Print Sermon

Cholinga cha tsamba ili ndi kupereka ma ulaliki a ulere olembedwa komanso a mkanema kwa a busa mdziko lonse la pansi makamaka maiko okwera kumene, komwe kuli ma sukulu a Baibulo ochepa kapena kulibiretu.

Maulaliki awa olembedwa komanso a m’ma video akupezeka pafupifupi m’ma kompyuta 1,500,000 m’maiko 221chaka chilichonse pa www.sermonsfortheworld.com. Anthu zikwi-zikwi amaonera kanema wa pa YouTube, koma kenaka amasiya YouTube ndikubwera ku website yathu. You Tube imawalondolera anthu ku website yathu. Maulaliki olembedwawa akupezeka mzilankhulo 46 mu makomputa 120,000 mwezi uli wonse. Maulalikiwa alibe chiletso, kotero alaliki akhoza kuagwiritsa ntchito mosafuna chilolezo. Chonde sindikizani apa kuti mudziwe m’mene mungaperekere thandizo la mwezi ndi mwezi lomwe lingathandize kwakukulu pofalitsa uthenga wa bwino kudziko lonse la pansi.

Mukafuna kulembera Dr. Hymers nthawi zonse muuzeni dziko limene mukukhala, apo ayi sangakuyankheni. E-mail ya Dr.Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net.




ZINTHU ZIRI NKUDZA –
UTHENGA WA CHAKA CHATSOPANO

THINGS TO COME – A NEW YEAR’S SERMON
(Chichewa)

ndi Dr. R. L. Hymers, Jr.

Uthenga wolalikidwa pa Chihema cha pa Baptist ku Los Angeles
Usiku wa tsiku la a Mbuye, Januwale 5, 2020
A sermon preached at the Baptist Tabernacle of Los Angeles
Lord’s Day Evening, January 5, 2020

“Zinthu ziri nkudza; zonse ndi zanu; koma inu ndi a Kristu; ndi Kristu ndi wa Mulungu” (I Akorinto 3:22-23).


“Zinthu ziri nkudza.” Mau awa ndi oopsa kwa iwo amene samudziwa Khristu! “Zinthu ziri nkudza.” Anthu otizungulira nthawi ilinkudza amayiona mwa mantha ndi ku nthunthumira! Amakhala opanda chiyembekezo.

Ndikuchuluka kwa makanema, ndi ma intaneti, ngozi sosiyana-siyana padziko lonse lapansi, nkhondo, uchigawenga, infa tikuziona m’makomo mwathumu tsiku ndi tsiku. Tikuona kuphana. Tikuona ma bomba. Tikuona mchitedwe wa uchigawenga. Azimayi kugwiriridwa, kusowa chakudya ndi kunzunzika zonsezi zikuchitika maso athu akuona palibe mbadwo womwe unaziona ngati zimene tikuzionazi mdziko lapansizi. Ife tikuona zimene iwo amangowerenga. Tsiku lirironse tikuon ngozi zosiyana-siyana mumawailesi, zomwe zikudzetsa nkhawa ndi mantha. Ndikukhulupirira kuti Khristu adadziwiratu za masiku ano amene ndi otsiriza. Akunena kuti anthu “adzapsinjika” ndi “kufooka” Luka 21:25 ndi,

“Anthu akukomoka ndi mantha, ndikuyembekezera zinthu ziri nkudza pa dziko lapansi…” (Luka 21:26).

Anthu olanda ndege mwa mbanda. Kuphulitsa zinyumba. Mabomba a chipulula akupezeka m’manja mwa anthu osayenera amene akhonza ku agwiritsa ntchito mosayenera. Anthu odziwika pa za sayansi, ndi atsogoleri a ndale, akutichenjeza za kutentha kodetsa nkhawa kumene kuli patsogolopa. Musaseke! Inde, mau akuti “zinthu zirinkudza” ndi zochititsa mantha kwa anthu ambiri. Monga Khristu analosera, “ mitima ya anthu (iri) komoka chifukwa cha mantha polingalira zirinkudzazo padziko lapansi

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

MA ULALIKI ATHU AKUPEZEKA MU MA FONI
ANU A M’MANJA TSOPANO.
PITANI KU WWW.SERMONSFORTHEWORLD.COM.
DAFANYANI BATANI LOBILIWIRA LOMWE LIRI NDI LIU LOTI “APP”
TSATIRANI MALANGIZO OTSATIRAWO.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

Pamwamba pa makanema oopsa onsewa, ife kuno ku Washington tikuoona zoopsa kwambiri tisanazionepo chikhalire! Andale ambiri akhala ngati azungulira mitu! Makamaka ma Demokalatsi!

