Print Sermon

Cholinga cha tsamba ili ndi kupereka ma ulaliki a ulere olembedwa komanso a mkanema kwa a busa mdziko lonse la pansi makamaka maiko okwera kumene, komwe kuli ma sukulu a Baibulo ochepa kapena kulibiretu.

Maulaliki awa olembedwa komanso a m’ma video akupezeka pafupifupi m’ma kompyuta 1,500,000 m’maiko 221chaka chilichonse pa www.sermonsfortheworld.com. Anthu zikwi-zikwi amaonera kanema wa pa YouTube, koma kenaka amasiya YouTube ndikubwera ku website yathu. You Tube imawalondolera anthu ku website yathu. Maulaliki olembedwawa akupezeka mzilankhulo 46 mu makomputa 120,000 mwezi uli wonse. Maulalikiwa alibe chiletso, kotero alaliki akhoza kuagwiritsa ntchito mosafuna chilolezo. Chonde sindikizani apa kuti mudziwe m’mene mungaperekere thandizo la mwezi ndi mwezi lomwe lingathandize kwakukulu pofalitsa uthenga wa bwino kudziko lonse la pansi.

Mukafuna kulembera Dr. Hymers nthawi zonse muuzeni dziko limene mukukhala, apo ayi sangakuyankheni. E-mail ya Dr.Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net.



Woyimba nyimbo ulaliki usanayambe: “Malo a pa mwamba”
          (ndi Johnson Oatman, Jr., 1856-1926).


KODI KACHILOMBO KA LOLONA KADZATILETSA?

(SHALL THE CORONAVIRUS STOP US?)
(Chichewa)

ndi Dr. R. L. Hymers, Jr.,
Mbusa Emeritus

Uthenga wolalikidwa pa chihema cha Baptist ku Los Angeles
kumadzulo kwa tsiku la Ambuye, Meyi 10,2020
A sermon preached at the Baptist Tabernacle of Los Angeles
Lord’s Day Afternoon, May 10, 2020


Chonde tsekulani pa Luka 21:8-11.

“Ndipo Iye anati, Yang’anirani musasocheretsedwe; pakuti ambiri adzadza mdzina langa, nadzanena, Ndine amene; ndipo Nthawi yayandikira; musawatsate pa mbuyo pao. Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi mapanduko, musaopsedwa; pakuti ziyenera izi ziambe kuchitika; koma mathedwe sakhala pomwepo. Pamenepo ananena nao, mtundu wa anthu udzaukira pa mtundu wina, ndipo ufumu pa ufumu wina: Ndipo kudzakhala zibvomezi zazikuru, ndi njala ndi mliri m’malo akuti akuti, ndipo kudzakhala zoopsya ndi zizindikiro zazikuru mwamba” (Luka 21:8-11).

Tsopano tsekurani ku Mateyu 24:4-8.

“Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, yang’anani, asasokeretse inu munthu. Pakuti ambiri adzafika mdzina langa, nadzanena, Ine ndine Kristu, nadzasokeretsa anthu ambiri. Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti zioneke; koma chitsiriziro sichinafike. Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zibvomezi m’malo akuti akuti. Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba” (Mateyu 24:4-8).

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

MA ULALIKI ATHU AKUPEZEKA MU MA FONI
ANU A M’MANJA TSOPANO.
PITANI KU WWW.SERMONSFORTHEWORLD.COM.
DAFANYANI BATANI LOBILIWIRA LOMWE LIRI NDI LIU LOTI “APP”
TSATIRANI MALANGIZO OTSATIRAWO.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

Tsopano liu lakuti “Mriri” ndi lofunikira, ndi loimoi (zochuluka) m’chi Giriki. Buku lotanthauzira Baibulo la Unger limati liu iri “limagwiritsidwa ntchito potanthauza…. Mliri.” Yesu analosera za Mriri wa EDZI. Liuri limalankhulanso za mliri wa kachilombo ka kolona. Taonani zimene Kristu ananena za miriri imeneyi, pa vesi 8, “Ndizo zonsezi zowawa zoyamba.” Liu la chi Giriki limatanthauza kuti “kuyamba kwa zowawa za kubereka” (MacArthur).

