.

Mu mutu wathu, akuwonetsa njira imodzi m’menene amalalikira monyenga. A kuwonetsa njira za chinyengo zochitira miyoyo yosochera:

“Ndiponso apoletsa bala la anthu anga pang’onopang’ono, ndi kuti, Mtendere, mtendere; koma palibe mtendere” (Yeremiya 6: 14).

Mulungu anauza mneneri kuti achenjeze anthu pa nkhondo imene ili nkudza. Mulungu amafuna kuwauza kuti nyumba zawo zidzawonongendwa – nkhondo imeneyo idzadza ndithu (onani pa Yeremiya 6:11-12).

Yeremiya anapereka uthenga wa chiphaliwali. Unayenera kuoopsa anthu ambiri ndikuwatengera kukulapa machimo awo. Koma aneneri onyenga ndi a nsembe anazungulira nawapatsa anthu chitonthozo chabodza. Ananena kuti Yeremiya ndiwamisala. Anati sikudzakhala nkhondo. Anauza anthu kuti kudzakhala mtendere, pamene Yeremiya anati kudzakhala kopanda mterendere.

Mau a m’ndime ya mutu wathu akunena za mtendere wa kunja. Koma ndi kukhulupirira kuti akulankhulanso za moyo. Ndikukhulupiriranso kuti akunena za a laliki onyenga amene amauza anthu kuti ndi abwino, chingakhale sanabadwenso kachiwiri. Anthu osapulumutsidwa amakonda ma ulaliki ngati amenewa. Mtima wa munthu ndi woyipa ndi wonyenga. Ndi Mulungu yekha amene angathe kudziwa koopsa kwa mtima wa muthu.

Ambiri a inu mumati muli pa mtendere ndi Mulungu, pomwe palibe mtendere weni-weni! Ambiri a inu mumaganiza kuti ndinu aKristu, koma sichoncho. Satana ndi amene wakupatsani mtendere wabodza. Si Mulungu amene wakupatsani “mtedere” umenewu. Si mtendere umene umaposa kamvetsetsedwe ka munthu. Muli ndi mtendere wa bodza.

Nkofunikira kuti mudziwe ngati muli ndi mtendere weni-weni kapena ayi. Aliyense amafuna mtendere. Mtendere ndi mdalitso waukuklu. Kotero ndiyenera kukuuzani kapezedwe keni-keni ka mtendere ndi Mulungu. Ndikufuna kukhala opanda mulandu ndi mwazi wanu. Ndiyenera kukupatsani uphungu wonse wa Mulungu. Kudzera m’mutu wathu, ndiyesa kukuwonetsani chimene chiyenera kuchitika kwa inu, ndichimene chiyenera kusintha mkati mwanu kuti mukhale ndi mtendere weni-weni mu mtima mwanu.

I. Choyamba, musanakhale ndi mtendere ndi Mulungu, muyenera kuonetsedwa, kudzimva, kulira, ndi kusweka mtima chifukwa cha mphulupulu zanu zotsutsana ndi malamulo a Mulungu.

Malinga ndi chipulumutso chifukwa cha ntchito, “moyo wochimwawo ndiwo udzafa”. (Ezekieli 18:4)

Aliyese ndiwotemberedwa amene sapitiriza kuchita zonse zimene zinalembedwa mbuku la chilamulo.

Simuyenera kumangochita zina zokha, koma muyenera kuchita zinthu zonse apo ayi ndinu wotembereredwa:

“Pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa ali yense wosakhala m’zonse zolembedwa m’buku la chilammulo kuzichita izi” (Agalatiya 3:10).

Kusuntha pang’ono ku chilamulo, kaya ndi m’maganizo, kapena m’mau, kapena m’machitidwe, zimakupangitsani kuti muyenera kulandira chilango chosatha, malingana ndi malamulo a Mulungu. Ndiye ngati lingaliro limodzi loyipa, ndi ganizo limodzi loyipa, ndi mchitidwe umodzi woyipa umamtengera munthu ku chitayiko, ndi majahena angati akuyenera anthu amene moyo wawo wonse wakhala womangomuchimwira Mulungu! Musanakhale ndi mtendere weni-weni mumtima mwanu, muyenera kuonetseredwa kuti nkoopsa kumusiya Mulungu ndi kuchimwa motsutsana ndi lamulo lake.