Poonjezera pa zonsezi mawanja athu avulala, kutha kwa mawanja akungotha chisawawa, ana athu abalalika, ndikutsatira njira zosayenera, gawo lalikulu mu mbadwo uno lafera mchikuta – pafupi-fupi 60 milioni amene aphedwa asanabadwe! Ana Anayi mwa asanu ndi awiri ali wonse a chi Amerika akuda achita kupulumutsidwa ku lamulo “lololeza kutaya mimba. Ndiye kuti, mkwiyo wa anthu a chiwembu walowerera mpaka kumakatokosola tiana tosabadwa m’mimba za azimayi ambiri. Palibe malo otetezedwa! Kulibe kubisala. Wolemba ndakatulo wotchuka dzina lake William Butler Yeats anati mu ndakatulo yake, “Kubweranso ka Chiwiri”:

Zinthu za sokonokera
Ulamuliro wa nkhanza wamasulidwa kupita kudziko la pansi.
Funde lofuna mwazi lamasulidwa, ndipo penapaliponse
Kolona wa mwambo wa osalakwa wakhazikitsitsa
Pakuchita zonsezi osamva ku tsutsika, pomwe choyipa kwambiri
Zikuchitika moposa muyeso……

Atangolandila ulemu wapadera ku Washington, Billy Graham anati, “ndife anthu amene tikudikira kudziononga” (Los Angeles Times, Meyi 3, 1996, p.A-10). Anthu akutha kumva kuti palibe malo amene ndi wotetezeka! Akutha kumva kuti kulibe kothawira kumchitidwe woopsa womwe tikuuona tsiku ndi tsiku m’makanema ndi m’ma intaneti. Nzosadabwitsa pa kuti pakubwera mau akuti “zinthu zirikudza” kudzadza mitima yawo ndi mantha ndi kunjenjemera!

Koma mutu wa chiphunzitsochi siunaperekedwe kwa iwo akutayika. Unalembedwera kwa iwo amene ndi opulumutsidwa. Pa vesi 21, mtumwi Paulo anati, “zonse ndi zanu.” Pa vesi 22 walemba mndandanda wa zinthu zimene ndi za a Khristu eni-eni. Pa mapeto pa mndandanda umenewu, anati, zinthu zilinkudza; zonse ndi zanu” (1 Akorinto 3:22)

“Zinthu zirinkudza; zones ndi zanu” (I Akorinto 3:22).

I. Choyamba, chisangalalo cha a Khristu ndi chanu!

Yesu anati,

“Ndidzakhazika mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzaulaka iwo” (Mateyu 16:18).

Kalonga wa Alaliki C. H. Spurgeone anati,

Tikamaona…m’mene zikuyendela ndale, tikuchitanazo mantha. Anthu akusonkhana apa ndi apo; tikudandaulira mpingo, pamene tikuona kuti chitetezo chake chiri pa chiopysezo, pamene tikuona kuti maufumu akugwa. Koma palibe kusintha kwina kuli konse kumene kungathe kuononga mpingo. Mu mbiri iliyonse ya mpungwepungwe, kapena zoopyseza zimene dziko lapansi lakumana nazozi, mpingo uyenera kukhalabe ndi chigonjetso, pamene chuma chikusowa m’maiko ake a Khristu (Mpingo) umasonkhanitsa chuma. (C. H. Spurgeon, “Zitnthu zilinkudza! Cholowa cha oyera mtima,” ulariki wa Spurgeon pamwamba Voluyumu 63, Tsiku loyamba losindikiza, 2009, tsamba. 341-342) Ulaliki wa Spurgeon

Ulamuliro wa angerezi unagwa, koma Chikristu chinapitirira kukhala cha thanzi m’maiko amene munali ulamuliro wao. Mafunde a chitsitsimutso akukokolola miyanda-miyanda kuwalowetsa m’mipingo! Pamene “maulamuliro” a Amerika ali pa mpembenu wakugwa, miyanda-miyanda ya anthu mu maiko okwera kumene ikusesedwera kwa Khristu kudzera mu mphamvu yodabwitsa ya Mulungu! Ndipo pamene ndikulankhula madzulo ano, ulosi wa Yesu ukuyenda mowirikiza kukwaniritsidwa kwache.

“Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse la pansi, ukhale umboni kwa anthu a mitundu yonse…..” (Mateyu 24:14).

“Akolona ndi mafumu zidzatha!” imbani nyimbo iyi!

Maufumu ndi maulamuliro zidzatha, amadzuka ndi kutha,
   Koma mpingo wa Yesu udzakhalabe;
Makomo a dziko la akufa sadzaulaka ‘mpingo udzakhalabe;
   Tiri ndi lonjezano la Khristu; limene silidzalephera.
Chitsogolo, asirikali a Chikhristu, kuguba ngati ku nkhondo,
   Ndi mtanda wa Yesu patsogolo!
(“Chitsogolo, Asirikali a Chikristu,” Wolemba Sabine Baring-Gould, 1834-1924).

Mpingo umene panopa ukumenya nkhondo, posachedwapa ugonjetsa! Posachedwapa udzafuula,

“Ufumu wa dziko lapansi Wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wache; ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi” (Chibvumbulutso 11:15).

“Zinthu ziri nkudza zonse ndi zanu” (I Akorinto 3:22).

II. Chachiwiri, Ufumu wa Kristu ulinkudza ndi wanu!

Yesu anati,

“Odala ali akufatsa: chifukwa adzalandira dziko lapansi.” (Mateyu 5:5).

Yesu anatinso:

“Musaope, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu” (Luka 12:32).

A Kristu akunyozedwa ndi kupeputsidwa kuno ku Amereka komanso dziko lonse la pansi. A Kristu akunzunzika, kumangidwa, ndipo kawiri-kawiri kuphedwa, chifukwa cha chikhulupiriro chao m’Maiko Okwera kumene. Anthu osakhulupirira ndi opandapake a m’masiku athu ano amaganiza kuti tidzalephera. Koma akunama kotheratu! Baibulo limati,

“Ngati tipirira tidzachitanso ufumu ndi iye” (II Timoteo 2:12).

pamene Ufumu Wake ukulamulira pa dziko lapansi! Ife tidzaimba kwa Kristu,

“mwaphedwa , mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu amafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse; ndipo mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu, ndipo achita ufumu padziko” (Chibvumbulutso 5:9-10).

Imbani nyimbo nambala 2, pa pepala lanu la nyimbo, “ Usiku wa mdima bii.” Imbani!

Usiku wa mdima bii, tchimo linalimbana nane;
   Timanyamula mtolo wolemetsa;
Koma tsopano tikuona zizindikiro za kudza kwache
   Mitima yathu idzawala
Chikho cha chimwemwe chisefuka
   Akumbweranso, Akubweranso
Yesu yemwe anakanidwa ndi anthu.
   Akubweranso, Akubweranso;
Ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu, akubweranso.
   (“Akubweanso wolemba” woyimba Mabel Johnston Camp, 1871-1937)

Imbaninso!

Usiku wa mdima bii, tchimo linalimbana nane;
   Timanyamula mtolo wolemetsa;
Koma tsopano tikuona zizindikiro za kudza kwache
   Mitima yathu idzawala
Chikho cha chimwemwe chisefuka
   Akumbweranso, Akubweranso
Yesu yemwe anakanidwa ndi anthu.
   Akubweranso, Akubweranso;
Ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu, akubweranso.

Ngati ndinu wopulumutsidwa, kubwranso kwa Ufumu wa Kristu ndi kwanu!

“Zinthu zirinkudza; zonse ndi zanu” (I Akorinto 3:22).