Ponena za masiku athu ano, J.N. Darby anati, “Kudzakhala mpingo wonyenga: Kudzakhala njala, miriri, zibvomezi.” Buku lotanthauzira mau la Vine’s limatanthauza mliri ngati “matenda onse akulu opatsirana, amene anenedwa kuti ndi ambiri pa Luka 21:11.”

Tsopano taganizirani m’mene anthu azidzachitira za “tchalitchi” utatha mliri wa Kovidi. Lipoti la pa onenewsnow.com (Epulo 24, 2020) unali ndi mutu woti, “Mmene anthu ‘adza chitire tchalitchi’ utatha mliri wa Kovidi?” Likuti anthu ambiri “azidzakhala pa mapemphero a pa lamya.” Limati “moyo wa kapembedzedwe utatha mliri umeneu udzakhala wosintha kwambiri kusiana ndi momwe unaliri kale.” “42% amati kaperekedwenso kadzasintha kusiyana ndi mliri usanabwere.” Nkhawa zagwa pakati pa atsogoleri a mipingo amene agwidwa ndi mantha pa zomwe atakumane nazo kutatha kutsekeredwaku.” “Anthu ambiri adzayamba kumapita ku matchalitchi akulu-akulu, izi zikuchititsa mantha atsogoleri ambiri mu Amereka yense.” Monga mwa chikhalidwe, a za sayansi, timakhulupirira kuti ‘pakachitika china chake nzachidziwikire – kuti abusa ambiri ndi wokhudzidwa.” “Chikhalidwe chaphunzitsa anthu kuvomereza zinthu zikamachitika… zomwe zikufunika."

Nditatha zaka 62 mu utumiki, Ndimakhulupirira kuti mpake kuti mantha amenewa akhalepo. Ndikuganiza kuti iri ndi gawo limodzi la uneneri wa m’masiku otsiriza umene unanenedwa mu II Atesalonika 2:3; “Munthu asakunyengezeni konseko; kuti silifika, koma chiyambe chifike chipatukocho” (awa ndi anthu wotaya chikhulupiriro). Dr. Merrill F. Unger anati “Mpatuko wa ung’ono udzapatsa mpata mpatuko weni-weni – kudzera pakusiya chikhulupiriro ukhulupirira mwa Kristu” (Buku lophunzitsa za ziwanda, tsamba 207). Kodi tingakhale a Kristu ene-eni ngati tikulephera kumvera vesi lofunikira limeneri la m’malemba?

“Osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga achitira ena; komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lirikuyandikira” (Ahebri 10:25).

Dr. W. A. Criswell pokambapo za vesi limeneri anati, “Wolemba buku la Ahebri analongosola kuti kusonkhana pamodzi koyenera kuwirikizidwa… pamene tsiku la Kristu likuyandikira…kufunikira kokhala pamodzi ngati mpingo ndi kwakukuru, ndi kufunikira kwa mkristu aliyese kukhala wokhulupirika ku mpingo wake monga woyera mtima achitira” (Baibulo lotanthauzira mau la Criswell; pa Ahebri 10:25).

Ndikukhulupirira kuti mau awa akanalibe ndi tanthauzo chingakhale masiku ano, pamene tikuona kubwera kwa Kristu kukuyandikira. Ma vangeri amakono sakumvera vesi limeneri. Lidzapitirira kukanidwa pamene tikudutsa moyandikira Chisautso Chachikuru. Satana akudziwa kuti ayenera kualetsa a Kristu kuti asamapite ku tchalitchi kuti afokere-fokere, kuti mapeto ake agonjere wokana Kristu.

Ndine wokhumudwa kuti atumiki monga David Jeremiah sa tsindika zolimbikitsa anthu kuti azipita ku tchalitchi. Dr. Jeremiah akulephera kukonzekeretsa mpingo ku Chinsautso Chachikulu.

Tsopano tsekurani Mateyu 24:6-8.

“Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma chitsiriziro sichinafike. Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhara njala ndi zibvomezi m’malo akutiakuti. Koma ndizo zonsezi zowawa zoamba.”

“Chitsiriziro sichinafike” (24:6).

“Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zibvomezi malo akutiakuti. Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba.

“Zonsezi zowawa zoyamba” (24:8).