Uyeseni mtima wanu. Ndikufunseni –Kodi panali nthawi pamene mutakumbukira machimo anu munamva kuwawa? Kodi panali nthawi pamene munamva kuti simungathenso kunyamula mtolo wa machimo anu? Kodi munaonapo kuti mkwiyo wa Mulungu akubwerani pa kaone, chifukwa mwa phwanyadi lamulo lake? Kodi munadzimverapo chisoni mumtima mwanu chifukwa cha tchimo? Kodi mutha Kunena kuti, “ Machimo anga ngolemera kwambiri sindingathe kuanyamula? Kodi munakumananazo izi? Ngati sichoncho, musadzitche kuti ndinu mkristu! Mukhoza kunena kuti muli ndi mtendere, koma mulibe mtendere. Ambuye akugalamutseni! Ambuye akutembenuzeni!

II. Komanso, musanakhale ndi mtendere ndi Mulungu, muyenera kutsutsidwa mozama; muyenera kutsutsidwa kuchikhalidwe chanu chokhotakhota, ndi kunzunzika kwa moyo wanu.

Muyenera kutsutsidwa kumachimo anu eni-eni. Muyenera kumanjenjemera chifukwa cha machimo amenewa. Koma kutsutsika kupose pamenepa. Muyenera kutsutsika chifukwa chophwanya malamulo a Mulungu. Chinanso muyenera kudziwa kuti munabadwa wochimwa, ndipo tchimo lachibadwidwe liri mu mtima mwanu limene Mulungu akhonza kukulangani nalo.

Anthu ambiri amene amadziyesa anzeru amati kulibe tchimo lobadwanalo. Amaganiza kuti Mulungu ndiwopanda chilungamo pokankhira tchimo la Adamu pa ife. Amanena kuti sitinabadwe mu uchimo. Amati simuyenera kubadwanso. Koma taonani zochitika m’dziko lomwe lakuzungulirani. Kodi ndi paradizo amene Mulungu analonjeza kwa munthu? Ayi! Palipose mdziko la pansi pali mpungwepugwe! Izi zikutanthauza kuti chinachake sichilibwino pa mtundu wa anthu. Ndi tchimo lachibadwidwe lomwe labweretsa mavuto amenewa pa dziko lapansi.

Kaya mukukana chotani za izi, mukadzagalamuka, mudzaliona kuti tchimo la m’moyo mwanu likuchokera mumtima wanu wotsutsika – mtima umene unasakazika ndi ndulu ya tchimo la chibadwidwe.

Pamene munthu wosatembenuka wagalamuka kwa nthawi yoyamba, amayamba kudabwa, “Kodi ndinali woyipa chotere?” Mzimu wa Mulungu amamuwonetsa kuti analibe chabwino mchikhalidwe chake chonse. Amaona kuti mulibe chabwino mwaiye komanso ndi wolephera. Munthu wotere amayamba kuona kuti nkoyenera kuti Mulungu amulange. Amaona kuti anasakazika ndi woukira mchikhalidwe chake chenicheni moti kunali koyenera kuti Mulungu amulange, chingakhale sanachimwepo ndi tchimo lowoneka ndi maso.

Kodi zinakuchitikiranipo izi? Munayamba mwamvapo kuti kunali koyenera kuti Mulungu akulangeni? Kodi munavomerezapo kuti ndinu ana a mkwiyo chibadwire? (Aefeso 2:3).

Ngati munabadwa katsopanodi, ndi kudzikonda kunachokadi mwa inu, mukanachiwona ndi kuchimva ichi. Ndipo ngati simunamvepo kulemera kwa tchimo lachibadwidwe, musadzitche m’kristu! Tchimo la chibadwidwe ndiye mtolo waukulu kwa munthu amene akufuna kupulumutsidwa. Munthu wobadwa katsopano weni-weni amadzutsika ndi tchimo la chibadwidwe lomwe linaononga chikhalidwe chake. Wopulumutsidwa weni-weni kawiri-kawiri amalira, “Ooo, adzandilanditse ndani m’thupi la imfa iyi?” (Aroma 7:24). Ichi nchimene chimamsautsa kwambiri munthu wogalamuka.- tchimo la mu mtima. Ngati simunazindikire kulephera kwanu, simungathe kupeza mtendere mu mtima mwanu.