III. Chachitatu, miyamba yatsopano ndi dziko latsopano ndi zanu!

Dziko lakale iri lidzapita! Pamene Kristu adzalamulire dziko la pansi zaka chikwi, Satana adzamasulidwa kuchoka mundende natsogolera oukira adziko lapansi mutsutsana ndi Iye. (Chibvumbulutso 20:7-9). Pamenepo moto wa Mulungu udzagwa kuchoka Kumwamba

“… m’mene miyamba idzapita ndi chibumo chachikuru, ndi zamwamba zidakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito ziri momwemo zidzatenthedwa….miyamba ndi potentha moto idzakanganuka, ndi zamwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukuklu” (II Petro 3:10, 12).

Koma osadera nkhawa, pakuti mtumwi Yohane anati m’masomphenya ake,

“Ndinaona m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano: pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka ndipo kulibenso Nyanja. Ndipo ine Yohane ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika kumwamba kwa Mulungu” (Chibvumbulutso 21:1-2).

Pamene Mulungu akulenga Kumwamba ndi Dziko latsopano, mudzakhala muli momwemo mu Yerusalemu watsopano – ngati ndinudi m’Kristu weni-weni! Inde mudzakhala momwemo kwanthawi za nthawi mu mpaladizo wa Mulungu, mdziko latsopano, ndi mu Yerusalemu wa Tsopano!

Zinthu zirinkudza; zonse ndi zanu” (I Akorinto 3:22).

“Zinthu zirinkudza; zonse ndi zanu” (I Akorinto 3:22).

Koma nditseke poonanso ndime, yomwe tinawerenga poyamba paja,

“Zirinkudza; zonse ndi zanu; Ndi a Kristu, ndi Kristu ndiye wa Mulungu” I Akorinto 3:22-23)

.

Taona zinthu zabwino “zirinkudza” kwa iwo amene ndi a Kristu. Koma kodi ndinu m’modzi wa iwo? Kodi mukhonza kunena motsimikiza kuti “ndinu wa Kristu”? Ngati simunganene, ndiye kuti palibe lonjezano lanenedwali ndi lanu! Spurgeon anati, “Ngati mulibe chikhulupiriro. Ndiye kuti mulibe tsogolo labwino koma mantha…. Ngati sindinu a Kristu, palibe choti tikusangalalireni” (ibid.p. 347).

Chidzakupinduliraninji ngati mutakhala ndi ndalama zambiri, ndikumasangala m’moyo uno, mapeto ake, ndikutaya zonse ndi infa ndikukupezani mulibe Kristu? “Zinthu ziri nkudza” zidzakhala zoopsa kwa inu ngati simunakhale oona kwa Kristu. Ndikukudandaulirani kuti muganizirepo bwino za chipulumutso cha moyo wanu. Ndikukupemphani kuti muganizire onetseredwani ndi muone za tchimo lanu ndi mtima wanu wochimwa. Ndikupemphani kuti muganizire zakuti tchimo lanu, ndi zofuna zanu zidzakuchotsani chiyembekezo chanu, ndikukuponyani ku Nyanja ya moto. Ndikupemphera kuti muchokeko ku mdima wa dziko lochimwa iri. Ndikupemphera kuti mudze msanga kwa Yesu Kristu. Ndipemphera kuti mumuwone mwa chikhulupiriro ndikuonetseredwa m’mene anachotsera tchimo lanu mwa mwazi wake wa muyaya! Idzani kwa Iye. Dzigwetsereni kwa amene ananzunzika, koma wolandira ulemu, mwana wa Mulungu. Adzakupulumutsani! Adzakupulumutsani! Mukatero ndiye chisangalalo ndi chiyembekezo “Zinthu zinkudza” zomwe zanenedwa, zidzakhala zanu!

Ngati mukufuna kulankhula ndi ambusa za m’mene mungakhalire Mkristu wene-weni, chonde imirirani ndi kupita kumbuyo kwa chipinda chino tsopano kuti akulankhuleni zokhudzana ndi tchimo, ndi chipulumutso mwa Kristu Yesu.

Tsopano mau owonjezera kwa inu. Kodi sikofunikira kuti ife amene tamva uthenga wabwino wotere wa Kristu tiyenera kuufalitsa kufikira kutari? Kodi sikwabwino kuti tiyambe mchaka cha tsopanochi pakudziperekanso ku kumvera mau a Kristu kwa ife omwe ali pa Mateyu 28:19-20)?