Tsopano ndi kubvomerezana ndi Dr. J. Vernon McGee kuti 24:9 ndi chiyambi cha Chibvuto Chachikulu. Dr. A. W. Tozer anati,

“Ndi zoonadi masiku ndi oipa ndi masiku akuthadi, koma a Kristu eni-eni sakutengedwa osadziwa. Iwo anachenjezedwa za nthawi ngati iyi ndipo zakhala zikuyembekezeredwa.” (“Za Mulungu ndi Anthu,” tsamba 131)

Chonde Imani pamene ndi kuwerenga Mateyu 24:7-14.

“Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zibvomezi m’malo akuti akuti. Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba. Pamenepo adzakuperekani kumasautso, nadzakuphani, ndipo anthu amitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa. Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mzache. Ndipo aneneri onama ambiri adzauka, nadzasokeretsa anthu ambiri. Ndipo chifukwa cha kuchuruka kwa kusayeruzika, chikondi cha anthu aunyinji chidzazirala. Koma iye wakulimbika chirimbikire kufikira chimariziro, yemweyo adzapulumuka. Ndipo uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chitsafika chimaliziro.” (Mateyu 24:7-14)

Tsopano ndiyenera kukuuzana kuti ine sindikhulupirira mkwatulu wochitika Chisautso chachikuru chitachitika. Ndafika pokhulupirira kuti mkwaturo udzachitika mkwiyo wa Mulungu usanatsenuke. Ndiye mwachidule ndingoti, Ndimakhulupirira Mkwaturo wochitika Mkwiyo Usanafike (Zosindikizidwa ndi Thomas Nelson 1990). Chonde musaweruze buku la Rosenthal pokha-pokha mutaliwerenga kaye.

Marvin J. Rosenthal, ngati ine, anali wokhulupirira za mkwatulo wa mpingo usanafike mkwiyo. Bambo Rosenthal amaphunzitsa, mbuku lake, kuti mkwatulo sudzachitika pokha-pokha titafika pafupi ndi kutsanuridwa kwa mbale za chiweruzo za pa Chibvumbulutso 16. Kotero, ndimakhulupirira za mkwatulo, koma sindikhulupirira kuti udzachitika pokha-pokha patangotsala pang’ono kuti mbale za chiweruzo zitsenulidwe za pa Chibvumbulutso 16. Iyi si nkhambakamwa ayi, koma zeni-zeni zimene Baibulo limalosera. Mlaliki wa chi Tchaina John Sung amakhulipiriranso zimenezi. Komanso Dr. Timothy Lin, kholo ndi mbusa wanga kwa zaka 24. Dr. Christopher L. Cagan amakhulupiriranso zimenezi.

Kodi Rosenthal amanena zoona? Ndikuganiza kuti alipafupi kwambiri ndi kunena zoona. Musanamutsutse Rosenthal, muwerenge chaputala cha chikhumi ndi chisanu ndi chimodzi cha buku lake, lotchedwa, “Kudza ndi Chimaliziro.”

Cholinga changa cha ulariki uwu ndi kuonetsera kuti ngati ife “A Kristu” sitingapirire ku “mliri” wakudza masiku amene Chisautso Chachikulu chisanafike, adzaima bwanji nthawi ya Chinsautso Chachikulu cheni-chenicho?

“Pakuti pomwepo padzakhala masautso akulu , monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso. Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense: koma chifukwa cha osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.” (Mateyu 24:21, 22).

Mavesi amanewa akuonetsa “Chisautso Chachikulu.” Dr. J. Vernon McGee anati, “Tikuwerenga m’Buku la Chibvumbulutso kuti nthawi ya Chisautso Chachikuru gawo limodza la magawo atatu a anthu mdziko lapansi adzaonongeka…. Mthawi ngati imeneyi. Idalipo nthawi imene izi zimaoneka ngati kuti ndi zosingirira. Izi ziri chomwechi, tsopano pamene maiko ambiri ali ndi mabomba achipulura, amene akhoza kuononga mtundu wa dziko la pansi, sizikuoneka kuti ndi zosinjiriranso ayi” (Kumasulira Baibulo lonse; pa Mateyu 24:22).