III. Popitirira apa, musanakhale ndi mtendere weni-weni ndi Mulungu, musamangovutika ndi machimo anu a chikhalidwe, komanso pa machimo a zisankho zanu, kudzipereka kwanu, komanso “moyo wa Chikristu.”

Mzanga. Nchiyani chimene ukuchita chimene Mulungu adzakuyamikire nacho? Ndiwe wosalugamitsidwa, ndi wosatembenuka chifukwa cha chikhalidwe chako. Uyenera kuponyedwa ku Jahena ka khumi chifukwa cha tchimo lako. Kodi ntchito zako zidzakupindulira chiyani? Sichingachite chinthu chabwino mthupi.

“Ndipo iwo amene ali m’thupi sangathe kukondweretsa Mulungu” (Aroma 8:8).

Nkosatheka munthu wosatembenuka kuchita chinthu cho mulemekeza Mulungu.

Chingakhale tinatembenuka, sitisinthikiratu kwathunthu, tchimo limapitilirabe mwa ife. Mzochitaka zathu mumakhalabe mchitidwe wa tchimo. Ndiye, tikatembenuka, ngati Yesu adativomera chifukwa cha ntchito zathu, tchito zathu zikanatitsutsa. Sitingamapemhere kopanda timachimo tina m’menemo, kudzikonda, ulesi, kusalungama kwina ndi kwina. Sindikudziwa chimene mukuganiza, koma ine sindingapemphere opanda kuchimwa. Sindingalalikile kwa inu opanda ku chimwa. Sindingachite chinthu chilichose opanda tchimo. Kulapakwanga kuyenera kulapidwa, misozi yanga ichapidwe mu Mwazi wopambana wa mpulumutsi wanga, Yesu Kristu!

Zikhazikitso zathu zabwino, ntchito zathu zabwino, ziganizo zathu zabwino, zimangoonetsera machimo chabe. Ntchito zathu za chipembedzo ndi zodzadza ndi machimo. Musanakhale ndi mtendere mumtima mwanu musango nyasidwa ndi machimo anu a chibadwidwe ndi machimo anu ooneka, koma musamveso bwino ndi chiyero cha inu nokha, ndi ntchito za chipembedzo. Muyenera kutsutsidwa kwakukulu musanatulukemo mkudziyenereza kwanu. Ngati simunamvepo kuti mulibe chiyero cha pa inu nokha, simungalungamitsidwe ndi Yesu Kristu. Ndiye kuti simunatembenuke.

Wina akhonza kunenena kuti, “Chabwino, ndikukhulupilira zonsezi”. Koma pali kusiyana kwakukulu pakati pa “kukhulupilira” ndi “kudzimva” Kodi munayamba mwadzimvapo kusoweka kwanu kwa muwomboli, kusoweka kwanu kwa Kristu? Kodi munayamba mwadzimvapo kuti mukufuna Kristu chifukwa mulibe ubwino wa inu nokha? Ndipo mukhonza kunena kuti , “ Ambuye mukhonza kundikana chifukwa cha ntchito za chipembedzo zomwe ndakhala ndi kuchita.” Ngati simunadzitsutse chotere, simungakhake ndi mtendere weni-weni.

IV. Tsopano, chachinayi, musanakhale ndi mtendere ndi Mulungu, pali tchimo limodzi limene muyenera kunzunzika nalo kwambiri. Ndikudziwa kuti ndiwochepa chabe amene angaganizire limeneri. Nditchimo lachikhalire padziko lapansi, koma dziko lapansi sili liganizira ngati tchimo. Mukufunsa, “Kodi nditchimo lanji limeneri?” Nditchimo limene ambiri a inu mumatsutsika nalo- ndipo ili ndi tchimo la kusakhulupirira.

Musanakhale ndi mtendere, muyenera kunzunzika ndi kusakhulupirira kwa mtima wanu. Kodi zikhonza kutheka kuti simukhulupilra mwa Yesu Kristu?

Ndikulankhula ndi mtima wanu. Ndili ndi nkhawa kuti mulibe chikhulupiriro mwa Yesu koposa satana mwini. Ndikuganiza kuti Satana amakhulupirira Bible kwambiri kuposa ambiri a inu. Amakhulupirira za uMulungu wa Yesu Kristu. Amakhulupilira ndipo amanjenjemera. Amanjenjemera kuposa zikwi za anthu amene amadzitcha Akristu.