Tiyeni tinene kuti, ndi mitima yathu yonse, tidzamvera Yesu pakularikira kwa munthu ndi munthu, ndi pomakhala nawo m’misonkhano ya chitsitsimutso ya mpingo wathu; ndi pofuna kuitana abwenzi ndi mabanja kuti adzamvere Uthenga wa bwino wa chipulumutso mwa Yesu. Mulungu atithandize kuti timvere Kristu po lalirikira ponse pamene patapezeke mwayi mchaka cha 2020! Chonde Imani ndi kuyimba nyimbo yomalizira pa tsamba lanu la nyimbo.

Tipatseni mau achiyembekezo pa ola lino, Liu lokoma, liwu la mphamvu,
Kufuula kwa ku nkhondo, kupuma kwa chigonjetso kapena infa kwa mveka.
Liu lodzutsa mpingo kutulo, Kuti umvere pempho lalikulu la Ambuye.
Taitanidwa, Miyamba inu, dzukani, Liula chiyembekezo ndi, lalikirani!

Mwa chimwemwe uthenga wamveka, Padziko lonse la pansi, mdzina la Yesu;
Liu lamveka mlengalenga: Lalikira! Larikira!
Kwa mbadwo wolefuka, mtundu wakugwa, adziwitse mphatso ya Uthenga wa chisomo;
Dziko limene liri mu mdima tsopano, Lalikira! Lalikira!
   (“Larikira! Lalikira!” ndi Dr. Oswald J. Smith, 1889-1986;
      yosinthidwa ndi Dr. Hymers; molingana ndi kamvekedwa ka “Ndikuti Zingachitike?”
ndi Charles Wesley, 1707-1788).

Ameni!


MUKAFUNA KULEMBERA DR.HYMERS MUYENERA KUTCHULA DZIKO LIMENE MUKULEMERA APO AYI SADZATHA KUYANKHA KALATA YANU. Ngati maulaliki awa akudalitsani tumizani e-mail kwa Dr. Hymers ndikumuuza, koma nthawi zonse tchulani dziko limene mukulembera. E-mail ya Dr. Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net dafanyani apa. Mukhoza kumulembera Dr. Hymers mchilankhulo chirichonse, koma muyesetse Mchigerezi ngati mungathe. Ngati mukufuna kulembera Dr. Hymers pa positi, keyara yake ndi P.O. Box 15308, Los Angels, CA 9001. Mukhoza kuimba foni pa (818) 352-0452.

(MAPETO A ULALIKI)
Mukhoza kuwerenga ma ulaliki a Dr. Hymers sabata iriyose pa intaneti iyi
www.sermonsfortheworld.com,
dafanyani “Maulaliki mchichewa.”

Maulaliki awa si oletsedwa. Mukhoza kuagwiritsa ntchito kopanda kufuna chilorezo kwa
Dr. Hymers. Komabe, maulaliki a mkanema ya tchalitchi lathu ngofunika kuagwiritsa
ntchito potenga chilorezo


KALEMBEDWE KA

ZINTHU ZIRI NKUDZA –
UTHENGA WA CHAKA CHATSOPANO

THINGS TO COME – A NEW YEAR’S SERMON

ndi Dr. R.L.Hymers, Jr.

“Ziri nkudza; zonse ndi zanu; Inu ndinu a Kristu; ndi Kristu ndiye wa Mulungu” (I Akorinto 3:22-23).

(Luka 21:25,26; I Akorinto 3:21,22).

I.   Choyamba, Chisangalalo cha oyera mtima ndi chanu! Mateyu 16:18;
Mateyu 24:14; Chibvumbulutso 11:15.

II.  Chachiwiri, Ufumu wa Kristu ndi wanu! Mateyu 5:5;
Luka 12:32; II Timoteo 2:12; Chibvumbulutso 5:9-10.

III. Chachitatu, kumwamba kwatsopano ndi dziko latsopano ndi zanu!
Chibvumbulutso 20:7-9; II Petro Chibvumbulutso 21:1-2;
Mateyu 28:19-20.