Yesu anati, “Chifukwa chache m’mene mukadzaona chonyansa chakupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Danieli mneneri, chitaima m’malo oyera, (iye amene awerenga m’kalata azindikire:)” (Mateyu 24: 15). Dr. McGee anati, “Ambuye wathu mosakaika akutanthauza chithunzi-thunzi cha Wokana Kristu (Wonani Danieli 12:11) chimene chidzaikike (kuumbidwa) Mkachisi.”

“Pakuti pomwepo padzakhala chimsauko akuru, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso. Ndipo akadaleka kufupikitsa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense: koma chifukwa cha osankhikawo masiku awo adzafupikitsidwa” (Mateyu 24:21,22)

.

Dr. McGee anati, “Mulungu sadzalola kuti mtundu wa anthu udziphe. Ndichifukwa chake kanthawi kake kadzakhale kochepa” (McGee, zomwe zatanthauziridwa kale pa Mateyu 24:22). Komanso muone kuti a Kristu “osankhika” adzakhalabe alipobe, monga m’mene Marvin J. Rosenthal akunenera m’buku lake, Mkwiyo usanadze mkwatulo wa mpingo. (The Pre-Wrath Rapture of the Church)

Tsopano chonde tsekulani II Atesalonika 2:3.

“Munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika koma chiyambe chifike chipatuko” (II Atesalonika 2:3).

“Nabvumbulutsidwe munthu wosayeruzika” (katanthauzidwe ka makono)

.

M’masiku ano akusayeruzika alaliki ambiri, monga Kreighton ndi Waldrip, amayiwala chenezo limene linanenedwa pa I Timoteo 4:1, 2. Tsekulani I Timoteo 4:1, 2.

“Koma mzimu anena monenetsa, kuti m’masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziwanda; m’maonekedwe onyenga a iwo onena ma bodza, olochedwa mchikumbu mtima mwao monga ndi chitsulo cha moto.”

Poti anaiwala uneneri umenewu, “amanyengeka ndi mizimu yosocheretsa, ndi maphunziro a (ziwanda); amaonekedwe onyenga a iwo onena mabodza; olochedwa mchikumbu mtima mwao monga ndi chitsulo chamoto.” Nchifukwa anthu ngati amenewa amagawa mipingo. Chifukwa? Mosatsiwa “amasatira ziphunzitso za ziwanda,” Ichi ndiye chifukwa chake!

Nawa makhalidwe a “tsogoleri” amene amagawa mipingo. Izi zinalembedwa ndi Dr. Roy Branson, mbuku lake lotchedwa, Mpatuko wa Mpingo (Church Split) (tsamba 29-31).


1. Odzitamandira. Safuna kuvumereza kuti wina wake, chingakha mbusa, akhonza kukhala a nzeru kuposa iwo.

2. Odzikonda. Amafuna kuchita monga iwo afunira osalabadira kuti atabvutike ndani pakutero.

3. Sabvomereza kuti alakwitsa. Chizindikiro china cha kudzitamandira.

4. Amakhala ndi njala yofuna kudziwika ndi ulemerero.

5. Safuna kukhala pansi pa wina. Palabe chiphunzitso chomwe ndi chomveka bwino choposa ulamuriro omwe uli mwa mbusa ndi kufunikira kowatsatira. Amanena kuti iwo amamvera Kristu yekha basi. Amati mbusa amalamulira mwa nkhanza.

6. Ndi onyenga. Amakhala ngati akukhudzidwa ndi zochitika mu mpingo. Pomwe chilinga ndi kufuna kukwaniritsa zofuna zao.

7. Amalankhula mwa chipha maso. “Ndimawakonda abusa, koma…” Kenaka ndikumawa nene abusa.

8. Amasinjirira zimene abusa anena, kuti zioneke ngati zolakwika.

9. Amazitenga ngati zolakwika zirizonse zimene a busa anena.

10. Sabvomera chiphunzitso chilichonse. Ama “chotsera” zimene Baibulo likunena.

11. Amatakasa anthu ena kuti azidadaula motsutsana ndi mbusa. Amasonkhanitsa timagulu kuti aukire ndi kugawanitsa mpingo.


Makhalidwe onsewa anaonekera pa mpatuko wa Kreighton ndi Waldrip.