Mumaganiza kuti ndinu okhulupirira chifukwa mumakhulupirira Baibulo, kapena poti mumapita ku tchalitchi. Zonsezi mukhoza kuchita opanda kukhala ndi chikhulupiriro mwa Kristu. Kungokhulupirira chabe kuti kunali munthu dzina lake Kristu sizingakuchitireni ubwino, nchimodzimodzi kukhulupirira kuti kunali Ceasar kapena Alexander Chiphona. Baibulo ndi Mau a Mulungu. Tikuthokoza chifukwa cha ilo. Koma mukhonza kulikhulupirira, koma usakhulupirira Ambuye Yesu.

Nditakufunsani kuti patenga nthawi yayitali bwanji chikhulupirireni Yesu Kristu, ambiri a inu munena kuti munakhulupirira iye kuyambira kale. Simunganene kuti simunamu khulupirire Yesu Kristu. Iwo amene amakhulupiriradi Kristu amadziwa kuti inalipo nthawi imene samakhululupirira Iye.

Ndilankhulepobe pa ichi, chifukwa limeneri ndi bodza lokanika kochoka. Anthu ambiri atengekanalo – poganiza kuti ndiwokhulupiria kale. Mkulu wina wake wotchedwa Marshall analemba mndandanda wa machimo ake molinganiza ndi malamulo khumi, napita nao kwa mbusa nafunsa kuti nanga nchifukwa chiyani sakupeza mtendere. Mbusa anayang’ana mndandanda uja nati, “Choka! Sindikuona liwu limodzi la tchimo la kusakhulupirira pa mndandanda wako.” Ndi ntchito ya Mzimu wa Mulungu kukutsutsa pa kusakhulupirira kwako – kuti mulibe chikhulupiriro. Yesu ananena za Mzimu Woyera.

“Adzatsutsa dziko lapansi za machimo…Za machimo, chifukwa sakhulupirira Ine” (Yohane 16:8-9).

Tsopano, okondedwa anzanga, Mulungu anayamba wakuonetsanipo kuti mulibe chikhulupiriro mwa Yesu? Munayamba mwadzimverapo chifukwa cha mtima wanu wouma wosakhulupirira? Kodi munapempherapo kuti, “Ambuye ndithandize ku mgwiritsitsa Kristu?” Kodi Mulungu anakutsutsanipo chifukwa cha kulephera kwanu kudza kwa Kristu, ndi kukupangitsani kuti mulire m’pemphero kuti mukhale ndi chikhulupiriro mwa Kristu? Ngati sichoncho, simudzapeza mtendere mumtima mwanu. Mulungu akugalamutsenu, nakupatsani mtendere weni-weni mwa Yesu, musanamwalire mwayi wotere usanathe.

V. Kenanso, musanakhale ndi mtendere ndi Mulungu, muyenera kugwiritsa chiyerero cha Kristu.

Musangotsutsidwa ndi tchimo limene mukuchita kapena lachibadwidwe, tchimo lodziyenereza, ndi tchimo la kusakhulupirira, koma muyenera kutha kugwiritsa chiyero cha ngwiro cha a Mbuye Yesu Kristu. Muyenera kugwiritsa chiyero cha Kristu. Mukatero mudzakhala ndi mtendere. Yesu anati:

“Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.” (Mateyu 11:28)

Vesi ili limapereka chilimbikitso kwa onse olema ndi othodwa, koma asati kwa wina aliyense. Pomwe lonjezo la kupumula ndi la okhawo amene adza na khulupirira Yesu Kristu. Musanakhale pa mtendere ndi Mulungu muyenera kulungamitsidwa mwachikhulupiriro mwa Ambuye wathu Yesu Kristu. Muyenera kumulandira Kristu m’moyo wanu, kuti chiyero Chake chikhale chiyero chanu, kuti zokoma zake zikhalenso zanu.

Anzanga okondedwa, kodi munakwatiwapo ndi Kristu? Kodi Yesu Kristu anadziperekapo kwa inu? Kodi inu munadzapo kwa Kristu muchikhulpiriro cha moyo? Ndikupemphera kwa Mulungu kuti Kristu adze nalankhule mtendere kwa inu. Izi zikuchitikireni kuti ngati ndinu wobadwanso katsopano.