Sindikanatha kulalikira choima. Izi zinamulimbitsa mtima Kreighton. Ndi munthu wamanyazi, anandipsera mtima chifukwa sindinampatse mpata wolalikira. Amakonda kunena kuti izi sizinamukhumudwitse. Mpaka anamulembera Dr. Cagan kuti samufuna kulalikira “kuti adzikondweretse.” Sindinalore kuti alalikire chifukwa analibe mphatso za kutero. Ankanena kuti izi anagwirizananazo. Koma chonsecho amanama ponena zimenezi. Monga achinamata ambiri a msinkhu wake, sanali ndi ubale wabwino ndi a bambo ake. Kotero, nthawi imene ndinadwala, anandiukira motsutsani ndi bamboo ake. Koma amachita izi mwa chisinsi. M’malo moti alankhule nane pamaso, anayamba kukhala ndi timaupo tachisinsi ndi mlaliki wina, dzinalake John Waldrip. Kukumana kwao ndi Waldrip ine sindimakudziwa. Waldrip anali wogwirizana naye pa maupo “a chisinsi” amenewa.

Kenaka Kreighton anayamba kudziwitsa anthu ena zoti sakugwirizana ndi ine. Chikhalirecho sanandiuzepo kuti sagwirizana nane. Ndimadzazindikira za kuukira kwache mochedwa. Anali atatenga kale ma gawo atatu achinyamata athu ndi kuyambanao “mpingo” wake. Anatisiira anthu 35 okha.

Koma nthawi ya mpatuko, ndinali ndi zaka makumi asanu ndi atatu, komanso ndimadwala. Poti izi ndinali nditadutsamo kale, ndinadziwa kuti Mulungu apanso andidutsitsamo. Ndi chifukwa chache sindinadenazo nkhawa.

M’modzi wa ma dikoni anfuna kundimenya ndi zibakera. Dikoni wina anayika zithunzi zolaula ndi mkazi patsamba la intaneti lake. Mtsogoleri wina anti ndimadana ndi anthu akuda mtchalitchi lathu. Mtsogoleri wina anati ndinasiya ulaliki wa m’misewu chifukwa choletsedwa ndi anthu o chita za dama, amene samathandizidwa.

Pamene zonsezi zimachitika ndinatura pansi udindo wanga ngati mbusa kenaka Dr. Cagan anasankhidwa kukhala mbusa. Mwana wake weni-weni amene ndi namulera kuti adzakhale mbusa watsatira, anachoka, chingakhale ndimamutenga ngati mzanga weni-weni.

Tsopano kwagwa kachilombo ka kolona! Tachoka mchalitchi tayamba kukumana m’manyumba, ine, ngati mbusa Emeritus, kulalikira la Mulungu liri lonse m’makanema a m’manyumba.

Tagula tchalitchi latsopano kunja kwa mzinda wa Los Angeles. Ndiamba kuyang’anira wachinyamata wa chi Tchaina kuti adzalowe m’malo mwanga ndikadzafikka polephera kulalikira.

Ndakhala ndikutsutsidwa chifukwa cholalikira za ziwanda ndi mpatuko wa ma tchalitchi, koma ndiri ndi a lariki amene amawerenga ma uthenga anga mzirankhulo 43 ochokera “m’maiko okwera kumene” chingakhalenso ku Amereka, ndimamva kuti maulariki amenewa adzathandizanso iwo. Ndikumva kuti Mulungu akufuna kuti ndilankhule za chiphunzitso chimenechi pamene tikuyamba tchalitchi la tsopano la chi Tchaina.

Ine ndiri wosangalala kuti Mulungu anandiitana kukhala wa mishoni kwa anthu a chi Tchaina ndikari ndi zaka 19. Patha zaka 60 ndikanachitabe zimene Mulungu anandiitanira zaka zambiri zapitazo. Ndikadali wa mishoni mchisomo cha Mulungu. Padafika poti ndi zisiye zoti ndikhale chimene ndiri! Nayi ndakatulo imene John Wesley analemba,

Kudzikuza pang’ono, kugwedezeka pang’ono,
Kuwala mtsiku la dzinja
Kodi onse o dziwika ndi a mphamvu alinako
Pakati pa kufukatiridwa ndi manda!

Ndabzyala mipingo ya mbiri “kuyambira popanda kanthu” mu zaka 62 zanga zolalikira. Ndikukhulupirira kuti Mulungu adzamuthandiza Dr. Cagan ndi ine kuti tiyambirenso.

Chingakhale izi sizidzakhala za pafupi. Mwa chisomo cha Mulungu, tiyamba mpingo pakati pa anthu otsutsana ndi zambiri za m’masiku otsiriza. Zisoweka munthu akhale wolimba mtima ndi wa khama. Uyenera kukhala wa khama kwambiri kotero kuti kachilombo ka kolona ndi kakang’ono koti sikangakuletseni kukhala chimene muyenera kukhala mwa Yesu Kristu, monga Dr. Timothy Lin ndi Mbusa Richard Wurmbrand. Kumbukirani, “tiyenea kulowa mu m’ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.” (Machitidwe 14:22).

Ndikukanikizidwira kumwamba, tsiku ndi tsiku ndikupita mulingo watsoppano;
    Pakupitirirabe m’mapemphero anga onka m’mwamba, “Ambuye. Bzyalani mapazi anga pa malo olimba.”
Ambuye, nditukulireni m’mwamba kuti ndiime njii, Mwachikhulupiriro, pa gome la m’mwamba.
    Ndege ya m’mwamba yoposa imene ndaipeza; Ambuye, bzyalani mapazi anga pa nthaka yolimba.

Mtima wanga sukufuna kukhala kuno Komwe makayiko akuchuluka ndi mantha atizika.
    Ngakhale ena angakhalebe msinga zimenezi, Pemphero anga, cholinga changa, ndi chapamwamba.
Ambuye, ndikwezeni ndi kundirimbitsa kuti ndiime njii, Mwachikhulupiriro, pa gome la m’mwamba.
     Ndege ya m’mwamba yoposa imene ndaipeza; Ambue, bzyalani mapazi anga pa nthaka yolimba.

Ndikufuna kukhala moyo wa pa mwamba, Ngakhale Satana akuponya mibvi yake pa ine;
    Pakuti chikhulupiriro chandipatsa chimwemwe, Nyimbo ya oyera mtima ya m’mwamba.
Ambuye, ndikwezeni ndi kundirimbitsa kuti ndiime njii, Mwachikhulupiriro, pa gome la m’mwamba.
     Ndege ya m’mwamba yoposa imene ndaipeza; Ambue, bzyalani mapazi anga pa nthaka yolimba.

Ndikutha kuona m’mwamba-mwamba Ndikuoona ulemerero;
    Koma ndipempherabe mpaka ndipeze m’mwamba, “Ambuye, nditsogolereni ku malo a m’mwamba.”
Ambuye, ndikwezeni ndi kundirimbitsa kuti ndiime njii, Mwachikhulupiriro, pa gome la m’mwamba.
    Ndege ya m’mwamba yoposa imene ndaipeza; Ambue, bzyalani mapazi anga pa nthaka yolimba.
  (“Malo a M’mwamba” ndi Johnson Oatman, Jr., 1856-1926).


MUKAFUNA KULEMBERA DR.HYMERS MUYENERA KUTCHULA DZIKO LIMENE MUKULEMERA APO AYI SADZATHA KUYANKHA KALATA YANU. Ngati maulaliki awa akudalitsani tumizani e-mail kwa Dr. Hymers ndikumuuza, koma nthawi zonse tchulani dziko limene mukulembera. E-mail ya Dr. Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net dafanyani apa. Mukhoza kumulembera Dr. Hymers mchilankhulo chirichonse, koma muyesetse Mchigerezi ngati mungathe. Ngati mukufuna kulembera Dr. Hymers pa positi, keyara yake ndi P.O. Box 15308, Los Angels, CA 9001. Mukhoza kuimba foni pa (818) 352-0452.

(MAPETO A ULALIKI)
Mukhoza kuwerenga ma ulaliki a Dr. Hymers sabata iriyose pa intaneti iyi
www.sermonsfortheworld.com,
dafanyani “Maulaliki mchichewa.”

Maulaliki awa si oletsedwa. Mukhoza kuagwiritsa ntchito kopanda kufuna chilorezo kwa
Dr. Hymers. Komabe, maulaliki a mkanema ya tchalitchi lathu ngofunika kuagwiritsa
ntchito potenga chilorezo