Ndikulankhula tsopano zeni-zeni za mdziko losaoneka ndi maso, za chikristu cha mkati, za ntchito za Mulungu mumtima mwa wochimwa. Ndikulankhula tsopano zinthu zofunikira kwambiri kwa inu. Nonsenu ndinu wokhudzidwa ndi izi. Moyo wanu ndiwo khudzidwa ndi ichi. Chipulumutso chanu chosatha chidalira ichi.

Mukhonza kumva mtendere opanda Kristu. Satana wakugonekani ndi kukupatsani chitetezo chabodza. Adzayesetsa kuti akugonekenibe mpaka akuponyeni ku Jahena. Kumeneko mukagalamuka, koma kudzakhala kugalamuka koopsa pakuti mudzazindikira muli m’malawi a moto komwe simudzathaso kulapa. Kujahena mudzaitanitsa dontho la madzi kuti liziziritse lilime lanu kwa muyaya, koma madzi sadzapatsidwa kwa inu.

Moyo wanu sudzapeza mpumulo pokhapokha mupumule mwa Yesu! Cholinga changa ndi kusonkhanitsira wochimwa kwa Mpulumutsi. O kuti Mulungu akubweretseni ena a inu kwa Yesu. Mzimu woyera akutsutseni inu ochimwa, ndi kukutembenuzani kunjira zanu zoyipa kwa Yesu. Ameni.


MUKAFUNA KULEMBERA DR.HYMERS MUYENERA KUTCHULA DZIKO LIMENE MUKULEMERA APO AYI SADZATHA KUYANKHA KALATA YANU. Ngati maulaliki awa akudalitsani tumizani e-mail kwa Dr. Hymers ndikumuuza, koma nthawi zonse tchulani dziko limene mukulembera. E-mail ya Dr. Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net dafanyani apa. Mukhoza kumulembera Dr. Hymers mchilankhulo chirichonse, koma muyesetse Mchigerezi ngati mungathe. Ngati mukufuna kulembera Dr. Hymers pa positi, keyara yake ndi P.O. Box 15308, Los Angels, CA 9001. Mukhoza kuimba foni pa (818) 352-0452.

(MAPETO A ULALIKI)
Mukhoza kuwerenga ma ulaliki a Dr. Hymers sabata iriyose pa intaneti iyi
www.sermonfortheworld.com,
dafanyani “Maulaliki mchichewa.”

Maulaliki awa si oletsedwa. Mukhoza kuagwiritsa ntchito kopanda kufuna chilorezo kwa
Dr. Hymers. Komabe, maulaliki a mkanema ya tchalitchi lathu ngofunika kuagwiritsa
ntchito potenga chilorezo

Nyimbo ya payekha: “O Lord, How Vile Am I” (ndi John Newton , 1725-1807).


KALEMBEDWE KA

“NJIRA YA CHISOMO” WOLALIKIDWA NDI GEORGE WHITE FIELD, WOKONZEDWANSO MCHIZUNGU CHATSOPANO

“THE METHOD OF GRACE” BY GEORGE WHITEFIELD,
CONDENSED AND ADAPTED TO MODERN ENGLISH

ndi Dr.R.L.Hymers, Jr.

“Apoletsa bala la anthu anga pang’onopang’ono, ndikuti, mtendere, mtendere, koma palibe mtendere.” (Yermiya 6:14)

(Yeremiya 6:13)

I. Musanakhale ndi mtendere ndi Mulungu, muyenera kuonetsedwa,
kudzimva, kulira, ndi kusweka mtima chifukwa cha mphulupulu zanu
ndi malamulo a Mulungu, Ezekiele 18:4; Agalatiya 3:10.

II. Musanakhale ndi mtendere ndi Mulungu, muyenera kutsutsidwa mozama;
muyenera kutsutsidwa kuchikhalidwe chanu chokhotakhota, ndi
unzunzika kwa moyo wanu, Ayefeso 2:3; Aroma 7:24.

III. Mmusanakhale ndi mtendere weni-weni ndi Mulungu, musamangovutika
ndi machimo anu a chikhalidwe, komanso pa machimo zisankho
zanu, kudzipereka kwanu, komanso “moyo wa Chikristu.,” Aroma 8:8.

IV. Musanakhale ndi mtendere ndi Mulungu, mukhale Wotsutsika ndi tchimo
la kusakhulupirira mwa Yesu, Yohane 16:8-9.

V. Musanakhale ndi mtendere ndi Mulungu, muyenera kugwiritsitsa
chiyero cha Kristu. Mateyu 11: 28.